Imfa ndi kuikidwa kwa Sara
1 Ndipo Sara anali wa zaka zana limodzi kudza makumi awiri ndi zisanu ndi ziwiri: ndizo zaka za moyo wa Sara.
2 Ndipo Sara anafa mu Kiriyati-Ariba (ndiwo Hebroni), m’dziko la Kanani; ndipo Abrahamu anadza ku maliro a Sara, kuti amlire.
3 Ndipo Abrahamu anauka pa wakufa wake, nanena kwa ana a Hiti, nati,
4 Ine ndine mlendo wakukhala ndi inu: mundipatse ndikhale ndi manda pamodzi ndi inu, kuti ndiike wakufa wanga ndisamthirenso maso.
5 Ndipo ana a Hiti anayankha Abrahamu nati kwa iye,
6 Mutimvere ife mfumu, ndinu kalonga wamkulu pakati pa ife; muike wakufa wanu m’manda mwathu mosankhika: palibe munthu yense wa ife adzakaniza manda ake, kuti muike wakufa wanu.
7 Ndipo anauka Abrahamu naweramira anthu a m’dzikomo, ana a Hiti.
8 Ndipo ananena nao, kuti, Ngati mukandivomereza kuti ndiike wakufa wanga ndisamthirenso maso, mundimvere ine, mundinenere ine kwa Efuroni mwana wake wa Zohari,
9 kuti andipatse ine phanga la Makipela, limene lili pansonga pamunda wake; pa mtengo wake wonse andipatse pakati pa inu, ndikhale nao manda.
10 Ndipo Efuroni anakhala pakati pa ana a Hiti, ndipo Efuroni Muhiti anayankha Abrahamu alinkumva ana a Hiti, onse amene analowa pa chipata cha mzinda wake, kuti,
11 Iai, mfumu, mundimvere ine; munda ndikupatsani inu, ndi phanga lili m’menemo ndikupatsani inu, pamaso pa ana a anthu anga ndikupatsani inu; ikani wakufa wanu.
12 Ndipo Abrahamu anawerama pamaso pa anthu a m’dzikomo.
13 Ndipo ananena kwa Efuroni alinkumva anthu a m’dzikomo, kuti, Koma ngati ufuna, undimveretu ine: ndidzakupatsa iwe mtengo wake wa munda; uulandire kwa ine, ndipo ndidzaika wakufa wanga m’menemo.
14 Ndipo Efuroni anamyankha Abrahamu, nati kwa iye,
15 Mfumu, mundimvere ine; kadziko ka mtengo wake wa masekeli asilivamazana anai, ndiko chiyani pakati pa ine ndi inu? Ikani wakufa wanu.
16 Ndipo Abrahamu anamvera Efuroni, ndipo Abrahamu anamuyesera Efuroni ndalama zimene ananena alinkumva ana a Hiti, masekeli a siliva mazana anai, ndalama zomwezo agulana nazo malonda.
17 Ndipo munda wa Efuroni umene unali mu Makipela, umene unali patsogolo pa Mamure, munda ndi phanga lili momwemo, ndi mitengo yonse inali m’mundamo, yokhala m’malire monse mozungulira momwemo,
18 inalimbitsidwa kwa Abrahamu ikhale yake, pamaso pa ana a Hiti, pa onse amene analowa pa chipata cha mzinda wake.
19 Zitatha izi Abrahamu anaika Sara mkazi wake m’phanga la munda wa Makipela patsogolo pa Mamure (ndiwo Hebroni), m’dziko la Kanani.
20 Ndipo ana a Hiti analimbitsira Abrahamu munda, ndi phanga lili m’menemo, likhale lake lamanda.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/23-14572c4b955c58837c431f5a8996ed45.mp3?version_id=1068—