Arita-kisereksesi atumiza Ezara ku Yerusalemu akonzenso chipembedzo cha Yehova
1 Zitatha izi tsono, pokhala mfumu Arita-kisereksesi mfumu ya Persiya, anadza Ezara mwana wa Seraya, mwana wa Azariya, mwana wa Hilikiya,
2 mwana wa Salumu, mwana wa Zadoki, mwana wa Ahitubi,
3 mwana wa Amariya, mwana wa Azariya, mwana wa Meraiyoti,
4 mwana wa Zerahiya, mwana wa Uzi, mwana wa Buki,
5 mwana wa Abisuwa mwana wa Finehasi, mwana wa Eleazara, mwana wa Aroni wansembe wamkulu.
6 Ezara amene anakwera kuchokera ku Babiloni, ndiye mlembi waluntha m’chilamulo cha Mose, chimene Yehova Mulungu wa Israele adachipereka; ndipo mfumu inampatsa chopempha iye chonse, monga linamkhalira dzanja la Yehova Mulungu wake.
7 Nakweranso kunka kuYerusalemuena a ana a Israele, ndi ansembe, ndi Alevi, ndi oimbira, ndi odikira, ndi antchito a m’kachisi, chaka chachisanu ndi chiwiri cha Arita-kisereksesi mfumu.
8 Ndipo iye anafika ku Yerusalemu mwezi wachisanu, ndicho chaka chachisanu ndi chiwiri cha mfumu.
9 Pakuti tsiku loyamba la mwezi woyamba, ndilo chiyambi cha ulendo wokwera kuchokera ku Babiloni, ndi tsiku loyamba la mwezi wachisanu anafika ku Yerusalemu, monga linamkhalira dzanja lokoma la Mulungu wake.
10 Pakuti Ezara adaikiratu mtima wake kuchifuna chilamulo cha Yehova, ndi kuchichita, ndi kuphunzitsa mu Israele malemba ndi maweruzo.
11 Malemba a kalatayo mfumu Arita-kisereksesi anampatsa Ezara wansembe mlembi, ndiye mlembi wa mau a malamulo a Yehova, ndi malemba ake kwa Israele, ndi awa:
12 Arita-kisereksesi mfumu ya mafumu kwa Ezara wansembe, mlembi wa lamulo la Mulungu wa Kumwamba, mtendere weniweni, ndi pa nthawi yakuti.
13 Ndilamulira kuti onse a ana a Israele, ndi ansembe ao, ndi Alevi, mu ufumu wanga, ofuna eni ake kumuka ku Yerusalemu, apite nawe.
14 Popeza utumidwa wochokera pamaso pa mfumu ndi aphungu ake asanu ndi awiri, kufunsira za Yuda ndi Yerusalemu monga mwa lamulo la Mulungu wako lili m’dzanja lako,
15 ndi kumuka nazosilivandi golide, zimene mfumu ndi aphungu ake, anapereka mwaufulu kwa Mulungu wa Israele, mokhala mwake muli mu Yerusalemu,
16 pamodzi ndi siliva ndi golide zilizonse ukazipeza m’dziko lonse la ku Babiloni, pamodzi ndi chopereka chaufulu cha anthu, ndi cha ansembe, akuperekera mwaufulu nyumba ya Mulungu wao ili ku Yerusalemu;
17 m’mwemo uzifulumira kugula ndi ndalama iyi ng’ombe, nkhosa zamphongo, anaankhosa, pamodzi ndi nsembe zao zaufa, ndi nsembe zao zothira; ndi kuzipereka paguwa la nsembe la nyumba ya Mulungu wanu yokhala ku Yerusalemu.
18 Ndipo chilichonse chidzakomera iwe ndi abale ako kuchita nazo siliva ndi golide zotsala, ichi muchite monga mwa chifuniro cha Mulungu wanu.
19 Ndipo zipangizozo akupatsa za utumiki wa nyumba ya Mulungu wako, uzipereka pamaso pa Mulungu wa ku Yerusalemu.
20 Ndi zina zotsala zakusowa nyumba ya Mulungu wako, zikayenera uzipereke, uzipereke zochokera kunyumba ya chuma cha mfumu.
21 Ndipo ine Arita-kisereksesi, mfumu ine, ndilamulira osunga chuma onse okhala tsidya lija la mtsinjewo, kuti chilichonse akupemphani Ezara wansembe, mlembi wa lamulo la Mulungu wa Kumwamba, chichitike mofulumira;
22 mpaka matalente a siliva zana limodzi, ndi miyeso ya tirigu zana limodzi, ndi mitsuko ya vinyo zana limodzi, ndi mitsuko ya mafuta zana limodzi, ndi mchere wosauwerenga.
23 Chilichonse Mulungu wa Kumwamba achilamulire chichitikire mwachangu nyumba ya Mulungu wa Kumwamba; pakuti padzakhaliranji mkwiyo pa ufumu wa mfumu ndi ana ake?
24 Tikudziwitsaninso kuti sikudzaloledwa kusonkhetsa aliyense wa ansembe, ndi Alevi, oimbira, odikira, antchito a m’kachisi, kapena antchito a nyumba iyi ya Mulungu msonkho, thangata, kapena msonkho wa panjira.
25 Ndipo iwe Ezara monga mwa nzeru za Mulungu wako ili m’dzanja lako, uike nduna, ndi oweruza milandu, aweruze anthu onse ali tsidya lija la mtsinje, onse akudziwa malamulo a Mulungu wako; ndi wosawadziwayo umphunzitse.
26 Ndipo aliyense wosachita lamulo la Mulungu wako, ndi lamulo la mfumu, mlandu umtsutse msanga, ngakhale kumupha, kapena kumpirikitsa m’dziko, kapena kumlanda chuma chake, kapena kummanga m’kaidi.
27 Wodala Yehova Mulungu wa makolo athu, amene anaika chinthu chotere mu mtima wa mfumu, kukometsera nyumba ya Yehova ili ku Yerusalemu,
28 nandifikitsira chifundo pamaso pa mfumu, ndi aphungu ake, ndi pamaso pa akalonga amphamvu onse a mfumu. Motero ndinalimbika mtima, monga umo dzanja la Yehova Mulungu wanga linakhala pa ine; ndipo ndinasonkhanitsa mwa Israele anthu omveka akwere nane limodzi.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZR/7-451eec82469f172e328a43118122e93a.mp3?version_id=1068—