Abrahamu kwa mfumu Abimeleki
1 Abrahamu ndipo anachoka kumeneko kunka ku dziko la kumwera, ndipo anakhala pakati pa Kadesi ndi Suri, ndipo anakhala ngati mlendo mu Gerari.
2 Ndipo Abrahamu anati za Sara mkazi wake, Iye ndiye mlongo wanga: ndipo Abimeleki mfumu ya Gerari anatumiza namtenga Sara
3 Koma Mulungu anadza kwa Abimeleki m’kulota kwa usiku, nati kwa iye, Taona, wakufa iwe, chifukwa cha mkazi amene wamtenga: pakuti iye ndiye mkazi wa mwini.
4 Koma Abimeleki sanayandikire naye; ndipo anati, Ambuye, kodi mudzaphanso mtundu wolungama?
5 Kodi iye sanati kwa ine, Ndiye mlongo wanga: ndipo mkazi iye yekha anati, Iye ndiye mlongo wanga: ndi mtima wanga wangwiro ndi manja anga osachimwa ndachita ine ichi.
6 Ndipo Mulungu anati kwa iye m’kulota, Inde ndidziwa Ine, kuti wachita icho ndi mtima wangwiro, ndipo Inenso ndinakuletsa iwe kuti usandichimwire ine: chifukwa chake sindinakuloleze iwe kuti umkhudze mkaziyo.
7 Tsopano, umbwezere munthuyo mkazi wake; chifukwa iye ndiye mneneri, ndipo adzakupempherera iwe, ndipo udzakhala ndi moyo: koma ukaleka kumbwezera, udziwe kuti udzafa ndithu, iwe ndi onse amene uli nao.
8 Ndipo Abimeleki analawira m’mamawa, naitana anyamata ake onse, nanena zonse zimenezo m’makutu mwao, ndipo anthu anaopa kwambiri
9 Ndipo Abimeleki anaitana Abrahamu, nati kwa iye, Watichitira ife chiyani iwe? Ndakuchimwiranji iwe kuti waufikitsa pa ine ndi pa ufumu wanga uchimo waukulu? Wandichitira ine zosayenera kuzichita.
10 Ndipo Abimeleki anati kwa Abrahamu, Unaona chiyani iwe kuti wachita ichi?
11 Ndipo Abrahamu anati, Chifukwa ndinati, Pompano palibe ndithu kumuopa Mulungu, ndipo adzandipha ine chifukwa cha mkazi wanga.
12 Koma ndiye mlongo wanga ndithu, mwana wa atate wanga, koma si mwana wa amai wanga: ndipo anakhala ndi ine mkazi wanga.
13 Ndipo panali pamene Mulungu anandiyendetsa ine kunyumba kwa atate wanga, ndinati kwa mkaziyo, Ichi ndicho chokoma mtima udzandichitire ine, konse kumene tidzafika ife, uzinena za ine, Iye ndiye mlongo wanga.
14 Ndipo Abimeleki anatenga nkhosa ndi ng’ombe ndi akapolo ndi adzakazi nampatsa Abrahamu, nambwezera iye Sara mkazi wake.
15 Ndipo Abimeleki anati, Taona dziko langa lili pamaso pako; kumene kuli kwabwino pamaso pako takhala kumeneko.
16 Kwa Sara ndipo anati, Taona, ndapatsa mlongo wako ndalama zasilivamazana khumi; taona, izo ndizo zoyeretsa maso za kwa onse amene ali ndi iwe: ndi pamaso pa onse ukhale wolungama.
17 Ndipo Abrahamu anapemphera Mulungu, ndipo Mulungu anachiritsa Abimeleki, ndi mkazi wake, ndi adzakazi ake; ndipo anabala ana.
18 Pakuti Yehova anatseketsa mimba yonse ya a m’nyumba ya Abimeleki, chifukwa cha Sara mkazi wake wa Abrahamu.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/20-27796640a9bf389abc70fd76a250db1b.mp3?version_id=1068—