Categories
EZEKIELE

EZEKIELE 5

1 Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, udzitengere mpeni wakuthwa, ndiwo lumo la wometa, udzitengere ndi kulipititsa pamutu pako ndi pa ndevu zako; nudzitengere muyeso kuyesa nao, ndi kugawa tsitsilo.

2 Limodzi la magawo ake atatu utenthe ndi moto pakati pa mzinda pakutha masiku a kuzingidwa mzinda, nutenge gawo lina ndi kukwapulakwapula ndi lupanga pozungulira pake, nuwaze kumphepo gawo lotsala; pakuti ndidzasolola lupanga lakuwatsata.

3 Utengekonso owerengeka ndi kuwamanga m’mkawo wa malaya ako.

4 Nutengekonso pa amenewa ndi kuwaponya pakati pa moto, ndi kuwatentha m’moto; kuchokera kumeneko udzatuluka moto pa nyumba yonse ya Israele.

Aneneratu za kupasuka kwa Yerusalemu

5 Atero Yehova Mulungu, Uwu ndi Yerusalemu ndinauika pakati paamitundu, ndi pozungulira pake pali maiko.

6 Koma anakaniza maweruzo anga ndi kuchita zoipa koposa amitundu, nakaniza malemba anga koposa maiko akuzungulira; pakuti anataya maweruzo anga, ndi malemba anga, sanayendemo.

7 Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Popeza kupokosera kwanu kwaposa kwa amitundu akukuzingani, ndipo simunayende m’malemba anga, kapena kuchita maweruzo anga, ngakhale maweruzo a amitundu akukuzingani simunawachite;

8 chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Taona ndidzatsutsana nawe Inedi, ndi kuchita maweruzo pakati pako pamaso pa amitundu.

9 Ndipo ndidzachita mwa iwe chimene sindinachichite ndi kale lonse, ndi kusadzachitanso momwemo, chifukwa cha zonyansa zako zonse.

10 Chifukwa chake atate adzadya ana pakati pako, ndi ana adzadya atate ao; ndipo ndidzachita maweruzo mwa iwe, ndi akutsala onse ndidzawabalalitsa kumphepo zonse.

11 M’mwemo, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, popeza wadetsa malo anga opatulika ndi zonyansa zako zonse ndi zoipsa zako zonse, ndidzakuchepsa; diso langa silidzalekerera, ndi Inenso sindidzachita chifundo.

12 Limodzi la magawo atatu la iwe lidzafa ndi mliri, nilidzatha ndi njala pakati pa iwe; ndi limodzi lidzagwa ndi lupanga pozinga pako; ndi limodzi ndidzalibalalikitsa kumphepo zonse, ndi kuwasololera lupanga lakuwatsata.

13 Motero mkwiyo wanga udzakwaniridwa, ndipo ndidzakhutitsa ukali wanga pa iwo, ndi kudzitonthoza; ndipo adzadziwa kuti Ine Yehova ndinanena m’changu changa, pokwaniridwa nao ukali wanga.

14 Ndidzakuikanso ukhale bwinja ndi chotonza pakati pa amitundu akukuzinga, pamaso pa onse akupitirirapo.

15 Momwemo chidzakhala chotonza ndi mnyozo, chilangizo ndi chodabwitsa kwa amitundu akukuzinga, pamene ndikuchitira maweruzo mu mkwiyo ndi ukali ndi madzudzulo aukali; Ine Yehova ndanena.

16 Pakuwatumizira Ine mivi yoipa ya njala yakuononga, imene ndidzatumiza kukuonongani, pamenepo ndidzakukuzirani njala, ndi kukuthyolerani mchirikizo, ndiwo chakudya.

17 Inde ndidzakutumizirani njala ndi zilombo, ndipo zidzakusowetsa ana ako; ndi mliri ndi mwazi zidzakugwera; ndidzakufikitsiranso lupanga; Ine Yehova ndachinena.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/5-5d4cb66c79e4f5f42467e2d46b52df7d.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *