Yakobo adalitsa ana ake namwalira
1 Ndipo Yakobo anaitana ana ake aamuna, nati, Sonkhanani inu, kuti ndikuuzeni inu chimene chidzakugwerani inu masiku akudzawo.
2 Sonkhanani, tamvani, ana aamuna a Yakobo;
tamverani Israele atate wanu.
3 Rubeni, ndiwe woyamba wanga,
mphamvu yanga ndi chiyambi cha mphamvu yanga;
ulemu wopambana, ndi mphamvu yopambana.
4 Wobwabwada ngati madzi; sudzapambana;
chifukwa unakwera pa kama wa atate wako;
pamenepo unaipitsapo; anakwera paja ndigonapo.
5 Simeoni ndi Levi ndiwo abale;
zida za mphulupulu ndizo malupanga ao.
6 Mtima wangawe, usalowe mu chiungwe chao;
ulemerero wanga, usadziphatike pa msonkhano yao;
chifukwa m’kukwiya kwao anapha munthu.
M’kufuna kwao anapundula ng’ombe.
7 Kutembereredwe kukwiya kwao,
chifukwa kunali koopsa;
ndi kupsa mtima kwao, chifukwa kunali kwankhalwe.
Ndidzawagawanitsa mu Yakobo.
Ndidzabalalitsa iwo mu Israele.
8 Yuda, abale ako adzakuyamika iwe;
dzanja lako lidzakhala pa khosi la adani ako;
ana aamuna a atate wako adzakuweramira.
9 Yuda ndi mwana wa mkango,
kuchokera kuzomotola, mwananga, wakwera;
anawerama pansi, anabwatama ngati mkango,
ndipo ngati mkango waukazi; ndani adzamukitsa iye?
10 Ndodo yachifumu siidzachoka mwa Yuda,
kapena wolamulira pakati pa mapazi ake,
kufikira atadza Silo;
ndipo anthu adzamvera iye.
11 Adamanga mwana wa kavalo wake pampesa,
ndi mwana wa bulu wake pa mpesa wosankhika;
natsuka malaya ake m’vinyo,
ndi chofunda chake m’mwazi wa mphesa.
12 Maso ake adzafiira ndi vinyo,
ndipo mano ake adzayera ndi mkaka.
13 Zebuloni adzakhala m’mphepete mwa nyanja;
ndipo iye adzakhala dooko la ngalawa;
ndipo malire ake adakhala pa Sidoni.
14 Isakara ndiye bulu wolimba,
alinkugona pakati pa makola.
15 Ndipo anaona popumulapo kuti panali pabwino,
ndi dziko kuti linali lokondweretsa;
ndipo anaweramitsa phewa lake kuti anyamule,
nakhala kapolo wakugwira ntchito ya msonkho.
16 Dani adzaweruza anthu ake,
monga limodzi la mafuko a Israele.
17 Dani adzakhala njoka m’khwalala,
songo panjira,
imene iluma zitendene za kavalo,
kuti womkwera wake agwe chambuyo.
18 Ndadikira chipulumutso chanu, Yehova.
19 Ndi Gadi, achifwamba adzampsinja iye;
koma iye adzapsinja pa chitendeni chao.
20 Ndi Asere, chakudya chake ndicho mafuta,
ndipo adzapereka zolongosoka zachifumu.
21 Nafutali ndi mbawala yomasuka;
apatsa mau abwino.
22 Yosefe ndi nthambi yobala,
nthambi yobala pambali pa kasupe;
nthambi zake ziyangayanga palinga.
23 Eni uta anavutitsa iye kwambiri,
namponyera iye, namzunza.
24 Koma uta wake unakhala wamphamvu,
ndi mikono ya manja ake inalimbitsidwa.
Ndi manja a Wamphamvu wa Yakobo.
(Kuchokera kumeneko ndi mbusa, mwala wa Israele.)
25 Ndi Mulungu wa atate wako amene adzakuthangata iwe,
ndi Wamphamvuyonse, amene adzakudalitsa iwe.
Ndi madalitso a Kumwamba,
madalitso a madzi akuya akukhala pansi,
madalitso a mawere, ndi a mimba.
26 Madalitso a atate wako
apambana mphamvu ndi madalitso a makolo anga,
kufikira ku malekezero a patali a mapiri a chikhalire.
Adzakhala pamutu wa Yosefe,
ndi pakati pamutu wa iye amene ali wolekanitsidwa
ndi abale ake.
27 Benjamini ndiye mmbulu wakulusalusa;
m’mamawa adzadya chomotola,
madzulo adzagawa zofunkha.
28 Awa onse ndiwo mafuko khumi ndi awiri a Israele: izo ndizo zomwe ananena kwa iwo atate wao nawadalitsa; yense monga mdalitso wake anawadalitsa.
29 Ndipo analangiza iwo nati kwa iwo, Ine nditi ndisonkhanitsidwe kwa anthu a mtundu wanga; mundiike ine pamodzi ndi makolo anga m’phanga lili m’munda wa Efuroni Muhiti,
30 m’phanga lili m’munda wa Makipela, umene uli patsogolo pa Mamure, m’dziko la Kanani, limene Abrahamu analigula kwa Efuroni Muhiti pamodzi ndi munda, likhale poikira pake:
31 pamenepo anaika Abrahamu ndi Sara mkazi wake; pamenepo anaika Isaki ndi Rebeka mkazi wake: pamenepo ndinaika Leya:
32 munda ndi phanga lili m’menemo, zinagulidwa kwa ana a Hiti
33 Pamene Yakobo anatha kulangiza ana ake aamuna, anafunya mapazi ake pakama, natsirizika, nasonkhanitsidwa kwa anthu a mtundu wake.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/49-098659bc775f80dce959efb58601b9df.mp3?version_id=1068—