Za nyama zodyeka ndi zosadyeka ndi zakufa zodetsa munthu
1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati nao,
2 Nenani ndi ana a Israele, ndi kuti, Izi ndi zamoyo zimene muyenera kumadya mwa nyama zonse zili padziko lapansi.
3 Nyama iliyonse yogawanika chiboda, nikhala yogawanikadi chiboda, ndi yobzikula, imeneyo muyenera kudya.
4 Koma izi zokha simuyenera kuzidya mwa zobzikulazo, kapena zogawanika chiboda;ngamira, ingakhale ibzikula, koma yosagawanika chiboda, muziiyesa yodetsedwa.
5 Ndi mbira, ingakhale ibzikula koma yosagawanika chiboda, muiyese yodetsedwa.
6 Ndi kalulu, popeza abzikula koma wosagawanika chiboda, mumuyese wodetsedwa.
7 Ndi nkhumba, popeza igawanika chiboda, nikhala yogawanikadi chiboda, koma yosabzikula, muiyese yodetsedwa.
8 Nyama yake musamaidya, mitembo yake musamaikhudza; muziyese zodetsedwa.
9 Mwa zonse zili m’madzi muyenera kumadya izi: zilizonse zili nazo zipsepse ndi mamba m’madzi, m’nyanja, ndi m’mitsinje, zimenezo muyenera kumadya.
10 Koma zilizonse zilibe zipsepse ndi mamba m’nyanja, ndi m’mitsinje, mwa zonse zokwawa za m’madzi, ndi mwa zamoyo zonse zili m’madzi, muziziyesa zonyansa;
11 inde muziyese zonyansa; musamadya nyama zao; mitembo yao zikunyansireni.
12 Zilizonse zopanda zipsepse kapena mamba m’madzimo muziyese zonyansa.
13 Ndipo mwa mbalame muziziyesa zonyansa izi; simuyenera kuzidya, zonyansa ndi izi: mphungu, ndi nkhwazi, ndi chikambi;
14 ndi muimba, ndi mphamba mwa mtundu wake;
15 khwangwala mwa mtundu wake;
16 ndi nthiwatiwa, ndi chipudo, ndi kakowa, ndi kabawi mwa mtundu wake;
17 ndi nkhutukutu ndi nswankhono ndi manchichi;
18 tsekwe, vuwo, ndi dembo;
19 indwa, ndi chimeza monga mwa mtundu wake, ndi sadzu, ndi mleme.
20 Zokwawa zonse zakuuluka zokhala ndi miyendo inai, muziyesa izi zonyansa.
21 Koma muyenera kudya izi mwa zokwawa zonse zakuuluka, zokhala ndi miyendo inai, zokhala ndi miyendo pa mapazi ao, ya kutumpha nayo pansi; mwa zimenezi muyenera kudya izi:
22 dzombe mwa mtundu wake, ndi chirimamine mwa mitundu yake, ndi njenjete mwa mtundu wake ndi tsokonombwe mwa mitundu yake.
23 Koma zokwawa zonse zakuuluka, za miyendo inai, muziyese zonyansa.
24 Ndipo izi zikudetsani: aliyense akhudza mtembo wake adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo;
25 ndipo aliyense akanyamulako nyama ya mtembo wake azitsuka zovala zake, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
26 Nyama iliyonse yakugawanika chiboda, koma yosagawanikitsa, ndi yosabzikula, muiyese yodetsa; aliyense wakuikhudza adzakhala wodetsedwa.
27 Ndipo iliyonse iyenda yopanda chiboda mwa zamoyo zonse za miyendo inai, muiyese yodetsedwa; aliyense wokhudza mtembo wake adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
28 Ndipo iye amene akanyamula mtembo wake atsuke zovala zake, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo; muziyese izi zodetsa.
29 Ndipo izi ndi zimene muziziyesa zodetsedwa mwa zinthu zokwawa zakukwawa pansi; likongwe, ndi mbewa, ndi msambulu mwa mtundu wake;
30 ndi gondwa, ndi mng’azi, ndi buluzi, ndi dududu, ndi birimankhwe.
31 Izi ndi zimene muziyese zodetsa, mwa zonse zakukwawa; aliyense azikhudza zitafa, adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
32 Ndipo chilichonse chakufa cha izi chikagwera kanthu, kanthuka kadzakhala kodetsedwa; ngakhale chipangizo chamtengo, kapena chovala, kapena chikopa kapena thumba, chipangizo chilichonse chimene agwira nacho ntchito, achiviike m’madzi, ndipo chidzakhala chodetsedwa kufikira madzulo; pamenepo chidzakhala choyera.
33 Ndipo chilichonse cha izi chikagwa m’chotengera chilichonse chadothi, chinthu chokhala m’mwemo chidetsedwa, ndi chotengeracho muchiswe.
34 Chakudya chilichonse chokhala m’mwemo, chokonzeka ndi madzi, chidzakhala chodetsedwa; ndi chakumwa chilichonse m’chotengera chotere chidzakhala chodetsedwa.
35 Ndipo kanthu ka mtembo wake kakagwa pa zinthu zilizonse zidzakhala zodetsedwa; ngakhale mchembo kapena mphika wovundikika, aziswe; zodetsa izi, muziyese zodetsedwa.
36 Koma kasupe kapena chitsime muli madzi, zidzakhala zoyera; koma iye amene akhudza mitembo yao adzadetsedwa.
37 Ndipo kanthu ka mtembo wake kakagwa pa mbeu yofesa, ikati ifesedwe, idzakhala yoyera.
38 Koma akathira madzi pa mbeuyi, ndi kanthu ka mtembo wake kakagwapo, muiyese yodetsedwa.
39 Ndipo ikafa nyama yakudya, iye amene akhudza mtembo wake adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
40 Ndipo iye wakudya kanthu ka mtembo wake azitsuka zovala zake, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo; iyenso wakunyamula mtembo wake atsuke zovala zake, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
41 Ndipo zokwawa zonse zakukwawa padziko lapansi zikhale zonyansa; musamazidya.
42 Zonse zoyenda chafufumimba, ndi zonse za miyendo inai, kapena zonse zokhala nayo miyendo yambiri ndi zokwawa zonse zakukwawa pansi, musamazidya; popeza ndizo zonyansa.
43 Musamadzinyansitsa ndi chokwawa chilichonse chakukwawa, musamadzidetsa nazo, kuti mukadziipse nazo.
44 Pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu; potero dzipatuleni, ndipo muzikhala oyera; pakuti Ine ndine woyera; ndipo musamadziipsa ndi chokwawa chilichonse chakukwawa pansi.
45 Pakuti Ine ndine Yehova amene ndinakukwezani kukutulutsani m’dziko la Ejipito, ndikhale Mulungu wanu; chifukwa chake mukhale oyera, popeza Ine ndine woyera.
46 Ichi ndi chilamulo cha nyama, ndi cha mbalame, ndi cha zamoyo zonse zakuyenda m’madzi, ndi cha zamoyo zonse zakukwawa pansi;
47 kusiyanitsa pakati zodetsa ndi zoyera, ndi pakati pa zamoyo zakudya ndi zamoyo zosadya.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LEV/11-6e4506ab2854ab0d65409bb9ca4d34fa.mp3?version_id=1068—