Categories
ESTERE

ESTERE 8

Ahasuwero avomereza pempho la Estere, Ayuda napulumuka

1 Tsiku lomwelo mfumu Ahasuwero anampatsa mkazi wamkulu Estere nyumba ya Hamani mdani wa Ayuda. Nafika Mordekai pamaso pa mfumu; pakuti Estere adamuuza za chibale chake.

2 Ndipo mfumu inavula mphete yake adailanda kwa Hamani, naipereka kwa Mordekai. Ndi Estere anaika Mordekai akhale woyang’anira nyumba ya Hamani.

3 Nanenanso Estere pamaso pa mfumu, nagwa ku mapazi ake, nalira misozi, nampembedza kuti achotse choipacho cha Hamani wa ku Agagi, ndi chiwembu adachipangira Ayuda.

4 Ndipo mfumu inaloza Estere ndi ndodo yachifumu yagolide. Nanyamuka Estere, naima pamaso pa mfumu.

5 Nati, Chikakomera mfumu, ndipo ngati yandikomera mtima, ndi kumuyenera mfumu, ngatinso ndimchititsa kaso, alembe makalata kusintha mau a chiwembu cha Hamani mwana wa Hamedata wa ku Agagi, amene adawalembera kuononga Ayuda okhala m’maiko onse a mfumu;

6 pakuti ndidzapirira bwanji pakuchiona choipa chilikudzera a mtundu wanga, kapena ndidzapirira bwanji pakuchiona chionongeko cha fuko langa?

7 Pamenepo mfumu Ahasuwero anati kwa mkazi wamkulu Estere, ndi kwa Mordekai Myuda, Taonani, ndampatsa Estere nyumba ya Hamani, ndi iyeyu anampachika pamtanda, chifukwa anatulutsa dzanja lake pa Ayuda.

8 Mulembere inunso kwa Ayuda monga mufuna, m’dzina la mfumu, nimusindikize ndi mphete ya mfumu; pakuti kalata yolembedwa m’dzina la mfumu, ndi kusindikizika ndi mphete ya mfumu, palibe munthu akhoza kuyisintha.

9 Pamenepo anaitana alembi a mfumu nthawi yomweyo, mwezi wachitatu, ndiwo mwezi wa Sivani, tsiku lake la makumi awiri ndi chitatu, monga mwa zonse Mordekai analamulira; nalembera kwa Ayuda, ndi kwa akazembe, ndi ziwanga, ndi akalonga a kumaiko, oyambira ku Indiya, ofikira ku Kusi, maiko zana limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi awiri, ku dziko lililonse monga mwa chilembedwe chao, ndi mtundu uliwonse monga mwa chinenedwe chao, ndi kwa Ayuda monga mwa chinenedwe chao.

10 Ndipo analembera m’dzina la mfumu Ahasuwero, nasindikiza ndi mphete ya mfumu, natumiza makalata ndi amtokoma pa akavalo, okwera pa akavalo aliwiro achifumu, obadwa mosankhika;

11 m’menemo mfumu inalola Ayuda okhala mu mzinda uliwonse asonkhane, ndi kulimbikira moyo wao, kuononga, kupha, ndi kupulula mphamvu yonse ya anthu ndi ya dziko yofuna kuwathira nkhondo, iwo, ana ao aang’ono, ndi akazi ao, ndi kulanda zofunkha zao,

12 tsiku lomwelo, m’maiko onse a mfumu Ahasuwero, tsiku lakhumi ndi chitatu la mwezi wakhumi ndi chiwiri, ndiwo mwezi wa Adara.

13 Chitsanzo chake, cha lemboli, chakuti abukitse lamulo m’maiko onse, chinalalikidwa kwa mitundu yonse ya anthu, kuti, Ayuda akonzekeretu tsiku lijalo, kubwezera chilango adani ao.

14 Natuluka amtokoma okwera pa akavalo aliwiro achifumu; pakuti mau a mfumu anawafulumiza ndi kuwaumiriza; ndipo lamulolo linabukitsidwa m’chinyumba cha ku Susa.

15 Ndipo Mordekai anatuluka pamaso pa mfumu wovala chovala chachifumu chamadzi ndi choyera, ndi korona wamkulu wagolide, ndi malaya abafuta ndi ofiirira; ndi mzinda wa Susa unafuula ndi kukondwera.

16 Ayuda anali nako kuunika, ndi kukondwera, ndi chimwemwe, ndi ulemu.

17 Ndi m’maiko monse, ndi m’mizinda yonse, mudafika mau a mfumu ndi lamulo lake, Ayuda anali nako kukondwera ndi chimwemwe, madyerero ndi tsiku lokoma. Ndipo ambiri a mitundu ya anthu a m’dziko anasanduka Ayuda; pakuti kuopsa kwa Ayuda kudawagwera.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EST/8-9660cb13c0716d9bd2b13721bc40e932.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *