Categories
ESTERE

ESTERE 6

Ahasuwero aona chifukwa cha kuchitira Mordekai ulemu

1 Usiku uja tulo tidamwazikira mfumu, niti abwere nalo buku la mbiri, naliwerenga pamaso pa mfumu.

2 Napeza mudalembedwa kuti Mordekai adawulula za Bigitana ndi Teresi, awiri a adindo a mfumu osunga pakhomo, amene adayesa kumthira manja mfumu Ahasuwero.

3 Niti mfumu, Anamchitira Mordekai ulemu ndi ukulu wotani chifukwa cha ichi? Ndipo anyamata a mfumu akuitumikira ananena nayo, Sanamchitire kanthu.

4 Niti mfumu, Ali kubwalo ndani? Koma Hamani adalowa m’bwalo lakunja la nyumba ya mfumu kulankhula ndi mfumu za kupachika Mordekai pamtengo adaukonzeratu.

5 Ndipo anyamata a mfumu ananena nayo, Taonani, Hamani alikuima pabwalo. Niti mfumu, Alowe.

6 Nalowa Hamani. Ndipo mfumu inati kwa iye, Kodi amchitire chiyani munthu amene mfumu ikondwera kumchitira ulemu? Ndipo Hamani anati mumtima mwake, Ndaniyo mfumu ikondwera kumchitira ulemu koposa ine?

7 Nati Hamani kwa mfumu, Munthu amene mfumu ikondwera kumchitira ulemu,

8 amtengere chovala chachifumu amachivala mfumu, ndi kavalo amakwerapo mfumu, naike korona wachifumu pamutu pake,

9 napereke chovala ndi kavalo m’dzanja la wina womveketsa wa akalonga a mfumu, naveke nacho munthu amene mfumu ikondwera kumchitira ulemu, namuyendetse pa kavaloyo m’khwalala la m’mzinda, nafuule pamaso pake, Azitero naye munthu amene mfumu ikondwera kumchitira ulemu.

10 Pamenepo mfumu inati kwa Hamani, Fulumira, tenga chovala ndi kavalo monga umo wanenera, nuchitire chotero Mordekai Myudayo, wokhala pa chipata cha mfumu; kasasowepo kanthu ka zonse wazinena.

11 Ndipo Hamani anatenga chovala ndi kavalo, naveka Mordekai, namuyendetsa pa kavalo m’khwalala la m’mzinda, nafuula pamaso pake, Azitero naye munthu amene mfumu ikondwera kumchitira ulemu.

12 Ndipo Mordekai anabweranso kuchipata cha mfumu. Koma Hamani anafulumira kunka kwao, wachisoni ndi wofunda mutu wake.

13 Ndipo Hamani anafotokozera Zeresi mkazi wake, ndi mabwenzi ake onse, zonse zidamgwera. Nanena naye anzeru ake, ndi Zeresi mkazi wake, Mordekai amene wayamba kutsika pamaso pake, akakhala wa mbumba ya Ayuda, sudzamgonjetsa; koma udzagwada pamaso pake.

14 Akali chilankhulire naye, anafika adindo a mfumu, nafulumira kumtenga Hamani kunka naye kumadyerero adawakonzera Estere.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EST/6-27c76f2781e0383f3aede7a9a2152c0f.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *