Aneneratu motsutsa mapiri a Israele
1 Ndipo mau a Yehova anandidzera, kuti,
2 Wobadwa ndi munthu iwe, lozetsa nkhope yako kumapiri a Israele, uwanenere,
3 nunene, Mapiri a Israele inu, tamverani mau a Yehova Mulungu: Atero Yehova Mulungu kwa mapiri ndi zitunda, kwa mitsinje ndi zigwa, Taonani, Ine ndikufikitsirani lupanga, ndipo ndidzaononga misanje yanu.
4 Ndi maguwa anu a nsembe adzakhala opasuka, ndi zoimiritsa zanu zadzuwa zidzasweka; ndipo ndidzagwetsa ophedwa anu pamaso pa mafano anu.
5 Ndipo ndidzaika mitembo ya ana a Israele pamaso pa mafano anu, ndi kumwaza mafupa anu mozungulira maguwa anu a nsembe.
6 Pokhala inu ponse mizinda idzapasuka, ndi misanje idzakhala yabwinja; kuti maguwa anu a nsembe akhale opasuka ndi mabwinja, ndi mafano anu asweke nalekeke, ndi zoimiritsa zanu zadzuwa zilikhidwe, ndi ntchito zanu zifafanizidwe.
7 Ndi ophedwa adzagwa pakati panu, motero mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
8 Koma ndidzasiyapo otsala, popeza mudzakhala nao ena akupulumuka lupanga mwaamitundupobalalitsidwa inu m’maiko maiko.
9 Pamenepo akupulumuka anu adzandikumbukira Ine kwa amitundu kumene anatengedwa ndende, kuti ndasweka ndi mtima wao wachigololo wolekana ndi Ine, ndi maso ao achigololo akutsata mafano ao; ndipo iwo adzakhala onyansa pamaso pao pa iwo eni, chifukwa cha zoipa anazichita m’zonyansa zao zonse.
10 Ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, sindinanene chabe kuti ndidzawachitira choipa ichi.
11 Atero Yehova Mulungu, Omba manja ako, ponda ndi phazi lako, nuti, Kalanga ine, chifukwa cha zonyansa zoipa zonse za nyumba ya Israele; pakuti adzagwa ndi lupanga, ndi njala, ndi mliri.
12 Wokhala kutali adzafa ndi mliri, wokhala pafupi adzagwa ndi lupanga; koma wotsala ndi kuzingidwa adzafa ndi njala; momwemo ndidzawakwaniritsira ukali wanga.
13 Ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pokhala ophedwa ao pakati pa mafano ao, pozinga maguwa ao a nsembe, pa zitunda zonse zazitali, pamwamba pa mapiri onse, ndi patsinde pa mitengo yogudira yonse, ndi patsinde pa thundu aliyense wagudugudu, pomwe adapereka zonunkhira zokoma kwa mafano ao onse.
14 Ndipo ndidzawatambasulira dzanja langa, ndi kulisandutsa dziko bwinja ndi lopasuka, koposa chipululu cha ku Ribula mokhalamo iwo monse; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/6-82040e3b617ac479a72203a6dcf6a05b.mp3?version_id=1068—