Categories
HOSEYA

HOSEYA 9

Tchimo la Israele ndi zotsatira zake

1 Usakondwera, Israele, ndi kusekerera, ngati mitundu ya anthu; pakuti wachita chigololo kuleka Mulungu wako, wakonda mphotho ya chigololo pa dwale la tirigu lililonse.

2 Dwale ndi choponderamo mphesa sizidzawadyetsa, vinyo watsopano adzamsowa.

3 Sadzakhala m’dziko la Yehova; koma Efuremu adzabwerera kunka ku Ejipito; ndipo adzadya chakudya chodetsa mu Asiriya.

4 Sadzatsanulira Yehova nsembe zavinyo; sizidzamkomera Iye nsembe zao; zidzakhala kwa iwo ngati mkate wa achisoni; onse akudyako adzadetsedwa; pakuti mkate wao udzakhala wa njala yao, uwu sudzalowa m’nyumba ya Yehova.

5 Mudzachitanji tsiku la misonkhano yoikika, ndi tsiku la chikondwerero cha Yehova.

6 Pakuti taonani, anachokera chionongeko, koma Ejipito adzawasonkhanitsa, Mofi adzawaika m’manda; khwisa adzalanda zofunika zao zasiliva; minga idzakhala m’mahema mwao.

7 Masiku a kulanga afika, masiku a kubwezera afika; Israele adzadziwa;mneneriali wopusa, munthu wamzimu ali wamisala, chifukwa cha kuchuluka mphulupulu yako, ndi popeza udani ndi waukulu.

8 Efuremu ndiye wozonda kwa Mulungu wanga; kunena za mneneri, msampha wa msodzi uli m’njira zake zonse, ndi udani m’nyumba ya Mulungu wake.

9 Anadzivunditsa kwambiri, monga masiku a Gibea; adzakumbukira mphulupulu yao, adzalanga zochimwa zao.

10 Ndinapeza Israele ngati mphesa m’chipululu, ndinaona makolo anu ngati chipatso choyamba cha mkuyu nyengo yake yoyamba; koma anadza kwa Baala-Peori, nadzipatulira chonyansacho, nasandulika onyansa, chonga chija anachikonda.

11 Kunena za Efuremu, ulemerero wao udzauluka ndi kuchoka ngati mbalame; sipadzakhala kubala, ndi kukhala ndi pakati, ndi kuima.

12 Angakhale alera ana ao, koma ndidzawasowetsa, wosatsala munthu; ndithunso tsoka iwowa, pamene ndiwachokera.

13 Efuremu, monga ndaona, akunga Tiro, wookedwa pokoma; koma Efuremu adzatulutsira ana ake wakuwaphera.

14 Apatseni, Yehova; mudzapatsa chiyani? Muwapatse mimba yotayataya, ndi mawere ouma.

15 Choipa chao chonse chili mu Giligala; pakuti pamenepo ndinawada, chifukwa cha kuipa kwa machitidwe ao ndidzawainga kuwachotsa m’nyumba mwanga; sindidzawakondanso; akalonga ao onse ndiwo opanduka.

16 Efuremu wakanthidwa, muzu wao wauma, iwo sadzabala zipatso; inde ngakhale abala, koma ndidzapha zipatso zofunika za mimba yao.

17 Mulungu wanga adzawataya, pakuti sanammvere Iye; ndipo adzakhala othawathawa mwaamitundu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/HOS/9-5f1dd37c92c4b4258807946d52087f5f.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *