Kaini ndi Abele. Kuphedwa koyamba
1 Ndipo mwamunayo anadziwa mkazi wake Heva: ndipo anatenga pakati, nabala Kaini, ndipo anati, Ndalandira munthu kwa Yehova.
2 Ndipo anabalanso mphwake Abele. Abele anakhala mbusa wa nkhosa, koma Kaini anali wakulima nthaka.
3 Ndipo panali atapita masiku, Kaini anatenga zipatso za nthaka, nsembe ya kwa Yehova.
4 Ndiponso Abele anatenga iyenso mwana woyamba wa nkhosa zake ndi mafuta omwe. Yehova ndipo anayang’anira Abele ndi nsembe yake:
5 koma sanayang’anire Kaini ndi nsembe yake. Kaini ndipo anakwiya kwambiri, ndipo nkhope yake inagwa.
6 Ndipo Yehova anati kwa Kaini, Ukwiyiranji? Yagweranji nkhope yako?
7 Ukachita zabwino, sudzalandiridwa kodi? Ukaleka kuchita zabwino, uchimo ubwatama pakhomo: kwa iwe kudzakhala kulakalaka kwake, ndipo iwe udzamlamulira iye.
8 Kaini ndipo ananena ndi Abele mphwake. Ndipo panali pamene anali kumunda, Kaini anamuukira Abele mphwake, namupha.
9 Yehova ndipo anati kwa Kaini, Ali kuti Abele mphwako? Ndipo anati, Sindidziwai: kodi ndine woyang’anira mphwanga?
10 Ndipo anati, Wachita chiyani? Mau a mwazi wa mphwako andifuulira Ine kunthaka.
11 Tsopano ndiwe wotembereredwa kunthaka, imene inatsegula pakamwa pake kulandira padzanja lako mwazi wa mphwako:
12 pamene udzalima panthaka siidzaperekanso kwa iwe mphamvu yake: udzakhala wothawathawa ndi woyendayenda padziko lapansi.
13 Ndipo Kaini anati kwa Yehova, Kulangidwa kwanga nkwakukulu kosapiririka.
14 Taonani, mwandiingitsa ine lero lomwe padziko; ndi pankhope panu ndidzabisika; ndipo ndidzakhala wothawathawa ndi woyendayenda padziko lapansi; ndipo kudzatero kuti onse akundipeza adzandipha.
15 Ndipo Yehova anati kwa iye, Chifukwa chake aliyense amene adzapha Kaini kudzabwezedwa kwa iye kasanu ndi kawiri. Ndipo Yehova anaika chizindikiro pa Kaini, kuti asamuphe aliyense akampeza.
Mbumba ya Kaini
16 Ndipo Kaini anatuluka pamaso pa Yehova, ndipo anakhala m’dziko la Nodi, kum’mawa kwake kwa Edeni.
17 Ndipo Kaini anamdziwa mkazi wake; ndipo anatenga pakati, nabala Enoki: ndipo anamanga mzinda, nautcha dzina lake la mzindawo monga dzina la mwana wake, Enoki.
18 Kwa Enoki ndipo kunabadwa Iradi; Iradi ndipo anabala Mehuyaele; Mehuyaele ndipo anabala Metusaele; Metusaele ndipo anabala Lameki.
19 Ndipo Lameki anadzitengera yekha akazi awiri: dzina lake la wina ndi Ada, dzina lake la mnzake ndi Zila.
20 Ndipo Ada anabala Yabala; iye ndiye atate wao wa iwo okhala m’mahema, akuweta ng’ombe.
21 Ndi dzina la mphwake ndilo Yubala; iye ndiye atate wao wa iwo oimba zeze ndi chitoliro.
22 Ndipo Zila, iyenso anabala Tubala-Kaini, mwini wakuphunzitsa amisiri onse a mkuwa ndi a chitsulo; mlongo wake wa Tubala-Kaini ndi Naama.
23 Lameki ndipo anati kwa akazi ake,
Tamvani mau anga, Ada ndi Zila;
inu akazi a Lameki, mverani kunena kwanga:
Ndapha munthu wakundilasa ine,
ndapha mnyamata wakundipweteka ine.
24 Ngati Kaini adzabwezeredwa kasanu ndi kawiri,
koma Lameki makumi asanu ndi awiri.
Kubadwa kwa Seti
25 NdipoAdamuanadziwanso mkazi wake; ndipo anabala mwana wamwamuna, namutcha dzina lake Seti, chifukwa anati iye, Mulungu wandilowezera ine mbeu ina m’malo mwa Abele amene Kaini anamupha.
26 Ndiponso kwa Seti, kwa iye kunabadwa mwana wamwamuna: anamutcha dzina lake Enosi: pomwepo anthu anayamba kutchula dzina la Yehova.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/4-ee2753885b65a822279db0f4483aa4e7.mp3?version_id=1068—