Mau ena oneneratu za Farao
1 Ndipo kunali chaka chakhumi ndi chimodzi, mwezi wachitatu, tsiku loyamba la mwezi, anandidzera mau a Yehova, akuti,
2 Wobadwa ndi munthu iwe, nena kwaFaraomfumu ya Aejipito ndi aunyinji ake, Ufanana ndi yani mu ukulu wako?
3 Taona, Asiriya anali mkungudza wa ku Lebanoni ndi nthambi zokoma zovalira, wautali msinkhu, kunsonga kwake ndi kumitambo.
4 Madzi anaumeretsa, chigumula chinaukulitsa, mitsinje yake inayenda, nizungulira munda wake, nipititsa michera yake kumitengo yonse yakuthengoko.
5 Chifukwa chake msinkhu wake unaposa mitengo yonse yakuthengo, ndi nthambi zake zinachuluka, ndi nthawi zake zinatalika, chifukwa cha madzi ambiri pophuka uwu.
6 Mbalame zonse za m’mlengalenga zinamanga zisa zao pa nthambi zake, ndi pansi pa nthawi zake zinaswana nyama zonse zakuthengo, ndi pa mthunzi wake inakhala mitundu yonse yaikulu ya anthu.
7 M’mwemo unakoma mu ukulu wake, m’kutalika kwa nthawi zake, popeza muzu wake unakhala kumadzi ambiri.
8 Mikungudza ya m’munda wa Mulungu siinathe kuubisa, milombwa siinanga nthambi zake, mifula siinanga nthawi zake; m’munda wa Mulungu munalibe mtengo wofanana nao kukoma kwake.
9 Ndinaupanga wokoma ndi nthawi zake zochuluka; ndi mitengo yonse ya mu Edeni inali m’munda wa Mulungu inachita nao nsanje.
10 Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Popeza mtengowo unakuza msinkhu wake, nufikitsa nsonga yake kumitambo, nukwezeka mtima wake m’kukula kwake,
11 ndidzaupereka m’dzanja la wamphamvu waamitundu; iye adzachita naotu, Ine ndautaya mwa choipa chake.
12 Ndipo alendo oopsawo a amitundu anaulikhatu, nausiya; nthawi zake zidagwa pamapiri ndi m’zigwa zonse, ndi nthambi zake zinathyokera ku timitsinje tonse ta m’dziko; ndi mitundu yonse ya anthu a padziko lapansi inatsika kumthunzi wake, niusiya.
13 Pogwera pake padzakhala mbalame zonse za m’mlengalenga, ndi nyama zonse zakuthengo zidzakhala pa nthambi zake;
14 kuti mitengo iliyonse ya kumadzi isadzikuze chifukwa cha msinkhu wao, kapena kufikitsa nsonga zao pakati pa mitambo, ndi kuti amphamvu ao asaime m’kukula kwao, ndiwo onse akumwa madzi; pakuti onsewo aperekedwa kuimfa munsi mwake mwa dziko, pakati pa ana a anthu, pamodzi ndi iwo otsikira kumanda.
15 Atero Ambuye Yehova, Tsiku lija anatsikira kumanda ndinachititsa maliro, ndinamphimbira nyanja, ndinachepsa mitsinje yake, ndi madzi aakulu analetseka; ndipo ndinamdetsera Lebanoni, ndi mitengo yonse yakuthengo inafota chifukwa cha uwo.
16 Ndinagwedeza amitundu ndi phokoso la kugwa kwake, muja ndinagwetsera kumanda, pamodzi ndi iwo otsikira kumanda; ndi mitengo yonse ya ku Edeni yosankhika, ndi yokometsetsa ya ku Lebanoni, yonse yakumwa madzi, inasangalala munsi mwake mwa dziko lapansi.
17 Iwonso anatsika naye kumanda kwa iwo ophedwa ndi lupanga, ndiwo amene adakhala dzanja lake okhala mumthunzi mwake pakati pa amitundu.
18 Momwemo ufanana ndi yani mu ulemerero ndi ukulu pakati pa mitengo ya Edeni? Koma udzatsitsidwa pamodzi ndi mitengo ya Edeni m’munsi mwake mwa dziko lapansi, udzagona pakati pa osadulidwa, pamodzi ndi iwo ophedwa ndi lupanga. Uwu ndi Farao ndi aunyinji ake onse, ati Ambuye Yehova.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/31-0b2a1b3711d044216d55eadb23bb0f83.mp3?version_id=1068—