Aneneratu za mapiri a Israele
1 Ndipo iwe, wobadwa ndi munthu, unenere kwa mapiri a Israele, uziti, Mapiri a Israele inu, imvani mau a Yehova.
2 Atero Ambuye Yehova, Popeza mdani ananena za inu, Ha! Ingakhale misanje yakale ili yathu, cholowa chathu;
3 chifukwa chake unenere, nuti, Atero Ambuye Yehova, Chifukwa, inde chifukwa kuti anakupasulani, nakumemezani pozungulira ponse, kuti mukhale cholowa chaamitunduotsala, ndipo mwafika pa milomo ya akazitape, ndi pa mbiri yoipa ya anthu;
4 chifukwa chake, mapiri inu a Israele, imvani mau a Ambuye Yehova. Atero Ambuye Yehova kunena ndi mapiri, ndi zitunda, ndi mitsinje, ndi zigwa, ndi zipululu zopasuka, ndi mizinda yamabwinja, imene yakhala chakudya ndi choseketsa amitundu otsala akuzungulira;
5 chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Zoonadi pa nsanje yanga yodya nayo moto ndinanena motsutsana nao amitundu otsala, ndi Edomu yense, amene anadzipatsira dziko langa likhale cholowa chao ndi chimwemwe cha mtima wonse, ndi mtima wopeputsa, kuti alande zake zonse zikhale zofunkha.
6 Chifukwa chake unenere za dziko la Israele, nuti kwa mapiri ndi kwa zitunda, kwa mitsinje ndi kwa zigwa, Atero Ambuye Yehova, Taonani, ndalankhula mu nsanje yanga ndi ukali wanga, popeza mwasenza manyazi a amitundu;
7 chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Ndakweza dzanja langa Ine, ndi kuti, Zedi amitundu akuzungulira inu adzasenza manyazi ao.
8 Koma inu, mapiri a Israele, mudzaphukitsa nthambi zanu, ndi kubalira anthu anga Israele zipatso zanu, pakuti ayandikira kufika.
9 Pakuti taonani, Ine ndikhalira nanu kumodzi, ndipo ndidzakutembenukirani; ndipo mudzabzalidwa ndi kupaliridwa,
10 ndipo ndidzakuchulukitsirani anthu nyumba yonse ya Israele, yonseyi, ndi m’mizindamo mudzakhala anthu, ndi kumabwinja kudzamangidwa mizinda.
11 Ndipo ndidzakuchulukitsirani anthu ndi nyama; ndipo adzachuluka, nadzabalana; ndipo ndidzakhalitsa anthu pa inu, monga umo anakhalira kale, ndipo ndidzachitira inu zabwino koposa poyamba paja; motero mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
12 Ndipo ndidzayendetsa anthu pa inu, ndiwo anthu anga Israele; adzakhala nawe dziko laolao, ndipo udzakhala cholowa chao osafetsanso ana ao.
13 Atero Ambuye Yehova, Popeza akuti nawe, Dzikowe ukudya anthu, nuyesa anthu ako afedwa;
14 chifukwa chake sudzadyanso anthu, kapena kuyesanso a mtundu wako afedwa, ati Ambuye Yehova.
15 Ndipo sindidzakumvetsanso za manyazi a amitundu, ndipo sudzasenzanso mtonzo wa mitundu ya anthu, kapena kukhumudwitsanso anthu ako, ati Ambuye Yehova.
Za kukonzekanso kwa Israele
16 Mau a Yehova anandidzeranso, ndi kuti,
17 Wobadwa ndi munthu iwe, muja a nyumba ya Israele anakhala m’dziko mwao, analidetsa ndi njira yao, ndi machitidwe ao; njira yao pamaso panga inanga chidetso cha mkazi amene akusamba.
18 M’mwemo ndinawatsanulira ukali wanga, chifukwa cha mwazi anautsanulira padziko, ndi chifukwa cha mafano analidetsa nalo dziko;
19 ndipo ndinawabalalitsa mwa amitundu, namwazika m’maiko monga mwa njira yao; ndi monga mwa machitidwe ao ndinawaweruza.
20 Ndipo pofika iwo kwa amitundu kumene anamukako, anadetsa dzina langa loyera; popeza anthu ananena za iwowa, Awa ndi anthu a Yehova, natuluka m’dziko mwake.
21 Koma ndinawaleka chifukwa cha dzina langa loyera, limene a nyumba ya Israele adalidetsa pakati pa amitundu, kumene adankako.
22 Chifukwa chake nena kwa nyumba ya Israele, Atero Ambuye Yehova, Sindichichita ichi chifukwa cha inu, nyumba ya Israele, koma chifukwa cha dzina langa loyera munaliipsalo pakati pa amitundu, kumene mudamukako.
23 Ndipo ndidzazindikiritsa dzina langa lalikulu kuti lili loyera, limene laipitsidwa mwa amitundu, limene inu munaliipsa pakati pao; ndipo amitundu adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ati Ambuye Yehova, pozindikiridwa Ine woyera mwa inu pamaso pao.
24 Pakuti ndidzakutengani kukutulutsani kwa amitundu, ndi kukusokolotsani m’maiko onse, ndi kubwera nanu m’dziko lanu.
25 Ndipo ndidzakuwazani madzi oyera, ndipo mudzakhala oyera; ndidzakuyeretsani kukuchotserani zodetsa zanu zonse, ndi mafano anu nonse.
26 Ndipo ndidzakupatsani mtima watsopano, ndi kulonga m’kati mwanu mzimu watsopano; ndipo ndidzachotsa mtima wamwala m’thupi, ndi kukupatsani mtima wamnofu.
27 Ndipo ndidzaika mzimu wanga m’kati mwanu, ndi kukuyendetsani m’malemba anga; ndipo mudzasunga maweruzo anga ndi kuwachita.
28 Ndipo mudzakhala m’dziko ndinapatsa makolo anulo, ndipo mudzakhala anthu anga, ndi Ine ndidzakhala Mulungu wanu.
29 Ndipo ndidzakupulumutsani kwa zodetsa zanu zonse, ndidzaitananso tirigu ndi kumchulukitsa, osaikiranso inu njala.
30 Ndipo ndidzachulukitsa zobala za mitengo, ndi zipatso za m’munda, kuti musalandirenso chitonzo cha njala mwa amitundu.
31 Pamenepo mudzakumbukira njira zanu zoipa, ndi zochita inu zimene sizinali zabwino; ndipo mudzanyansidwa nokha pamaso panu, chifukwa cha mphulupulu zanu ndi zonyansa zanu.
32 Dziwani kuti sindichita ichi chifukwa cha inu, ati Ambuye Yehova; chitani manyazi, dodomani, chifukwa cha njira zanu, nyumba ya Israele inu.
33 Atero Ambuye Yehova, Tsiku loti ndikuyeretsani kukuchotserani mphulupulu zanu zonse, ndidzakhalitsa anthu m’mizindamo; ndi pamabwinja padzamangidwa.
34 Ndi dziko lachipululu lidzalimidwa, chinkana linali lachipululu pamaso pa onse opitako.
35 Ndipo adzati, Dziko ili lachipululu lasanduka ngati munda wa Edeni ndi mizinda yamabwinja, ndi yachipululu, ndi yopasuka, yamangidwa malinga, muli anthu m’mwemo.
36 Pamenepo amitundu otsala pozungulira panu adzadziwa kuti Ine Yehova ndamanga malo opasuka, ndi kubzala pamene panali chipululu; Ine Yehova ndanena ndidzachita.
37 Atero Ambuye Yehova, Ichi chomwe adzandipempha a nyumba ya Israele ndiwachitire ichi, ndidzawachulukitsira anthu ngati nkhosa.
38 Ngati nkhosa za nsembe, ngati nkhosa za kuYerusalemupa zikondwerero zake zoikika, momwemo mizinda yamabwinja idzadzala nao magulu a anthu; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/36-7985bfadcc97b0fed2f108aba39fd9b5.mp3?version_id=1068—