Yakobo ayanjanitsidwa ndi Esau
1 Ndipo Yakobo anatukula maso ake, taonani, anadza Esau, ndi pamodzi naye anthu mazana anai. Ndipo anagawira ana kwa Leya, ndi kwa Rakele, ndi kwa adzakazi awiri aja.
2 Ndipo anaika adzakazi ndi ana ao patsogolo, ndi Leya ndi ana ake pambuyo pao, ndi Rakele ndi Yosefe pambuyo pa onse.
3 Ndipo iye mwini anatsogolera patsogolo pao, nawerama pansi kasanu ndi kawiri mpaka anayandikira mkulu wake.
4 Ndipo Esau anathamangira kukomana naye namfungatira, nagwa pankhope pake, nampsompsona; ndipo analira iwo.
5 Ndipo anatukula maso ake nawaona akazi ndi ana; nati, Ndani awa ali ndi iwe? Ndipo iye anati, Ndiwo ana amene Mulungu anakomera mtima kumpatsa kapolo wanu.
6 Ndipo adzakazi anayandikira ndi ana ao, nawerama pansi.
7 Ndiponso Leya ndi ana ake anayandikira nawerama pansi: pambuyo pake anayandikira Yosefe ndi Rakele, nawerama pansi.
8 Ndipo anati, Nanga khamu lonse limene ndinakomana nalo nlotani? Ndipo anati, Kuti ndipeze ufulu pamaso pa mbuyanga.
9 Ndipo Esau anati, Zanga zikwanira; mbale wanga, khala nazo zako iwe wekha.
10 Ndipo Yakobo anati, Iaitu, ngatitu ndapeza ufulu pamaso panu, mulandire mphatso yanga padzanja langa; pakuti popeza ndinaona nkhope yanu, monga anthu aona nkhope ya Mulungu, ndipo inu mwandivomereza ine.
11 Landiranitu mdalitso wanga umene wafika kwa inu, pakuti Mulungu wandichitira ine zaufulu, ndipo zanganso zindikwanira. Ndipo anamkakamiza, nalandira.
12 Ndipo Esau anati, Tiyeni timuke; nditsogolera ndine.
13 Ndipo anati kwa iye, Mbuyanga adziwa kuti ana ali anthete, ndipo nkhosa ndi zoweta ndili nazo zilinkuyamwitsa: ndipo akathamangitsa tsiku limodzi zoweta zonse zidzafa.
14 Mbuyanga atsogoleretu kapolo wake, ndipo ine ndidzazitsogolera pang’onopang’ono monga mwa mayendedwe a zoweta zili pamaso panga, ndi monga mwa mayendedwe a ana, mpaka ndifike kwa mbuyanga ku Seiri.
15 Ndipo Esau anati, Ndikusiyire anthu ena amene ali ndi ine. Ndipo iye anati, Chifukwa chanji? Ndipeze ine ufulu pamaso pa mbuyanga.
16 Ndipo Esau anabwerera tsiku lomwelo kunka ku Seiri.
17 Ndipo Yakobo anankabe ulendo wake ku Sukoti, namanga nyumba yake pamenepo, namanga makola a zoweta zake: chifukwa chake dzina lake la kumeneko ndi Sukoti.
Yakobo afika ku Sekemu
18 Ndipo Yakobo anafika ndi mtendere kumzinda wa Sekemu umene uli m’dziko la Kanani, pamene anachokera ku Padanaramu; namanga tsasa pandunji pa mzindapo.
19 Ndipo anagula ndi ndalama zana limodzi dera la munda kumeneko anamanga hema wake, padzanja la ana ake a Hamori atate wake wa Sekemu.
20 Ndipo anamanga pamenepo guwa la nsembe, natcha pamenepo El-Elohe-Israele.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/33-b31b30b9f8e4ef2aae55ca926d7415a0.mp3?version_id=1068—