Mau Oyamba
Mneneri Hoseya adalalikira pambuyo pa mneneri Amosi, ku Israele, ufumu wakumpoto, mzinda wa Samariya usanapasuke. Iye amamva chisoni poona kuti Aisraelewo ngosakhulupirika ndi opembedza milungu ina. Tsono anayerekeza kusakhulupirika kwaoko ndi zimene mwiniwakeyo adazipeza m’banja lake, mkazi wake atamchokera nkutsata amuna ena. Chonchonso anthu a Mulunguwo anafulatira Yehova Mbuye wao natsata milungu ina. Mulungu sadzalephera kuwalanga chifukwa cha kusakhulupirika kwaoko; komabe potsiriza, chifukwa cha chikondi chake chosasinthika, adzawakokeranso kwa Iye ndipo adzayanjana nawonso. Atsimikiza chikondi chakecho ndi mauwa, “Ndidzakusiya bwanji, Efuremu? Ndidzakupereka bwanji, Israele…Mtima wanga watembenuka m’kati mwanga, zachifundo zanga zilira zonse pamodzi” (11.8).
Za mkatimu
Ukwati wa Hoseya ndi banja lake
1.1—3.5
Mau a Yehova odzudzula Israele
4.1—13.16
Uthenga wa kulapa ndinso lonjezo la kukonzedwanso kwa zinthu
14.1-9