Categories
GENESIS

GENESIS 46

Yakobo atsikira ku Ejipito

1 Ndipo Israele anamuka ulendo wake ndi zonse anali nazo, nafika ku Beereseba, napereka nsembe kwa Mulungu wa Isaki atate wake.

2 Ndipo Mulungu ananena kwa Israele, m’masomphenya a usiku, nati, Yakobo, Yakobo.

3 Nati iye, Ndine pano. Ndipo anati, Ine ndine Mulungu, Mulungu wa atate wako; usaope kunka ku Ejipito; pakuti pamenepo ndidzakusandutsa iwe mtundu waukulu;

4 Ine ndidzatsikira pamodzi ndi iwe ku Ejipito; ndipo Ine ndidzakubwezanso ndithu; ndipo Yosefe adzaika dzanja lake pamaso pako.

5 Ndipo Yakobo anachoka ku Beereseba, ndipo ana aamuna a Israele anamnyamula Yakobo atate wao, ndi ana ao aang’ono, ndi akazi ao, m’magaleta ameneFaraoanatumiza kuti amnyamule iye.

6 Ndipo anatenga ng’ombe zao ndi chuma chao anachipeza m’dziko la Kanani, nadza ku Ejipito, Yakobo ndi mbeu zake zonse pamodzi ndi iye;

7 ana ake aamuna, ndi zidzukulu zake zazimuna, ndi ana aakazi ake, ndi zidzukulu zake zazikazi, ndi mbeu zake zonse anadza nazo mu Ejipito.

8 Maina a ana a Israele amene anadza mu Ejipito ndi awa: Yakobo ndi ana aamuna ake: Rubeni mwana wamwamuna woyamba wa Yakobo.

9 Ndi ana aamuna a Rubeni: Hanoki, ndi Palu, ndi Hezironi, ndi Karimi.

10 Ndi ana aamuna a Simeoni: Yemuwele ndi Yamini, ndi Ohadi, ndi Yakini, ndi Zohari, ndi Shaulo, mwana wamwamuna wa mkazi wa ku Kanani.

11 Ndi ana aamuna a Levi: Geresoni, Kohati, ndi Merari.

12 Ndi ana aamuna a Yuda: Eri, ndi Onani, ndi Sela, ndi Perezi, ndi Zera; koma Eri ndi Onani anafa m’dziko la Kanani. Ndi ana aamuna a Perezi ndiwo Hezironi ndi Hamuli.

13 Ndi ana aamuna a Isakara: Tola ndi Puva, ndi Iyobu, ndi Simironi.

14 Ndi ana aamuna a Zebuloni: Seredi, ndi Eloni ndi Yaleele.

15 Amenewo ndi ana aamuna a Leya, amene anambalira Yakobo ku Padanaramu, pamodzi ndi mwana wamkazi wake Dina; ana aamuna ndi aakazi onse ndiwo anthu makumi atatu kudza atatu.

16 Ndi ana aamuna a Gadi: Zifiyoni, ndi Hagi, ndi Suni, ndi Eziboni, ndi Eri, ndi Arodi, ndi Areli.

17 Ndi ana aamuna a Asere: Imina, ndi Isiva, ndi Isivi, ndi Beriya, ndi Sera mlongo wao; ndi ana a Beriya: Hebere, ndi Malikiele.

18 Amenewa ndi ana a Zilipa, amene Labani anampatsa Leya mwana wake wamkazi, amenewo anambalira Yakobo, anthu khumi ndi asanu ndi mmodzi.

19 Ana a Rakele mkazi wake wa Yakobo: Yosefe ndi Benjamini.

20 Kwa Yosefe kunabadwa m’dziko la Ejipito Manase ndi Efuremu, amene Asenati mwana wamkazi wa Potifera wansembe wa Oni anambalira iye.

21 Ndi ana aamuna a Benjamini: Bela ndi Bekere, ndi Asibele, ndi Gera, ndi Naamani, ndi Ehi ndi Rosi, Mupimu ndi Hupimu, ndi Aridi.

22 Amenewo ndi ana a Rakele, amene anabadwira Yakobo; anthu onse ndiwo khumi ndi anai.

23 Ndi ana aamuna a Dani: Husimu.

24 Ndi ana aamuna a Nafutali: Yazeele, ndi Guni, ndi Yezere ndi Silemu.

25 Amenewa ndi ana a Biliha, amene Labani anampatsa Rakele mwana wake wamkazi, amenewo anambalira Yakobo; anthu onse ndiwo asanu ndi awiri.

26 Ndi anthu onse amene anadza ndi Yakobo mu Ejipito, amene anatuluka m’chuuno mwake, pamodzi ndi akazi a ana aamuna a Yakobo ndiwo makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi mmodzi;

27 ndi ana aamuna a Yosefe, amene anambadwira iye mu Ejipito ndiwo anthu awiri; anthu onse a mbumba ya Yakobo, amene analowa mu Ejipito anali makumi asanu ndi awiri.

Yakobo akomana ndi Yosefe

28 Ndipo anatumiza Yuda patsogolo pake kwa Yosefe, amtsogolere kumuonetsa njira yonka ku Goseni: ndipo anafika ku dziko la Goseni.

29 Ndipo Yosefe anamanga galeta lake nakwera kunka kukakomana naye Israele atate wake, ku Goseni, ndipo anadzionetsera yekha kwa iye, nagwera pakhosi pake nakhala m’kulira pakhosi pake.

30 Ndipo Israele anati kwa Yosefe, Ndife tsopano, popeza ndaona nkhope yako, kuti ukali ndi moyo.

31 Ndipo Yosefe anati kwa abale ake, ndi kwa mbumba ya atate wake, Ndidzanka, ndikauze Farao, ndipo ndidzati kwa iye, Abale anga ndi mbumba ya atate wanga, amene anali m’dziko la Kanani, afika kwa ine;

32 ndipo anthuwo ali abusa chifukwa anakhala oweta ng’ombe; ndipo anadza ndi nkhosa zao ndi ng’ombe zao ndi zonse ali nazo.

33 Ndipo padzakhala pamene Farao adzaitana inu, nadzati, Ntchito yanu njotani?

34 Mudzati, Akapolo anu akhala oweta ng’ombe chiyambire ubwana wathu kufikira tsopano, ife ndi atate athu; kuti mukhale m’dziko la Goseni; chifukwa abusa onse anyansira Aejipito.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/46-6ca9879d206aae064fa8211a3d54fd7e.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *