Categories
EZEKIELE

EZEKIELE 1

Masomphenya a Ezekiele

1 Ndipo kunali chaka cha makumi atatu, mwezi wachinai, tsiku lachisanu la mwezi, pokhala ine pakati pa andende kumtsinje Kebara, kunatseguka kumwamba, ndipo ndinaona masomphenya a Mulungu.

2 Tsiku lachisanu la mwezi, ndicho chaka chachisanu cha kutengedwa ndende mfumu Yehoyakini,

3 anadzadi mau a Yehova kwa Ezekiele wansembe, mwana wa Buzi, m’dziko la Ababiloni kumtsinje Kebara; ndi pomwepo dzanja la Yehova lidamkhalira.

4 Ndinapenya, ndipo taonani, mkuntho wa mphepo wochokera kumpoto, mtambo waukulu ndi moto wofukusika m’mwemo, ndi pozungulira pake padachita cheza, ndi m’kati mwake mudaoneka ngati chitsulo chakupsa m’kati mwa moto.

5 Ndi m’kati mwake mudaoneka mafaniziro a zamoyo zinai. Ndipo maonekedwe ao ndiwo anafanana ndi munthu,

6 ndi yense anali nazo nkhope zinai, ndi yense wa iwo anali nao mapiko anai.

7 Ndi mapazi ao anali mapazi oongoka, ndi kumapazi ao kunanga kuphazi kwa mwanawang’ombe; ndipo ananyezimira ngati mawalidwe a mkuwa wowalitsidwa.

8 Zinali naonso manja a munthu pansi pa mapiko ao pa mbali zao zinai; ndipo zinaizi zinali nazo nkhope zao ndi mapiko ao.

9 Mapiko ao analumikizana; sizinatembenuke poyenda; chilichonse chinayenda ndi kulunjika kutsogoloko.

10 Mafaniziro a nkhope zao zinali nayo nkhope ya munthu; ndi izi zinai zinali nayo nkhope ya mkango pa mbali ya kudzanja lamanja; ndi izi zinai zinali nayo nkhope ya ng’ombe pa mbali ya kudzanja lamanzere; izi zinai zinali nayonso nkhope ya chiombankhanga.

11 Ndi nkhope zao ndi mapiko ao zinagawikana kumutu; chilichonse chinali nao mapiko awiri olumikizana, ndi awiri anaphimba thupi.

12 Ndipo zinayenda, chilichonse chinalunjika kutsogolo kwake uko mzimu unafuna kumukako zinamuka, sizinatembenuke poyenda.

13 Kunena za mafaniziro a zamoyozo, maonekedwe ao ananga makala amoto, monga maonekedwe a miyuni; motowo unayendayenda pakati pa zamoyozo, ndi motowo unachita cheza, ndi m’motomo mudatuluka mphezi.

14 Ndipo zamoyozo zinathamanga ndi kubwerera, ngati maonekedwe a mphezi yong’anima.

15 Ndipo pakupenyerera ine zamoyozo, taonani, njinga imodziimodzi yoponda pansi pafupi ndi zamoyozo pa nkhope zao zinai.

16 Maonekedwe a njingazi ndi mapangidwe ao ananga mawalidwe a berulo; ndi izi zinai zinafanana mafaniziro ao; ndi maonekedwe ao ndi mapangidwe ao anali ngati njinga ziwiri zopingasitsana.

17 Poyenda zinayenda kumbali zao zinai, zosatembenuka poyenda.

18 Ndi mikombero yake inali yokuzika ndi yoopsa; ndi izi zinai zinali ndi mikombero yao yodzala ndi maso pozungulira pao.

19 Ndipo poyenda zamoyozo, njingazi zinayenda pambali pao; ndipo ponyamuka pansi zamoyozo, njinga zinanyamuka.

20 Kuli konse mzimu ukuti umuke, zinamuka komwe mzimu ukuti umuke; ndi njingazi zinanyamuka pambali pa izi; pakuti mzimu wa zamoyozo unali m’njingazo.

21 Poyenda zija zinayenda izi, poima zija zinaima izo; ndipo ponyamuka pansi zija njingazi zinanyamuka pambali pa izi; pakuti mzimu wa zamoyozo unali mu njingazi.

22 Ndi pa mitu ya zamoyozi panali chifaniziro cha thambo, monga mawalidwe a krustalo woopsa, loyalika pamwamba pamitu pao.

23 Ndi pansi pathambolo mapiko ao analunjikana, lina kulunjika kulinzake; chilichonse chinali nao mapiko awiri akuphimba matupi ao, chakuno ndi chauko.

24 Ndipo pakuyenda izi ndinamva mkokomo wa mapiko ao, ngati mkokomo wa madzi aakulu, ngati mau a Wamphamvuyonse, phokoso lakusokosera ngati phokoso la ankhondo; pakuima zinagwetsa mapiko ao.

25 Ndipo panamveka mau pamwamba pathambolo linali pamwamba pa mitu yao; pakuima izi zinagwetsa mapiko ao.

26 Ndi pamwamba pathambolo linali pamitu pao panali chifaniziro cha mpando wachifumu, maonekedwe ake ngati mwala wa safiro; ndipo pa chifaniziro cha mpando wachifumu panali chifaniziro ngati maonekedwe ake a munthu wokhala pamwamba pake.

27 Ndipo ndinapenya ngati chitsulo chakupsa, ngati maonekedwe ake a moto m’kati mwake pozungulira pake, kuyambira maonekedwe a m’chuuno mwake ndi kumwamba kwake; ndipo kuyambira maonekedwe a m’chuuno mwake ndi kunsi kwake ndinaona ngati maonekedwe ake a moto; ndi kunyezimira kudamzinga.

28 Ngati maonekedwe a utawaleza uli m’mtambo tsiku la mvula, momwemo maonekedwe a kunyezimira kwake pozungulira pake. Ndiwo maonekedwe a chifaniziro cha ulemerero wa Yehova. Ndipo pakuchipenya ndinagwa nkhope pansi, ndipo ndinamva mau a wina wakunena.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZK/1-a870287340db53835ae59b76eaa34614.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *