Categories
HOSEYA

HOSEYA 10

1 Israele ndi mpesa wotambalala, wodzibalira wokha zipatso; monga umo zinachulukira zipatso zake, momwemo anachulukitsa maguwa a nsembe ake; monga mwa kukoma kwake kwa dziko lake anapanga zoimiritsa zokoma.

2 Mtima wao wagawikana, tsopano adzapezeka opalamula, adzapasula maguwa ao a nsembe, nadzaononga zoimiritsa zao.

3 Pakuti tsopano adzati, Tilibe mfumu, popeza sitiopa Yehova; ndi mfumu idzatichitira chiyani?

4 Anena mau akulumbira monama, pakuchita mapangano momwemo; chiweruzo chiphuka ngati zitsamba zowawa m’michera ya munda.

5 Okhala mu Samariya adzaopera chifanizo cha anaang’ombe a ku Betaveni; pakuti anthu ake adzamva nacho chisoni, ndi ansembe ake amene anakondwera nacho, chifukwa cha ulemerero wake, popeza unachichokera.

6 Adzachitengeranso ku Asiriya chikhale mphatso ya kwa mfumu Yarebu; Efuremu adzatenga manyazi, ndi Israele adzachita manyazi ndi uphungu wake.

7 Ndipo Samariya, mfumu yake yamwelera ngati thovu pamadzi.

8 Ndipo misanje ya Aveni, ndiyo tchimo la Israele, idzaonongeka; minga ndi mitungwi idzamera pa maguwa ao a nsembe; ndipo adzati kwa mapiri, Tiphimbeni; ndi kwa zitunda, Tigwereni.

9 Israele, wachimwa kuyambira masiku a Gibea; pomwepo anaimabe; nkhondo ya pa ana a chosalungama siinawapeze ku Gibea.

10 Pamene ndifuna ndidzawalanga, ndi mitundu ya anthu idzawasonkhanira pomangidwa iwo pa zolakwa zao ziwiri.

11 Ndipo Efuremu ndiye ng’ombe yaikazi yaing’ono, yozereweredwa, yokonda kupuntha tirigu; koma ndapita pa khosi lake lokoma; ndidzamsenzetsa Efuremu goli; Yuda adzalima, Yakobo adzaphwanya chibuluma chake.

12 Mudzibzalire m’chilungamo mukolole monga mwa chifundo; limani masala anu, pakuti yafika nthawi ya kufuna Yehova, mpaka afika Iye, navumbitsira inu chilungamo.

13 Mwalima choipa, mwakolola chosalungama, mwadya zipatso za mabodza; pakuti watama njira yako ndi kuchuluka kwa anthu ako amphamvu.

14 Momwemo phokoso lidzaukira anthu ako, ndi malinga ako onse adzapasuka, monga Salimani anapasula Betaribele; tsiku la nkhondo amai anaphwanyika pamodzi ndi ana ake.

15 Momwemo adzakuchitirani Betele, chifukwa cha choipa chanu chachikulu; mbandakucha mfumu ya Israele idzalikhika konse.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/HOS/10-80907289bc518b6cde7deadba346282b.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *