Fanizo la mphika wobwadamuka
1 Anandidzeranso mau a Yehova chaka chachisanu ndi chinai, mwezi wakhumi, tsiku lakhumi la mwezi, ndi kuti,
2 Wobadwa ndi munthu iwe, Udzilembere dzina la tsiku lomwe lino, mfumu ya ku Babiloni wayandikiraYerusalemutsiku lomwe lino.
3 Ndipo uphere nyumba yopandukayo fanizo, nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Tereka mphika; uutereke, nuthire madzi m’menemo.
4 Longamo pamodzi ziwalo zake, ziwalo zonse zokoma, mwendo wathako ndi wamwamba; uudzaze ndi mafupa osankhika.
5 Tengako choweta chosankhika, nuikire mafupa mulu wa nkhuni pansi; ubwadamuke, ndi mafupa ake omwe uwaphike m’mwemo.
6 Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Tsoka mzinda wokhetsa mwazi, mphika m’mene muli dzimbiri, losauchokera dzimbiri lake; uchotsemo chiwalochiwalo; sanaugwere maere.
7 Pakuti mwazi wake uli m’kati mwake anauika pathanthwe poyera, sanautsanulire panthaka kuukwirira ndi fumbi.
8 Pofuna kuutsa ukali, ndi kubwezera chilango, ndaika mwazi wake pathanthwe poyera, kuti usakwiririke.
9 Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Tsoka mzinda wokhetsa mwazi, ndidzakulitsa mulu wa nkhuni.
10 Zichuluke nkhuni, koleza moto, nyama ipse, uwiritse msuzi wake, ubwadamuke, ndi mafupa ake atibuke.
11 Pamenepo uukhazike pa makala ake opanda kanthu m’menemo, kuti utenthe, nuyake mkuwa wake; ndi kuti chodetsa chake chisungunuke m’mwemo, kuti dzimbiri lake lithe.
12 Ntchito ya mphika ndi yolemetsa, koma dzimbiri lake lalikulu siliuchokera, dzimbiri lake liyenera kumoto.
13 M’chodetsa chako muli dama, popeza ndinakuyeretsa; koma sunayeretsedwa, sudzayeretsedwanso kukuchotsera chodetsa chako, mpaka nditakwaniritsa ukali wanga pa iwe.
14 Ine Yehova ndachinena, chidzachitika; ndipo ndidzachichita, sindidzamasula, kapena kulekerera, kapena kuwaleka, monga mwa njira zako, ndi monga umo unachitira adzakuweruza iwe, ati Ambuye Yehova.
Kumwalira kwa mkazi wa Ezekiele kuli chizindikiro cha kwa Yuda
15 Mau a Yehova anandidzeranso, akuti,
16 Wobadwa ndi munthu iwe, taona, ndikuchotsera chokonda maso ako ndi chikomo, koma usamve chisoni, kapena kulira, kapena kudza misozi.
17 Usa moyo mosamveka, usalira wakufayo, dzimangire chilemba, nuvale nsapato kumapazi ako, usaphimbe milomo yako. Kapena kudya mkate wa anthu.
18 Ndipo nditalankhula ndi anthu m’mawa, madzulo ake mkazi wanga anamwalira; ndi m’mawa mwake ndinachita monga anandilamulira.
19 Nanena nane anthu, Simudzatiuza kodi zitani nafe izi muzichita?
20 Ndipo ndinanena nao, Anandidzera mau a Yehova, akuti,
21 Nena ndi nyumba ya Israele, Atero Ambuye Yehova, Taona, ndidzadetsa malo anga opatulika, ulemerero wa mphamvu yanu, chokonda m’maso mwanu, chimene moyo wanu ali nacho chifundo; ndipo ana anu aamuna ndi aakazi otsalira inu adzagwa ndi lupanga.
22 Ndipo mudzachita monga umo ndachitira ine, osaphimba milomo yanu, kapena kudya mkate wa anthu.
23 Ndi zilemba zanu zidzakhala pamitu panu, ndi nsapato zanu kumapazi anu, simudzachita chisoni kapena kulira, koma mudzaonda ndi mphulupulu zanu, ndi kubulirana wina ndi mnzake.
24 Momwemo Ezekiele adzakhala kwa inu chizindikiro; umo monse anachitira iye mudzachita ndinu; chikadza ichi mudzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.
25 Ndipo wobadwa ndi munthu iwe, sikudzakhala kodi tsiku loti ndiwachotsera mphamvu yao, chimwemwe chao chopambana, chowakonda m’maso mwao, ndi chokhumbitsa mtima wao, ana ao aamuna ndi aakazi,
26 kuti tsiku lomwelo wopulumukayo adzakudzera, kukumvetsa m’makutu mwako?
27 Tsiku lomwelo pakamwa pako padzatsegukira wopulumukayo; mudzalankhula osakhalanso chete, momwemo udzawakhalira chizindikiro; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/24-2b20ed4fd402c04b53702f660891531d.mp3?version_id=1068—