Categories
GENESIS

GENESIS 6

Kulowerera kwa mtundu wa anthu

1 Ndipo panali pamene anthu anayamba kuchuluka padziko, ndi ana aakazi anawabadwira iwo,

2 kuti ana aamuna a Mulungu anayang’ana ana aakazi a anthu, kuti iwo anali okongola; ndipo anadzitengera okha akazi onse amene anawasankha.

3 Ndipo anati Yehova, Mzimu wanga sudzakangana ndi anthu nthawi zonse, chifukwa iwonso ndiwo thupi lanyama: koma masiku ake adzakhala zaka zana limodzi kudza makumi awiri.

4 Padziko lapansi panali anthu akuluakulu masiku omwewo ndiponso pambuyo pake, ana aamuna a Mulungu atalowa kwa ana aakazi a anthu, ndipo anabalira iwo ana, amenewo ndiwo anthu amphamvu akalekale, anthu omveka.

5 Ndipo anaona Yehova kuti kuipa kwa anthu kunali kwakukulu padziko lapansi, ndiponso kuti ndingaliro zonse za maganizo a mitima yao zinali zoipabe zokhazokha.

6 Ndipo Yehova anamva chisoni chifukwa anapanga munthu padziko lapansi, ndipo anavutika m’mtima mwake.

7 Ndipo anati Yehova, Ndidzafafaniza anthu amene ndawalenga padziko lapansi; anthu, ndi nyama, ndi zokwawa, ndi mbalame za m’mlengalenga: pakuti ndimva chisoni chifukwa ndapanga izo.

8 Koma Nowa anapeza ufulu pamaso pa Yehova.

9 Mibadwo ya Nowa ndi iyi: Nowa anali munthu wolungama ndi wangwiro m’mibadwo yake; Nowa anayendabe ndi Mulungu.

10 Ndipo Nowa anabala ana aamuna atatu: Semu, Hamu ndi Yafeti.

11 Ndipo dziko lapansi linavunda pamaso pa Mulungu, dziko lapansi ndipo linadzala ndi chiwawa.

12 Ndipo Mulungu anaona dziko lapansi, ndipo taonani, linavunda; pakuti anthu onse anavunditsa njira yao padziko lapansi.

Chigumula

13 Ndipo Mulungu anati kwa Nowa, Chimaliziro chake cha anthu onse chafika pamaso panga; pakuti dziko lapansi ladzala ndi chiwawa chifukwa cha iwo; taonani, ndidzaononga iwo pamodzi ndi dziko lapansi.

14 Udzipangire wekha chingalawa cha mtengo wanjale; upangemo zipinda m’chingalawamo, ndipo upake ndi utoto m’kati ndi kunja.

15 Kupanga kwake ndi kotere: m’litali mwake mwa chingalawa mikono mazana atatu, m’mimba mwake mikono makumi asanu, m’msinkhu mwake mikono makumi atatu.

16 Uike zenera m’chingalawacho, ulimalize ndi kusiya mkono umodzi pamwamba pake: khomo la chingalawa uike m’mbali mwake; nuchipange ndi nyumba yapansi, ndi yachiwiri, ndi yachitatu.

17 Ndine, taonani, ndipo Ine ndidzadzetsa chigumula cha madzi padziko lapansi, kuti chiononge zamoyo zonse, m’mene muli mpweya wa moyo pansi pathambo; zinthu zonse za m’dziko lapansi zidzafa.

18 Koma ndidzakhazikitsa ndi iwe pangano langa; ndipo udzalowa m’chingalawamo iwe ndi ana ako ndi mkazi wako, ndi akazi a ana ako pamodzi ndi iwe.

19 Ndipo zonse zokhala ndi moyo, ziwiriziwiri za mtundu wao ulowetse m’chingalawamo, kuti zikhale ndi moyo pamodzi ndi iwe; zikhale zamphongo ndi zazikazi.

20 Za mbalame monga mwa mitundu yao, ndi zinyama monga mwa mitundu yao, ndi zokwawa zonse za dziko lapansi monga mwa mitundu yao, ziwiriziwiri monga mwa mitundu yao, zidzadza kwa iwe kuti zikhale ndi moyo.

21 Ndipo iwe udzitengereko wekha zakudya zonse zodyedwa, nudzisonkhanitsire izi wekha: ndipo zidzakhala zakudya za iwe ndi za iwo.

22 Chotero anachita Nowa, monga mwa zonse anamlamulira iye Mulungu, momwemo anachita.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/6-f8f61fd7b59ea7e66b41611084360816.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *