Categories
GENESIS

GENESIS 3

Kuchimwa kwa Adamu ndi Heva

1 Ndipo njoka inali yochenjera yoposa zamoyo zonse za m’thengo zimene anazipanga Yehova Mulungu. Ndipo inati kwa mkaziyo, Eya! Kodi anatitu Mulungu, Usadye mitengo yonse ya m’mundamu?

2 Mkaziyo ndipo anati kwa njoka, Zipatso za mitengo ya m’mundamu tidye.

3 Koma zipatso za mtengo umene uli m’kati mwa munda, Mulungu anati, Musadye umenewo, musakhudze umenewo, mungadzafe.

4 Njokayo ndipo inati kwa mkaziyo, Kufa simudzafai;

5 chifukwa adziwa Mulungu kuti tsiku limene mukadya umenewo, adzatseguka maso anu, ndipo mudzakhala ngati Mulungu, wakudziwa zabwino ndi zoipa.

6 Ndipo pamene anaona mkaziyo kuti mtengo unali wabwino kudya, ndi kuti unali wokoma m’maso, mtengo wolakalakika wopatsa nzeru, anatenga zipatso zake, nadya, napatsanso mwamuna wake amene anali naye, nadya iyenso.

7 Ndipo anatseguka maso ao a onse awiri, nadziwa kuti anali amaliseche: ndipo adasoka masamba amkuyu, nadzipangira matewera.

8 Ndipo anamva mau a Yehova Mulungu alinkuyendayenda m’munda nthawi yamadzulo: ndipo anabisalaAdamundi mkazi wake pamaso pa Yehova Mulungu pakati pamitengo ya m’munda.

9 Ndipo Yehova Mulungu anaitana mwamunayo nati kwa iye, Uli kuti?

10 Ndipo anati, Ndinamva mau anu m’mundamu, ndipo ndinaopa chifukwa ndinali wamaliseche ine; ndipo ndinabisala.

11 Ndipo anati, Ndani anakuuza iwe kuti uli wamaliseche? Kodi wadya za mtengo uja, umene ndinakuuza iwe kuti usadye?

12 Ndipo anati mwamunayo, Mkazi amene munandipatsa ine kuti akhale ndi ine, ameneyo anandipatsa ine za mtengo, ndipo ndinadya.

13 Ndipo Yehova Mulungu anati kwa mkaziyo, Chiyani chimene wachitachi? Ndipo anati mkaziyo, Njoka inandinyenga ine, ndipo ndinadya.

14 Ndipo anati Yehova Mulungu kwa njokayo, Chifukwa kuti wachita ichi, wotembereredwa ndiwe wopambana ndi zinyama zonse ndi zamoyo zonse za m’thengo: uziyenda ndi pamimba pako, uzidya fumbi masiku onse a moyo wako:

15 ndipo ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbeu yako ndi mbeu yake; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira chitendeni chake.

16 Kwa mkaziyo ndipo anati, Ndidzachulukitsa kusauka kwako ndi potenga mimba pako; udzasauka pakubala: udzakhumba mwamuna wako, ndipo iye adzakulamulira iwe.

17 Kwa Adamu ndipo anati, Chifukwa kuti wamvera mau a mkazi wako, nudya za mtengo umene ndinakuuza iwe kuti, Usadyeko; nthaka ikhale yotembereredwa chifukwa cha iwe; m’kusauka udzadyako masiku onse a moyo wako:

18 minga ndi mitula idzakubalira iwe; ndipo udzadya therere la m’thengo:

19 m’thukuta la nkhope yako udzadya chakudya, kufikira kuti udzabwerera kunthaka: chifukwa kuti m’menemo unatengedwa: chifukwa kuti ndiwe fumbi, ndi kufumbiko udzabwerera.

20 Ndipo mwamuna anamutcha dzina la mkazi wake, Heva; chifukwa ndiye amake wa amoyo onse.

21 Yehova Mulungu ndipo anapangira Adamu ndi mkazi wake malaya azikopa, nawaveka iwo.

22 Ndipo anati Yehova Mulungu, Taonani, munthuyo akhala ngati mmodzi wa ife, wakudziwa zabwino ndi zoipa: ndipo tsopano kuti asatambasule dzanja lake ndi kutenga za mtengo wa moyo, ndi kudya, ndi kukhala ndi moyo nthawi zonse,

23 Yehova Mulungu anamtulutsa iye m’munda wa Edeni, kuti alime nthaka m’mene anamtenga iye.

24 Ndipo anamuingitsa munthuyo; nakhazikaakerubicha kum’mawa kwake kwa munda wa Edeni, ndi lupanga lamoto lakuzungulira ponsepo, lakusunga njira ya ku mtengo wa moyo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/3-ac803b5dee7ff3dcff0de60934d699fb.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *