Fanizo la mkango waukazi, ndi la mpesa
1 Ndipo iwe, takwezera akalonga a Israele nyimbo ya maliro,
2 uziti, Mai wako ndi chiyani? Mkango waukazi unabwanthama mwa mikango, unalera ana ake pakati pa misona.
3 Ndipo unalera mmodzi wa ana ake, iye nasanduka msona, unaphunzira kugwira nyama, unalusira anthu.
4 Mitundu ya anthu idamva mbiri yake, unagwidwa m’mbuna mwao; ndipo anadza nao ndi zokowera kudziko la Ejipito.
5 Pakuona tsono waukaziwo, kuti unalindirira, ndi kuti chiyembekezo chake chidatha, unatenga wina wa ana ake, numsandutsa msona.
6 Ndipo unayendayenda pakati pa mikango, nukhala msona, nuphunzira kugwira nyama, nulusira anthu.
7 Ndipo unadziwa amasiye ao, nupasula mizinda yao, ndipo dziko ndi kudzala kwake linasanduka labwinja, chifukwa cha phokoso la kubangula kwake.
8 Pamenepo mitundu ya anthu inadzipereka kuukola kuchokera kumaiko a kumbali zonse, niuphimba ndi ukonde wao, nugwidwa uwu m’mbuna mwao.
9 Nauika m’chitatanga ndi zokowera, nadza nao kwa mfumu ya ku Babiloni; anaulonga m’malinga, kuti mau ake asamvekenso pa mapiri a Israele.
10 Mai wako ananga mpesa wookedwa kumadzi; muja anakhala mumtendere unabala zipatso, wodzala ndi nthambi, chifukwa cha madzi ambiri.
11 Ndipo unali nazo ndodo zolimba zikhale ndodo zachifumu, za ochita ufumu, ndi msinkhu wao unakula kufikira kumitambo, ndipo zinaoneka m’kusomphoka kwao pakati pa nthambi zake zambiri.
12 Koma unazulidwa mwaukali, unaponyedwa pansi ndi mphepo ya kum’mawa, inaumitsa zipatso zake, ndodo zake zolimba zinathyoka ndi kuuma, moto unazitha.
13 Ndipo tsopano waokedwa m’chipululu m’dziko louma ndi la ludzu.
14 Unatulukanso moto kundodo za kunthambi zake, unatha zipatso zake; m’mwemo ulibe ndodo yolimba ikhale ndodo yachifumu ya kuchita ufumu. Iyi ndi nyimbo idzakhala nyimbo ya maliro.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/19-13f826a7a8eed27f6f6df022ee53cead.mp3?version_id=1068—