Categories
HOSEYA

HOSEYA 4

Mlandu pakati pa Mulungu ndi Israele

1 Imvani mau a Yehova, inu ana a Israele; pakuti Yehova ali ndi mlandu ndi okhala m’dziko, popeza palibe choonadi, kapena chifundo, kapena kudziwa Mulungu m’dziko.

2 Koma kulumbira, ndi kunama, ndi kupha, ndi kuba, ndi kuchita chigololo; aboola, ndi mwazi ukhudzana nao mwazi.

3 Chifukwa chake dziko lidzachita chisoni, ndi aliyense wokhalamo adzalefuka, pamodzi ndi nyama zakuthengo, ndi mbalame za m’mlengalenga; ndi nsomba za m’nyanja zomwe zidzachotsedwa.

4 Koma munthu asatsutsane ndi mnzake, kapena kudzudzula mnzake; popeza anthu ako ndiwo akunga otsutsana ndi wansembe.

5 Ndipo udzakhumudwa usana, ndimneneriyemwe adzakhumudwa pamodzi ndi iwe usiku; ndipo ndidzaononga mai wako.

6 Anthu anga aonongeka chifukwa cha kusadziwa; popeza unakana kudziwa, Inenso ndikukaniza, kuti usakhale wansembe wanga; popeza waiwala chilamulo cha Mulungu wako, Inenso ndidzaiwala ana ako.

7 Monga anachuluka, momwemo anandichimwira; ndidzasanduliza ulemerero wao ukhale manyazi.

8 Adyerera tchimo la anthu anga, nakhumbira chosalungama chao, yense ndi mtima wake.

9 Ndipo kudzakhala monga anthu, momwemo wansembe; ndipo ndidzawalanga chifukwa chanjira zao, ndi kuwabwezera machitidwe ao.

10 Ndipo adzadya, koma osakhuta; adzachita chigololo, koma osachuluka; pakuti waleka kusamalira Yehova.

11 Chigololo, ndi vinyo, ndi vinyo watsopano, zichotsa mtima.

12 Anthu anga afunsira kumtengo wao, ndi ndodo yao iwafotokozera; pakuti mzimu wachigololo wawalakwitsa, ndipo achita chigololo kuchokera Mulungu wao.

13 Pamwamba pa mapiri aphera nsembe, nafukiza pazitunda, patsinde pa thundu, ndi minjali, ndi mkundi; popeza mthunzi wake ndi wabwino, chifukwa chake ana anu aakazi achita uhule, ndi apongozi anu achita chigololo.

14 Sindidzalanga ana anu aakazi pochita iwo uhule, kapena apongozi anu pochita chigololo iwo; pakuti iwo okha apatukira padera ndi akazi achiwerewere, naphera nsembe pamodzi ndi akazi operekedwa ku uhule; ndi anthu osazindikirawo adzagwetsedwa chamutu.

15 Chinkana iwe, Israele, uchita uhule, koma asapalamule Yuda; ndipo musafika inu ku Giligala, kapena kukwera ku Betaveni, kapena kulumbira, Pali Yehova.

16 Pakuti Israele wachita kuuma khosi ngati ng’ombe yaikazi yaing’ono youma khosi; tsopano Yehova adzawadyetsa ngatimwanawankhosakuthengo lalikulu.

17 Efuremu waphatikana ndi mafano, mlekeni.

18 Chakumwa chao chasasa, achita uhule kosalekeza; akulu ao akonda manyazi kwambiri.

19 Mphepo yamkulunga m’mapiko ake, ndipo adzachita manyazi chifukwa cha nsembe zao.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/HOS/4-e9cbf51d18eb8fac295a99a21bf78333.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *