Categories
EZEKIELE

EZEKIELE 43

Kukonzekanso kwa Kachisi: ulemerero wa Mulungu

1 Pamenepo anamuka nane kuchipata choloza kum’mawa,

2 ndipo taonani, ulemerero wa Mulungu wa Israele unadzera njira ya kum’mawa, ndi mau ake ananga mkokomo wa madzi ambiri, ndi dziko linanyezimira ndi ulemerero wake.

3 Ndipo maonekedwe a masomphenya ndinawaona anali monga masomphenya aja ndinawaona pakudza ine kupasula mzinda; ndi masomphenyawa anali ngati masomphenya aja ndinawaona kumtsinje wa Kebara; ndipo ndinagwa nkhope pansi.

4 Ndipo ulemerero wa Yehova unalowa mu Kachisi kudzera njira ya chipata choloza kum’mawa.

5 Ndipo mzimu unandinyamula numuka nane kubwalo la m’kati; ndipo taonani, ulemerero wa Yehova unadzaza Kachisi.

6 Ndipo ndinamva wina alikulankhula nane ali mu Kachisi, naima nane munthu.

7 Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, pano mpokhala mpando wachifumu wanga, mpoponda kumapazi anga, pomwe ndidzakhala pakati pa ana a Israele kosatha; ndi nyumba ya Israele siidzadetsanso dzina langa loyera, ngakhale iwo kapena mafumu ao, mwa chigololo chao, ndi mitembo ya mafumu ao pa misanje yao,

8 ndi kuika chiundo chao pafupi pa chiundo changa, ndi mphuthu yao pa mbali ya mphuthu yanga, ndipo panali khoma lokha pakati pa iwo ndi Ine, nadetsa dzina langa loyera ndi zonyansa zao anazichita; chifukwa chake ndinawatha mu mkwiyo wanga.

9 Ataye tsono chigololo chao ndi mitembo ya mafumu ao kutali kwa Ine, ndipo ndidzakhala pakati pao kosatha.

10 Wobadwa ndi munthu iwe, onetsa nyumba ya Israele Kachisiyu, kuti achite manyazi ndi mphulupulu zao; ndipo ayese muyeso wake.

11 Ndipo ngati akachita manyazi nazo zonse anazichita, uwadziwitse maonekedwe a Kachisiyu, ndi muyeso wake, ndi potulukira pake, ndi polowera pake, ndi malongosoledwe ake onse, ndi malemba ake onse, ngakhale maonekedwe ake onse, ndi malamulo ake onse; nuwalembere pamaso pao, kuti asunge maonekedwe ake onse, ndi malemba ake onse, nawachite.

12 Lamulo la Kachisi ndi ili: pamwamba paphiri malire ake onse pozungulira pake azikhala opatulika kwambiri. Taonani, limeneli ndi lamulo la Kachisi.

13 Ndipo miyeso ya guwa la nsembe, kuyesa mikono ndi iyi: (mkonowo ndiwo mkono ndi chikhato), tsinde lake likhale mkono, ndi kupingasa kwake dzanja limodzi, ndi mkuzi wake m’mphepete mwake pozungulira pake kuyesa zala; ili ndi tsinde la guwali.

14 Ndi kuyambira kunsi kwake kunthaka, kufikira phaka lamunsi, mikono iwiri; ndi kupingasa kwake mkono umodzi; ndi kuyambira phaka laling’ono kufikira phaka lalikulu mikono inai; ndi kupingasa kwake mkono.

15 Ndi guwa lapamwamba mikono inai; ndi pamoto paguwa padzatuluka nyanga zinai.

16 Ndi pamoto paguwa, m’litali mwake mikono khumi ndi iwiri, ndi kupingasa kwake khumi ndi iwiri, laphwamphwa mbali zake zinai.

17 Ndi phaka, m’litali mwake mikono khumi ndi inai, ndi kupingasa kwake mikono khumi ndi inai kumbali zake zinai; ndi mkuzi wake pozungulira pake mkono wa nusu, ndi tsinde lake mkono pozungulira pake, ndi makwerero ake aloza kum’mawa.

18 Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, atero Ambuye Yehova, Malemba a guwa la nsembe, tsiku lakulimanga, kuperekapo nsembe zopsereza, ndi kuwazapo mwazi, ndi awa;

19 Upatse ansembe Alevi, a mbeu za Zadoki, okhala pafupi ndi Ine, kunditumikira Ine, ati Ambuye Yehova, mwanawang’ombe, akhale wa nsembe yauchimo.

20 Nutengeko mwazi wake, ndi kupaka pa nyanga zinai za guwa, ndi pangodya zinai za phaka, ndi pa mkuzi wake pozungulira; motero uliyeretse ndi kulichitira chotetezera.

21 Utengenso ng’ombe ya nsembe yauchimo, aipsereze pamalo oikika a Kachisi kunja kwa malo opatulika.

22 Ndipo tsiku lachiwiri upereke tonde wopanda chilema, akhale nsembe yauchimo; ndipo ayeretse guwa la nsembe monga umo analiyeretsera ndi ng’ombeyo.

23 Utatha kuliyeretsa upereke mwanawang’ombe wopanda chilema, ndi nkhosa yamphongo ya zoweta yopanda chilema.

24 Ndipo ubwere nazo kwa Yehova, ndi ansembe athirepo mchere, ndi kuzipereka nsembe yopsereza ya Yehova.

25 Masiku asanu ndi awiri uzikonzera mbuzi tsiku ndi tsiku, ikhale nsembe yauchimo; akonzerenso mwanawang’ombe, ndi nkhosa yamphongo ya zoweta zopanda chilema.

26 Masiku asanu ndi awiri achite chotetezera guwali ndi kuliyeretsa, momwemo alipatule.

27 Ndipo atatsiriza masiku, kudzachitika tsiku lachisanu ndi chitatu ndi m’tsogolo, ansembe azichita nsembe zanu zopsereza, ndi nsembe zanu zoyamika paguwalo; ndipo ndidzakulandirani, ati Ambuye Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/43-e77b8c498a090a08716e1505fe587e3d.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *