Abramu ndi Loti alekana
1 Ndipo anakwera Abramu kuchoka ku Ejipito, iye ndi mkazi wake, ndi zonse anali nazo, ndi Loti pamodzi naye, kunka ku dziko la kumwera.
2 Ndipo Abramu anali wolemera ndithu ndi ng’ombe ndisilivandi golide.
3 Ndipo anankabe ulendo wake kuchokera ku dziko la kumwera kunka ku Betele, kufikira kumalo kumene kunali hema wake poyamba paja pakati pa Betele ndi Ai;
4 kumalo kwa guwa la nsembe analimanga iye kumeneko, poyamba paja; ndipo pamenepo Abramu anaitanira dzina la Yehova.
5 Ndiponso Loti anayenda ndi Abramu anali ndi nkhosa ndi ng’ombe ndi mahema.
6 Ndipo dziko silinathe kuwakwanira iwo, kuti akhale pamodzi: chifukwa kuti chuma chao chinali chambiri, ndipo sanathe kukhala pamodzi.
7 Ndipo panali ndeu, abusa a Abramu kudana ndi abusa a Loti. Akanani ndi Aperizi ndipo analinkukhala nthawi yomweyo m’dzikomo.
8 Ndipo Abramu anati kwa Loti, Tisachite ndeu, ine ndi iwe, abusa anga ndi abusa ako: chifukwa kuti ife ndife abale.
9 Dziko lonse silili pamaso pako kodi? Ulekanetu ndi ine: ukanka iwe ku dzanja lamanzere, ine ndinka ku dzanja lamanja: ukanka iwe ku dzanja lamanja, ine ndinka ku dzanja lamanzere.
10 Ndipo Loti anatukula maso ake nayang’ana chigwa chonse cha Yordani kuti chonsecho chinali ndi madzi ambiri, asanaononge Yehova Sodomu ndi Gomora, monga munda wa Yehova, monga dziko la Ejipito pakunka ku Zowari.
11 Ndipo Loti anasankha chigwa chonse cha Yordani; ndipo Loti anachoka ulendo wake kunka kum’mawa: ndipo analekana wina ndi mnzake.
12 Ndipo Abramu anakhala m’dziko la Kanani, ndipo Loti anakhala m’mizinda ya m’chigwa, nasendeza hema wake kufikira ku Sodomu.
13 Ndipo anthu a ku Sodomu anali oipa ndi ochimwa kwambiri pamaso pa Yehova.
Mulungu alonjeza kwa Abramu kumpatsa Kanani
14 Ndipo Yehova anati kwa Abramu, atalekana naye Loti, Tukulatu maso ako, nuyang’anire kuyambira kumene uliko, kumpoto, ndi kumwera, ndi kum’mawa, ndi kumadzulo:
15 chifukwa kuti dziko lonse limene ulinkuona, ndidzakupatsa iwe ndi mbeu yako nthawi yonse.
16 Ndipo ndidzayesa mbeu yako monga fumbi lapansi: chotere kuti ngati munthu angathe kuwerenga fumbi lapansi, chomwechonso mbeu yako idzawerengedwa.
17 Tauka, nuyendeyende m’dzikoli m’litali mwake ndi m’mimba mwake; chifukwa kuti ndidzakupatsa iwe limenelo.
18 Ndipo Abramu anasuntha hema wake nafika nakhala pa mitengo yathundu ya pa Mamure, imene ili mu Hebroni, nammangira Yehova kumeneko guwa la nsembe.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/13-0d859721be73dee8c1227b976e2c9850.mp3?version_id=1068—