Categories
GENESIS

GENESIS 18

Amithenga atatu amuonekera Abrahamu

1 Ndipo Yehova anamuonekera iye pa mtengo yathundu ya ku Mamure, pamene anakhala pa khomo la hema wake pakutentha dzuwa.

2 Ndipo anatukula maso ake, nayang’ana, taonani, anthu atatu anaima pandunji pake; pamene anaona iwo, anawathamangira kuchoka ku khomo la hema kukakomana nao, nawerama pansi, nati,

3 Mbuyanga, ngatitu ndi ndikapeza ufulu pamaso panu, musapitiriretu pa kapolo wanu;

4 nditengetu madzi pang’ono, ndikusambitseni mapazi anu, mupumule pansi pa mtengo;

5 ndipo ndidzatenga chakudya pang’ono, nimutonthoze mitima yanu; mutatero mudzapitirira, chifukwa mwafika kwa kapolo wanu. Ndipo anati, Chita chomwecho monga momwe wanena.

6 Ndipo Abrahamu analowa msanga m’hema wake kwa Sara, nati, Konza msanga miyeso itatu ya ufa wosalala, nuumbe, nupange mikate.

7 Ndipo Abrahamu anafulumira kunka kuzoweta, natenga kamwana ka ng’ombe kofewa ndi kabwino, napatsa mnyamata, ndipo anafulumira kuphika.

8 Ndipo anatenga mafuta amkaka, ndi mkaka, ndi kamwana ka ng’ombe kamene anaphika, naziika patsogolo pao; ndipo iye anaimirira iwo patsinde pa mtengo, ndipo anadya.

9 Ndipo anati kwa iye, Ali kuti Sara mkazi wako? Ndipo anati, Taonani m’hemamo.

10 Ndipo anati, Ndidzabwera kwa iwe ndithu pakufika nyengo yake; taonani Sara mkazi wako adzakhala ndi mwana wamwamuna. Ndipo Sara anamva pakhomo pa hema amene anali pambuyo pake.

11 Koma Abrahamu ndi Sara anali okalamba, anapitirira masiku ao; ndipo kunaleka kwa Sara konga kumachita ndi akazi;

12 ndipo Sara anaseka m’mtima mwake, nati, Kodi ndidzakhala ndi kukondwa ine nditakalamba, ndiponso mbuyanga ali wokalamba?

13 Ndipo Yehova anati kwa Abrahamu, Bwanji anaseka Sara, kuti, Kodi ndidzabala ine ndithu, ine amene ndakalamba?

14 Kodi chilipo chinthu chomkanika Yehova? Pa nthawi yoikidwa ndidzabwera kwa iwe, pakufika nyengo yake, ndipo Sara adzakhala ndi mwana wamwamuna.

15 Koma Sara anakana, nati, Sindinasekai; chifukwa anaopa. Ndipo anati, Iai; koma unaseka.

16 Ndipo anthuwo anauka kuchokera kumeneko nayang’ana ku Sodomu; ndipo Abrahamu ananka nao kuwaperekeza.

17 Ndipo Yehova adati, Kodi ndidzabisira Abrahamu chimene ndichita?

18 Pakuti Abrahamu adzakhala ndithu wamkulu ndi wamphamvu, ndipo mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsika mwa iye?

19 Chifukwa ndamdziwa iye kuti alamulire ana ake ndi banja lake la pambuyo pake, kuti asunge njira ya Yehova, kuchita chilungamo ndi chiweruziro, kuti Yehova akamtengere Abrahamu chomwe anamnenera iye.

20 Ndipo anati Yehova, Popeza kulira kwa Sodomu ndi Gomora kuli kwakukulu, ndipo popeza kuchimwa kwao kuli kulemera ndithu,

21 ndidzatsikatu ndikaone ngati anachita monse monga kulira kwake kumene kunandifikira: ngati sanatero ndidzadziwa.

Abrahamu apempherera a ku Sodomu

22 Ndipo anthuwo anatembenuka nachoka kumeneko, napita kunka ku Sodomu. Koma Abrahamu anaimabe pamaso pa Yehova.

23 Ndipo Abrahamu anayandikira nati, Kodi mudzaononga olungama pamodzi ndi oipa?

24 Kapena alipo olungama makumi asanu m’kati mwa mzinda; kodi mudzaononga, simudzasiya malowo chifukwa cha olungama makumi asanu ali momwemo?

25 Musamatero ai, kupha olungama pamodzi ndi oipa, kuta olungama akhale monga oipa; musamatero ai; kodi sadzachita zoyenera woweruza wa dziko lonse lapansi?

26 Ndipo anati Yehova, Ndikapeza mu Sodomu olungama makumi asanu m’kati mwa mzinda, ndidzasiya malo onse chifukwa cha iwo.

27 Ndipo anayankha Abrahamu nati, Taonanitu, ndadziyesera kunena kwa Ambuye, ine ndine fumbi ndi phulusa:

28 kapena akaperewera asanu pa olungama makumi asanuwo; kodi mudzaononga mzinda wonse chifukwa cha kuperewera asanu? Ndipo anati, Ndikapeza makumi anai ndi asanu sindidzauononga.

29 Ndipo ananenanso kwa Iye nati, Kapena akapezedwa makumi anai m’menemo. Ndipo anati, Sindidzachita chifukwa cha makumi anai.

30 Ndipo anati, Asakwiyetu Ambuye, ndipo ndidzanenanso: kapena akapezedwa makumi atatu m’menemo? Ndipo anati, Ndikapeza makumi atatu m’menemo sindidzachita.

31 Ndipo anati, Taonanitu, ndadziyesera kunena kwa Ambuye: kapena akapezedwa makumi awiri m’menemo. Ndipo anati, Sindidzachita chifukwa cha makumi awiri.

32 Ndipo anati, Asakwiyetu Ambuye, ndipo ndidzanena kamodzi aka kokha: kapena akapezedwa khumi m’menemo? Ndipo anati, Sindidzachita chifukwa cha khumi.

33 Ndipo Yehova anapita atatha kunena naye Abrahamu: ndipo Abrahamu anabwera kumalo kwake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/18-c9c3040893da0e8085753567f42b711e.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *