Kupembedza mafano ndi kusamvera kwa Israele
1 Lipenga kukamwa kwako. Akudza ngati chiombankhanga, kulimbana ndi nyumba ya Yehova; chifukwa analakwirachipanganochanga, napikisana nacho chilamulo changa.
2 Adzafuulira kwa Ine, Mulungu wanga, ife Aisraele tikudziwani.
3 Israele wachitaya chokoma, mdani adzamlondola.
4 Analonga mafumu, koma sikunachokera kwa Ine; anaika akalonga, koma sindinadziwa; anadzipangira mafano asilivawao ndi golide wao, kuti akalikhidwe.
5 Mwanawang’ombe wako wakutaya, Samariya iwe; mkwiyo wanga wayakira iwo; adzalephera kuyera mtima mpaka liti?
6 Pakuti ichi chomwe chafumira kwa Israele; mmisiri wampanga, koma sali Mulungu; inde mwanawang’ombe wa Samariya adzaphwanyikaphwanyika.
7 Pakuti abzala mphepo, nadzakolola kamvulumvulu; alibe tirigu wosasenga; ngala siidzatulutsa ufa; chinkana iutulutsa, alendo adzaumeza.
8 Israele wamezedwa; tsopano ali mwaamitundungati chotengera choti munthu sakondwera nacho.
9 Pakuti anakwera kunka ku Asiriya, ngati mbidzi ya pa yokha mwini wake; Efuremu walembera omkonda ngati antchito.
10 Inde angakhale alembera mwa amitundu ndidzawasonkhanitsa tsopano; ndipo ayamba kuchepa chifukwa cha katundu wa mfumu ya akalonga.
11 Popeza Efuremu anachulukitsa maguwa a nsembe akuchimwako, maguwa a nsembe omwewo anamchimwitsa.
12 Ndinamlembera zinthu zambirimbirizo za chilamulo changa, koma zinayesedwa ngati chinthu chachilendo.
13 Kunena za nsembe za zopereka zanga, aphera nsembe yanyama, naidya; koma Yehova sazilandira; tsopano adzakumbukira mphulupulu yao, nadzalanga zochimwa zao; adzabwerera kunka ku Ejipito.
14 Pakuti Israele waiwala Mlengi wake, namanga akachisi; ndipo Yuda wachulukitsa mizinda yamalinga; koma ndidzatumizira mizinda yake moto, nudzatha nyumba zake zazikulu.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/HOS/8-18c048283f98cc4c860c68fe9ae69711.mp3?version_id=1068—