Aneneratu za kulangidwa kwa a kuphiri la Seiri
1 Nandidzeranso mau a Yehova, akuti,
2 Wobadwa ndi munthu iwe, Lozetsa nkhope yako kuphiri la Seiri, nulinenere molitsutsa;
3 nuti nalo, Atero Ambuye Yehova, Taona, ndiipidwa nawe phiri la Seiri, ndipo ndidzakutambasulira dzanja langa, ndi kukusanduliza lachipululu ndi lodabwitsa.
4 Ndidzapasula mizinda yako, nudzakhala lachipululu; ndipo udzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
5 Popeza uli nao udani wosatha, waperekanso ana a Israele kumphamvu ya lupanga m’nthawi ya tsoka lao, mu nthawi ya mphulupulu yotsiriza;
6 chifukwa chake, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, ndikukonzeratu uphedwe, ndi mwazi udzakulondola; popeza sunadane nao mwazi, mwazi udzakulondola.
7 Ndipo ndidzaika phiri la Seiri lodabwitsa ndi lachipululu, ndi kuononga pomwepo wopitapo ndi wobwerapo.
8 Ndipo ndidzadzaza mapiri ake ndi ophedwa ake pa zitunda zako, ndi m’zigwa zako, ndi m’mitsinje mwako monse; adzagwa ophedwa ndi lupanga.
9 Ndidzakusandutsa mabwinja osatha; ndi m’mizinda mwako simudzakhalanso anthu; motero mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
10 Popeza wanena, Mitundu iwiri iyi ya anthu ndi maiko awiri awa adzakhala anga, tidzakhala nao ngati cholowa chathu, angakhale Yehova anali komweko;
11 chifukwa chake, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, ndidzachita monga mwa mkwiyo wako, ndi monga mwa nsanje yako unachita nayo pa kukwiya nao iwe; ndipo ndidzadziwika nao pamene ndikuweruza.
12 Ndipo udzadziwa kuti Ine Yehova ndidamva zamwano zako zonse udazinena pa mapiri a Israele, ndi kuti, Apasuka, apatsidwa kwa ife tiwadye.
13 Ndipo pakamwa panu mwadzikuza pa Ine, ndi kundichulukitsira mau anu ndawamva Ine.
14 Atero Ambuye Yehova, Pokondwerera dziko lonse ndidzakusanduliza lachipululu.
15 Monga momwe unakondwerera cholowa cha nyumba ya Israele, popeza chidapasuka, momwemo ndidzakuchitira iwe; udzakhala wopasuka, phiri la Seiri iwe, ndi Edomu lonse lonseli; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/35-c078e1a6e3fed80ae2fdeec17b6b3a0a.mp3?version_id=1068—