Categories
GENESIS

GENESIS 34

Dina ndi a Sekemu

1 Ndipo Dina mwana wamkazi wa Leya, amene anambalira Yakobo, ananka kukaona akazi a kumeneko.

2 Pamene anamuona iye Sekemu, mwana wake wamwamuna wa Hamori Muhivi, kalonga wa dzikolo, anamtenga nagona ndi iye, namuipitsa.

3 Ndipo mtima wake unakhumba Dina mwana wake wamkazi wa Yakobo, ndipo anamkonda namwaliyo, nanena momkopa namwaliyo.

4 Ndipo anati Sekemu kwa atate wake Hamori kuti, Munditengere ine mkazi uyo akhale mkazi wanga.

5 Ndipo anamva Yakobo kuti anamuipitsa Dina, mwana wake wamkazi; ana ake aamuna anali ndi zoweta zake kudambo: ndipo Yakobo anakhala chete mpaka anafika iwo.

6 Ndipo Hamori atate wake wa Sekemu anatuluka kunka kwa Yakobo kukanena ndi iye.

7 Ndipo pakumva icho ana ake aamuna a Yakobo anabwera pochokera kudambo: amunawo ndipo anapwetekwa mtima, nakwiya kwambiri, chifukwa iyeyo anachita chopusa choipira Israele pakugona ndi mwana wamkazi wa Yakobo; ndicho chosayenera kuchita.

8 Ndipo Hamori ananena ndi iwo, kuti, Mtima wa Sekemu mwana wanga umkhumba mwana wako wamkazi: umpatsetu kuti akhale mkazi wake.

9 Mukwatirane ndi ife: tipatseni ife ana anu akazi, ndiponso dzitengereni ana athu aakazi.

10 Ndipo mudzakhala pamodzi ndi ife, dziko lidzakhala pamaso panu; khalani m’menemo ndi kuchita malonda, ndi kukhala nazo zanuzanu m’menemo.

11 Ndipo Sekemu anati kwa atate wake wa mkazi ndi kwa abale ake, Tipeze ufulu pamaso panu, chimene mudzanena kwa ine ndidzapereka.

12 Mundipemphe ine za mitulo ndi zaulere zambirimbiri, ndipo ndidzapereka monga mudzanena kwa ine; koma mundipatse ine namwaliyo akhale mkazi wanga.

13 Ndipo ana ake aamuna a Yakobo anayankha Sekemu ndi Hamori atate wake monyenga, nanena, popeza anamuipitsa Dina mlongo wao,

14 nati kwa iwo, Sitingathe kuchita ichi, kupereka mlongo wathu kwa mwamuna wosadulidwa; chifukwa kumeneko ndiko kutichepetsa ife.

15 Koma apa pokha tidzakuvomerezani: ngati mudzakhala onga ife ndikudulidwaamuna onse;

16 pamenepo tidzakupatsani inu ana athu aakazi, ndipo tidzadzitengera ana anu aakazi, ndipo tidzakhala pamodzi ndi inu, ndi kukhala mtundu umodzi.

17 Koma mukapanda kutimvera ndi kusadulidwa, pamenepo tidzatenga mwana wathu wamkazi, ndi kumuka naye.

18 Mau ao ndipo anakomera Hamori ndi Sekemu mwana wake wa Hamori.

19 Ndipo mnyamatayo sanachedwe kuchichita popeza anakondwera ndi mwana wake wamkazi wa Yakobo; ndipo iye anali wolemekezedwa woposa onse a pa banja la atate wake.

20 Ndipo Hamori ndi Sekemu mwana wake anafika ku chipata cha mzinda wao, nalankhulana ndi anthu a mzinda wao, kuti,

21 Anthu amenewa ali amtendere pamodzi ndi ife; chifukwa chake akhale m’dzikomo, achite malonda m’menemo: pakuti taonani dzikolo lili lalikulu lokwanira iwo; tidzitengere ana ao aakazi akhale aakazi athu, tiwapatse amenewa ana athu aakazi.

22 Anthuwo adzatiloleza ife tikhale nao anthu amodzi, pokhapo amuna onse a mwa ife adzadulidwa, monga iwo adulidwa.

23 Kodi ng’ombe zao ndi chuma chao ndi zoweta zao sizidzakhala zathu? Pokhapo tivomerezana nao ndipo adzakhala pamodzi ndi ife.

24 Ndipo onse amene anatuluka pa chipata cha mzinda wao anamvera Hamori ndi mwana wake Sekemu, nadulidwa amuna onse akutuluka pa chipata cha mzinda wao.

25 Ndipo panali tsiku lachitatu pamene anamva kuwawa, ana aamuna awiri a Yakobo, Simeoni ndi Levi, abale ake a Dina, anatenga wina lupanga lake wina lake, nalimbika mtima nalowa m’mzinda napha amuna onse.

26 Ndipo anapha Hamori ndi Sekemu mwana wake ndi lupanga, natulutsa Dina m’nyumba ya Sekemu nachoka naye.

27 Ndipo ana aamuna a Yakobo anadza kwa ophedwa nafunkha mzinda chifukwa anamuipitsa mlongo wao.

28 Ndipo analanda nkhosa zao ndi zoweta zao ndi abulu ao, ndi za m’mzinda, ndi za m’munda;

29 ndi chuma chao chonse ndi ana ao ndi akazi ao anawagwira, nafunkha zonse za m’nyumba.

30 Ndipo Yakobo anati kwa Simeoni ndi Levi, Mwandisautsa ndi kundinukhitsa ine mwa anthu okhala m’dzikomu, mwa Akanani ndi mwa Aperizi; ndipo ine ndine wa anthu owerengeka, adzandisonkhanira ine ndi kundikantha: ndipo ndidzapasulidwa ine ndi a pa nyumba yanga.

31 Ndipo iwo anati, Kodi iye ayenera kusandutsa mlongo wathu wadama?

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/34-712269c133e20d1605ac1c6913eb0126.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *