Categories
GENESIS

GENESIS 11

Nsanja ya Babiloni

1 Ndipo dziko lapansi linali la chinenedwe chimodzi ndi chilankhulidwe chimodzi.

2 Ndipo panali pamene anayendayenda ulendo kum’mawa, anapeza chigwa m’dziko la Sinara, ndipo anakhala kumeneko.

3 Ndipo ananenana wina ndi wina, Tiyeni tipange njerwa, tiziotchetse. Ndipo anali ndi njerwa naziyesa miyala, ndi katondo anayesa matope.

4 Ndipo anati, Tiyeni, timange mzinda ndi nsanja, pamutu pake pafikire kumwamba; ndipo tidzipangire ife tokha dzina kuti tisabalalike padziko lonse lapansi.

5 Ndipo Yehova anatsikira kudzaona mzinda ndi nsanja imene analinkumanga ana a anthu.

6 Ndipo Yehova anati, Taonani, anthu ali amodzi, ndipo onse ali nacho chinenedwe chao chimodzi; ndipo ichi ayamba kuchita: ndipo tsopano palibe kanthu kakuletsedwa nao kamene akafuna kuchita.

7 Tiyeni, titsike, pomwepo tisokoneze chinenedwe chao, kuti wina asamvere chinenedwe cha mnzake.

8 Ndipo Yehova anabalalitsa iwo padziko lonse lapansi, ndipo analeka kumanga mzinda.

9 Chifukwa chake anatcha dzina lake Babiloni pakuti kumeneko Yehova anasokoneza chinenedwe cha dziko lonse lapansi; kuyambira pamenepo Yehova anabalalitsa iwo padziko lonse lapansi.

Mibadwo ya Semu

10 Mibadwo ya Semu ndi iyi: Semu anali wa zaka zana limodzi ndipo anabala Aripakisadi, chitapita chigumula zaka ziwiri;

11 ndipo Semu anakhala ndi moyo zaka mazana asanu, atabala Aripakisadi, nabala ana aamuna ndi aakazi.

12 Ndipo Aripakisadi anakhala ndi moyo zaka makumi atatu kudza zisanu nabala Sela;

13 ndipo Aripakisadi anakhala ndi moyo zaka mazana anai kudza zitatu, atabala Sela, nabala ana aamuna ndi aakazi.

14 Ndipo Sela anakhala ndi moyo zaka makumi atatu, nabala Eberi;

15 ndipo Sela anakhala ndi moyo zaka mazana anai kudza zitatu, atabala Eberi, nabala ana aamuna ndi aakazi.

16 Ndipo Eberi anakhala ndi moyo zaka makumi atatu kudza zinai, nabala Pelegi;

17 ndipo Eberi anakhala ndi moyo zaka mazana anai kudza makumi awiri, atabala Pelegi, nabala ana aamuna ndi aakazi.

18 Ndipo Pelegi anakhala ndi moyo zaka makumi atatu, nabala Reu;

19 ndipo Pelegi anakhala ndi moyo zaka mazana awiri kudza zisanu ndi zinai, atabala Reu, nabala ana aamuna ndi aakazi.

20 Ndipo Reu anakhala ndi moyo zaka makumi atatu kudza ziwiri, nabala Serugi:

21 ndipo Reu anakhala ndi moyo zaka mazana awiri kudza zisanu ndi ziwiri, atabala Serugi, nabala ana aamuna ndi aakazi.

22 Ndipo Serugi anakhala ndi moyo zaka makumi atatu, nabala Nahori:

23 ndipo Serugi anakhala ndi moyo zaka mazana awiri, atabala Nahori, nabala ana aamuna ndi aakazi.

24 Ndipo Nahori anakhala ndi moyo zaka makumi awiri kudza zisanu ndi zinai, nabala Tera:

25 ndipo Nahori anakhala ndi moyo zaka zana limodzi kudza khumi ndi zisanu ndi zinai, atabala Tera, nabala ana aamuna ndi aakazi.

26 Ndipo Tera anakhala ndi moyo zaka makumi asanu ndi awiri, nabala Abramu, ndi Nahori ndi Harani.

27 Mibadwo ya Tera ndi iyi: Tera anabala Abramu, ndi Nahori, ndi Harani; ndipo Harani anabala Loti.

28 Ndipo anafa Harani pamaso pa atate wake Tera m’dziko la kubadwa kwake, mu Uri wa kwa Akaldeya.

29 Ndipo Abramu ndi Nahori, anadzitengera okha akazi; dzina lake la mkazi wa Abramu ndilo Sarai; ndi dzina lake la mkazi wa Nahori ndilo Milika, mwana wake wa Harani, atate wake wa Milika, ndi atate wake wa Isika.

30 Koma Sarai anali wouma; analibe mwana.

31 Ndipo Tera anatenga Abramu mwana wake wamwamuna, ndi Loti mwana wa Harani, mwana wake wamwamuna, ndi Sarai mpongozi wake, mkazi wa mwana wake Abramu; ndipo anatuluka pamodzi nao ku Uri wa kwa Akaldeya kuti amuke ku dziko la Kanani, ndipo anafika ku Harani, nakhala kumeneko.

32 Masiku a Tera anali zaka mazana awiri kudza zisanu; ndipo anafa Tera mu Harani.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/GEN/11-68e116a8407f3d88dfca544dcfed1e03.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *