Chiweruzo cha Mulungu pa mafumu a Ayuda
1 Pamenepo unandikweza mzimu, nudza nane kuchipata cha kum’mawa cha nyumba ya Yehova choloza kum’mawa; ndipo taonani, pa chitseko cha chipata amuna makumi awiri mphambu asanu; ndipo ndinaona pakati pao Yazaniya mwana wa Azuri ndi Pelatiya mwana wa Benaya, akalonga a anthu.
2 Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, awa ndi anthu olingirira za mphulupulu, ndi kupangira uphungu woipa m’mzinda muno;
3 ndiwo akuti, siinafike nyengo yakumanga nyumba; mzinda uwu ndi mphika, ife ndife nyama.
4 Chifukwa chake uwanenere, neneratu, wobadwa ndi munthu iwe.
5 Pamenepo mzimu wa Yehova unandigwera, ndipo anati kwa ine, Nena, Atero Yehova, Mwatero nyumba ya Israele, pakuti ndidziwa zimene zimalowa m’mtima mwanu.
6 Mwachulukitsa ophedwa anu m’mzinda muno, mwadzazanso makwalala ake ndi ophedwawo.
7 Chifukwa chake atero Yehova Mulungu, Ophedwa anu munawaika m’kati mwake, iwo ndiwo nyama imene, ndi mzinda uwu ndiwo mphika; koma inu mudzatulutsidwa m’kati mwake.
8 Mwaopa lupanga, tsono ndidzakufikitsirani lupanga, ati Yehova Mulungu.
9 Ndipo ndidzakutulutsani m’kati mwake, ndi kukuperekani m’manja a alendo, ndi kuchita maweruzo pakati panu.
10 Mudzagwa ndi lupanga, ndidzakuweruzirani kumalire a Israele; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
11 Mzinda uno sudzakhala mphika wanu, ndi inu simudzakhala nyama m’kati mwake, ndidzakuweruzirani kumalire a Israele;
12 ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pakuti simunayende m’malemba anga, kapena kuchita maweruzo anga, koma mwachita monga mwa maweruzo aamitunduokhala pozungulira panu.
13 Ndipo kunali, pakunenera ine, anamwalira Pelatiya mwana wa Benaya. Pamenepo ndinagwa nkhope yanga pansi, ndi kufuula ndi mau aakulu, ndi kuti, Kalanga ine, Yehova Mulungu? Mudzatsiriza kodi otsala a Israele?
14 Ndipo mau a Yehova anandidzera kuti,
15 Wobadwa ndi munthu iwe, abale ako, inde abale ako aamuna a chibale chako, ndi nyumba yonse ya Israele, yonseyi ndiwo amene okhala muYerusalemuananena nao, Muzikhala kutali kwa Yehova; dziko ili lapatsidwa kwa ife, likhale cholowa chathu;
16 chifukwa chake uziti, Atero Yehova Mulungu, Ngakhale ndawachotsa kutali mwa amitundu, ngakhalenso ndawabalalikitsa m’maiko, koma ndidzawakhalira malo opatulika kanthawi kumaiko adafikako.
17 Chifukwa chake uziti, Atero Yehova Mulungu, Ndidzakumemezani kumitundu ya anthu, ndi kukusonkhanitsani muchoke m’maiko m’mene munabalalikiramo, ndipo ndidzakuninkhani dziko la Israele.
18 Ndipo adzafikako, nadzachotsako zonyansa zake zonse, ndi zake zonse zakuipitsamo.
19 Ndipo ndidzawapatsa mtima umodzi, ndi kuika mzimu watsopano m’kati mwao; ndipo ndidzawachotsera mtima wamwala m’thupi mwao, ndi kuwapatsa mtima wamnofu;
20 kuti ayende m’malemba anga, ndi kusunga maweruzo anga, ndi kuwachita; ndipo adzakhala anthu anga, ndi Ine ndidzakhala Mulungu wao.
21 Koma iwo amene mtima wao unatsata mtima wa zonyansa zao, ndi zoipitsitsa zao, ndidzawabwezera njira yao pamutu pao, ati Yehova Mulungu.
22 Pamenepoakerubianatambasula mapiko ao, ndi njinga zinali pa mbali pao; ndi ulemerero wa Mulungu wa Israele unali pamwamba pao.
23 Ndipo ulemerero wa Yehova unakwera kuchoka pakati pa mzinda, nuima paphiri la kum’mawa kwa mzinda.
24 Ndipo mzimu unandikweza, nufika nane m’masomphenya mwa mzimu wa Mulungu kudziko la Ababiloni, kwa andendewo. M’mwemo masomphenya ndidawaona anandichokera, nakwera.
25 Pamenepo ndinanena ndi andendewo zonse zija adandionetsa Yehova.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/11-cbb910feacce70f66beedaa88604a47b.mp3?version_id=1068—