Categories
GENESIS

GENESIS 50

Maliro a Yakobo

1 Ndipo Yosefe anagwa pa nkhope ya atate wake, namlirira iye nampsompsona iye.

2 Ndipo Yosefe anauza akapolo ake asing’anga kuti akonze atate wake ndi mankhwala osungira thupi: ndipo asing’anga anakonza Israele.

3 Ndipo anatha masiku ake makumi anai a iye; chifukwa chomwecho amatsiriza masiku akukonza thupi; ndipo Aejipito anamlira iye masiku makumi asanu ndi awiri.

4 Atapita masiku akumlira iye, Yosefe anati kwa mbumba yaFarao, kuti, Ngatitu ndapeza ufulu pamaso panu, nenanitu m’makutu a Farao kuti,

5 Atate wanga anandilumbiritsa ine, kuti, Taona, ndilinkufa; m’manda m’mene ndadzikonzeratu ndekha m’dziko la Kanani, m’menemo udzandiika ine. Tsopano mundiloletu, ndikwereko, ndipite, ndikaike atate wanga, nditatero ndidzabweranso.

6 Ndipo Farao anati, Pita, kaike atate wako, monga iye anakulumbiritsa iwe.

7 Ndipo Yosefe anapita kukaika atate wake; ndipo anakwera pamodzi ndi akapolo onse a Farao, ndi akulu a pa mbumba yake, ndi akulu onse a m’dziko la Ejipito,

8 ndi mbumba yonse ya Yosefe ndi abale ake, ndi mbumba ya atate wake: ang’ono ao okha, ndi nkhosa zao, ndi ng’ombe zao, anazisiya m’dziko la Goseni.

9 Ndipo anakwera pamodzi ndi iye magaleta ndi apakavalo; ndipo panali khamu lalikulu.

10 Ndipo anafika pa dwale la Atadi, lili tsidya lija la Yordani, pamenepo anamlira maliro a atate wake masiku asanu ndi limodzi.

11 Ndipo pamene anthu okhala m’dzikomo, Akanani, anaona maliro a m’dwale la Atadi, anati, Awa ndi maliro aakulu a Aejipito: chifukwa chake dzina la pamenepo linatchedwa Abele-Mizraimu, pali tsidya lija la Yordani.

12 Ndipo ana ake aamuna anamchitira iye monga anawalamulira iwo;

13 chifukwa kuti ana ake aamuna anamnyamula iye kulowa naye m’dziko la Kanani, ndi kumuika iye m’phanga la munda wa Makipela, limene Abrahamu analigula pamodzi ndi munda, likhale poikira pake, kwa Efuroni Muhiti, patsogolo pa Mamure.

14 Ndipo ataika atate wake, Yosefe anabwera ku Ejipito, iye ndi abale ake, ndi onse amene anakwera pamodzi naye kukaika atate wake.

15 Ndipo pamene abale ake a Yosefe anaona kuti atate wao anafa, anati, Kapena Yosefe adzatida ife, ndipo adzatibwezera ife zoipa zonse tidamchitira iye.

16 Ndipo anatumiza mthenga kwa Yosefe kuti, Atate wathu asanafe analamulira, kuti,

17 Muziti chotero kwa Yosefe, Mukhululukiretu tsopano kulakwa kwa abale anu, ndi kuchimwa kwao, chifukwa kuti anakuchitirani inu choipa; tsopano mutikhululukiretu kulakwa kwa akapolo a Mulungu wa atate wanu. Ndipo Yosefe analira pamene iwo ananena ndi iye.

18 Ndiponso abale ake anamuka namgwadira pamaso pake; nati, Taonani, ife ndife akapolo anu.

19 Ndipo Yosefe anati kwa iwo, Musaope; pakuti ndili ine kodi m’malo a Mulungu?

20 Koma inu, munandipangira ine choipa; koma Mulungu anachipangira chabwino, kuti kuchitike monga lero, kupulumutsa amoyo anthu ambiri.

21 Ndipo tsopano musaope; ine ndidzachereza inu, ndi ana anu aang’ono. Ndipo anawatonthoza iwo mitima yao, nanena nao mokoma mtima.

Kumwalira kwa Yosefe

22 Ndipo Yosefe anakhala mu Ejipito, iye, ndi mbumba ya atate wake; ndipo Yosefe anakhala ndi moyo zaka zana limodzi ndi khumi.

23 Ndipo Yosefe anaona ana a Efuremu a mbadwo wachitatu; ananso a Makiri mwana wamwamuna wa Manase anabadwa pa maondo a Yosefe.

24 Yosefe ndipo anati kwa abale ake, Ndilinkufa ine, koma Mulungu adzaonekera kwa inu, adzakuchotsani inu m’dziko muno kubwera kunka ku dziko limene analumbirira kwa Abrahamu ndi kwa Isaki, ndi kwa Yakobo.

25 Ndipo Yosefe analumbiritsa ana a Israele kuti, Mulungu adzaonekera kwa inu ndithu, ndipo mudzakwera nao mafupa anga kuchokera kuno.

26 Ndipo anafa Yosefe, anali wa zaka zana limodzi ndi khumi; ndipo anakonza thupi lake ndi mankhwala osungira, ndipo anamuika iye m’bokosi mu Ejipito.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/50-91ad4c3e2091639e356c11214e92c65e.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *