Categories
HOSEYA

HOSEYA 13

Tchimo la Israele ndi kulangidwa kwake

1 Pamene Efuremu analankhula panali kunjenjemera; anadzikweza mu Israele; koma pamene anapalamula mwaBaala, anafa.

2 Ndipo tsopano aonjeza kuchimwa, nadzipangira mafano oyenga asilivawao, mafano monga mwa nzeru zao, onsewo ntchito ya amisiri; anena za iwo, Anthu ophera nsembe apsompsone anaang’ombe.

3 Chifukwa chake adzakhala ngati mtambo wa m’mawa, ndi ngati mame akamuka mamawa, ngati mungu umene mphepo iuuluza kudwale, ndi ngati utsi wotuluka kukafwambira.

4 Koma Ine ndiye Yehova Mulungu wako chichokere m’dziko la Ejipito, ndipo suyenera kudziwa mulungu wina koma Ine; ndi popanda Ine palibe mpulumutsi.

5 Ndinakudziwa m’chipululu, m’dziko lotentha kwambiri.

6 Monga mwa podyetsa pao, momwemo anakhuta; anakhuta, ndi mtima wao unakwezeka; chifukwa chake anandiiwala Ine.

7 Chifukwa chake ndikhala nao ngati mkango; ngati nyalugwe ndidzalalira kunjira.

8 Ndidzakomana nao ngati chimbalangondo chochilanda ana ake, ndi kung’amba chokuta mtima wao; ndi pomwepo ndidzawalusira ngati mkango; chilombo chidzawamwetula.

9 Israele, chikuononga ndi ichi, chakuti utsutsana ndi Ine, chithandizo chako.

10 Ili kuti mfumu yako tsopano, kuti ikupulumutse m’mizinda yako yonse? Ndi oweruza ako amene unanena za iwo, Ndipatseni mfumu ndi akalonga?

11 Ndinakupatsa mfumu mu mkwiyo wanga; ndinamchotsanso mu ukali wanga.

12 Mphulupulu ya Efuremu yamangika, tchimo lake lisungika.

13 Zowawa zonga za mkazi wobala zidzamgwera, ndiye mwana wopanda nzeru; pakuti pali nyengo yakuti asachedwe mobalira ana.

14 Ndidzawaombola kumphamvu ya kumanda, ndidzawaombola kuimfa; imfa, miliri yako ili kuti? Kulekerera kudzabisika pamaso panga.

15 Chinkana abala mwa abale ake, mphepo ya kum’mawa idzafika, mphepo ya Yehova yokwera kuchokera kuchipululu; ndi gwero lake lidzaphwa, ndi kasupe wake adzauma, adzafunkha chuma cha akatundu onse ofunika.

16 Samariya adzasanduka wabwinja, pakuti anapandukana ndi Mulungu wake; iwo adzagwa ndi lupanga, ana ao amakanda adzaphwanyika, ndi akazi ao okhala ndi pakati adzatumbulidwa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/HOS/13-aebf9218e58c9049adaf7d9c0c43f99f.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *