Categories
GENESIS

GENESIS 15

Mulungu apangana ndi Abramu

1 Zitapita izo, mau a Yehova anadza kwa Abramu m’masomphenya, kuti, Usaope, Abramu, Ine ndine chikopa chako ndi mphotho yako yaikulukulu.

2 Ndipo Abramu anati, Ambuye Mulungu, mudzandipatsa ine chiyani popeza ndine wopanda mwana, ndi amene adzakhala mwini nyumba yanga ndiye Eliyezere wa ku Damasiko?

3 Ndipo Abramu anati, Taonani, simunandipatse ine mbeu; ndipo, taonani, wobadwa m’nyumba mwanga adzalowa m’malo mwanga.

4 Ndipo, taonani, mau a Yehova anadza kwa iye kuti, Uyu sadzakhala wakulowa m’malo mwako; koma iye amene adzatuluka m’chuuno mwako, ndiye adzakhala wakulowa m’malo mwako.

5 Ndipo anamtulutsa iye kunja, nati, Tayang’anatu kumwamba, uwerenge nyenyezi, ngati ukhoza kuziwerenga zimenezo: ndipo anati kwa iye, Zoterezo zidzakhala mbeu zako.

6 Ndipo anakhulupirira Yehova, ndipo kunayesedwa kwa iye chilungamo.

7 Ndipo anati kwa iye, Ine ndine Yehova amene ndinatulutsa iwe mu Uri wa kwa Akaldeya, kuti ndikupatse iwe dziko limeneli likhale lakolako.

8 Ndipo anati, Ambuye Mulungu, nanga ndidzadziwa bwanji kuti lidzakhala cholowa changa?

9 Ndipo anati kwa iye, Kanditengere Ine ng’ombe yaikazi ya zaka zitatu, ndi mbuzi yaikazi ya zaka zitatu, ndi tonde wa zaka zitatu, ndi njiwa, ndi bunda.

10 Ndipo anatenga iye zonse zimenezo, nazidula pakati, naika bandu popenyana ndi linzake: koma mbalame sanazidule.

11 Pamene miimba inatsikira panyama, Abramu anaingitsa iyo.

12 Ndipo linalinkulowa dzuwa, ndi tulo tatikulu tinamgwera Abramu: ndipo taonani, kuopsa kwa mdima waukulu kunamgwera iye.

13 Ndipo anati kwa Abramu, Dziwitsa ndithu kuti mbeu zako zidzakhala alendo m’dziko la eni, ndipo zidzatumikira iwo, ndipo iwo adzasautsa izo zaka mazana anai;

14 ndiponso mtunduwo adzautumikira, Ine ndidzauweruza: ndiponso pambuyo pake adzatuluka ndi chuma chambiri.

15 Ndipo iwe udzanka kwa makolo ako m’mtendere; nudzaikidwa ndi ukalamba wabwino.

16 Koma iwo adzabweranso kuno mbadwo wachinai: pakuti mphulupulu za Aamori sizinakwaniridwe.

17 Ndipo panali pamene litalowa dzuwa ndi kudza mdima, taonani, ng’anjo yofuka utsi ndi muuni wamoto unadutsa pakati pa mabanduwo.

18 Tsiku lomwelo Yehova anapanganachipanganondi Abramu, nati, Ndidzapatsa mbeu zako dziko ili, kuyambira pamtsinje wa ku Ejipito kufikira pamtsinje waukulu, mtsinje wa Yufurate:

19 Akeni ndi Akenizi, Akadimoni,

20 ndi Ahiti, ndi Aperizi, ndi Arefaimu,

21 ndi Aamori, ndi Akanani, ndi Agirigasi, ndi Ayebusi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/15-43828ba51bf786711580ac93910f8240.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *