Akwatiranso mkazi woipa, kufaniziranso zochita ana a Israele
1 Ndipo Yehova anati kwa ine, Mukanso, konda mkazi wokondedwa ndi bwenzi lake, koma wakuchita chigololo, monga Yehova akonda ana a Israele, angakhale atembenukira kumilungu ina, nakonda nchinchi za mphesa zouma.
2 M’mwemo ndinadzigulira iye ndi masekeli khumi ndi asanu asiliva, ndi homeri ndi leteki wa barele;
3 ndipo ndinati kwa iye, Uzikhala ndi ine masiku ambiri, usachita chigololo, usakhala mkazi wa mwamuna aliyense; momwemo inenso nawe.
4 Pakuti ana a Israele adzakhala masiku ambiri opanda mfumu, ndi opanda kalonga, ndi opanda nsembe, ndi opanda choimiritsa, ndi opandaefodikapenaaterafi;
5 atatero ana a Israele adzabwera, nadzafuna Yehova Mulungu wao, ndi Davide mfumu yao, nadzafika ndi mantha kwa Yehova, ndi ku ukoma wake masiku otsiriza.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/HOS/3-4c3a9f43b001c991074188e26b2637e3.mp3?version_id=1068—