1 Paulo, wandende waKhristuYesu, ndi Timoteo mbaleyo, kwa Filemoni wokondedwayo ndi wantchito mnzathu,
2 ndi kwa Afiya mlongoyo, ndi Arkipo msilikali mnzathu, ndi kwaMpingouli m’nyumba yako:
3 Chisomo kwa inu ndi mtendere za kwa Mulungu Atate wathu ndi Ambuye Yesu Khristu.
4 Ndiyamika Mulungu wanga nthawi zonse, ndi kukumbukira iwe m’mapemphero anga,
5 pakumva za chikondi chako ndi chikhulupiriro uli nacho chakulinga kwa Ambuye Yesu, ndi kwa oyera mtima onse;
6 kuti chiyanjano cha chikhulupiriro chako chikakhale champhamvu podziwa chabwino chilichonse chili mwa inu, cha kwa Khristu.
7 Pakuti ndinali nacho chimwemwe chambiri ndi chisangalatso pa chikondi chako, popeza mitima ya oyera mtima yatsitsimuka mwa iwe, mbale.
Paulo apempherera kapolo wothawa wotembenuka mtima
8 Momwemo, ndingakhale ndili nako kulimbika mtima kwakukulu mu Khristu kukulamulira chimene chiyenera,
9 koma makamaka ndidandaulira mwa chikondi, pokhala wotere, Paulo nkhalamba, ndipo tsopano wandendenso wa Khristu Yesu;
10 ndikudandaulira chifukwa cha mwana wanga, amene ndambala m’ndende, Onesimo,
11 amene kale sanakupindulire, koma tsopano watipindulira bwino iwe ndi ine;
12 amene ndi yemweyo ndakubwezera iwe, ndiye mtima weniweni wa ine.
13 Ameneyo ndikadafuna ine kumsunga akhale nane, kuti m’malo mwako akadanditumikira ine m’ndende za Uthenga Wabwino:
14 koma wopanda kudziwa mtima wako sindinafune kuchita kanthu; kuti ubwino wako usakhale monga mokakamiza, komatu mwaufulu.
15 Pakuti kapena anasiyanitsidwa ndi iwe kanthawi chifukwa cha ichi, ndi kuti udzakhala naye nthawi zonse;
16 osatinso monga kapolo, koma woposa kapolo, mbale wokondedwa, makamaka ndi ine, koma koposa nanga ndi iwe, m’thupi, ndiponso mwa Ambuye.
17 Ngati tsono undiyesa woyanjana nawe, umlandire iye monga ine mwini.
18 Koma ngati anakulakwira kanthu, kapena wokongola kanthu, kanthu, kapena wakongola kanthu, undiwerengere ine kameneko;
19 ine Paulo ndichilemba ndi dzanja langa, ndidzachibwezera ine; kuti ndisanene nawe kuti iwe ndiwe mangawa anga.
20 Inde, mbale, ndikondwere nawe mwa Ambuye: utsitsimutse mtima wanga mwa Khristu.
21 Pokhulupirira kumvera kwako ndikulembera iwe, podziwa kuti udzachitanso koposa chimene ndinena.
22 Koma undikonzerenso pogona; pakuti ndiyembekeza kuti mwa mapemphero anu ndidzapatsidwa kwa inu.
23 Epafra wandende mnzanga mwa Khristu Yesu akukupatsa moni;
24 ateronso, Marko, Aristariko, Dema, Luka, antchito anzanga.
25 Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu chikhale pamodzi ndi mzimu wanu.Amen.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PHM/1-c1ff28ddda308b79f709697f9dd45fb2.mp3?version_id=1068—