Categories
ESTERE

ESTERE 2

Ahasuwero akwatira Estere

1 Zitatha izi, utaleka mkwiyo wa mfumu Ahasuwero, anakumbukira Vasiti, ndi chochita iye, ndi chomlamulidwira.

2 Pamenepo anyamata a mfumu omtumikira anati, Amfunire mfumu anamwali okongola;

3 ndi mfumu aike oyang’anira m’maiko onse a ufumu wake, kuti asonkhanitse anamwali onse okongola m’chinyumba cha ku Susa, m’nyumba ya akazi; awasunge Hegai mdindo wa mfumu wosungira akazi, nawapatse zowayeretsa;

4 ndi namwali womkonda mfumu akhale mkazi wamkulu m’malo mwa Vasiti. Ndipo chinthuchi chinamkonda mfumu, nachita chomwecho.

5 Panali Myuda m’chinyumba cha ku Susa, dzina lake ndiye Mordekai, mwana wa Yairi, mwana wa Simei, mwana wa Kisi Mbenjamini;

6 uyu anatengedwa ndende kuYerusalemu, pamodzi ndi andende anatengedwa pamodzi ndi Yekoniya mfumu ya Yuda, amene Nebukadinezara mfumu ya Babiloni adamtenga ndende.

7 Ndipo iye adalera Hadasa, ndiye Estere, mwana wamkazi wa atate wake wamng’ono; popeza iye analibe atate kapena amai; ndi namwaliyo anali wa maonekedwe okoma, ndi wokongola; ndipo atamwalira atate wake ndi mai wake, Mordekai anamtenga akhale mwana wake.

8 Ndipo kunali, atamveka mau a mfumu ndi lamulo lake, ndipo atasonkhanidwa anamwali ambiri m’chinyumba cha ku Susa, awasunge Hegai, anamtenga Estere yemwe, alowe m’nyumba ya mfumu, amsunge Hegai wosunga akazi.

9 Ndipo namwaliyo anamkomera, namchitira chifundo; ndipo anafulumira kumpatsa zake zomyeretsa, ndi magawo ake, ndi anamwali asanu ndi awiri oyenera kumpatsa ochokera m’nyumba ya mfumu; ndipo anamsuntha iye ndi anamwali ake akhale m’malo okometsetsa m’nyumba ya akazi.

10 Estere sadawulule mtundu wake ndi chibale chake; pakuti Mordekai adamuuzitsa kuti asadziwulule.

11 Ndi Mordekai akayendayenda tsiku ndi tsiku kubwalo la nyumba ya akazi, kuti adziwe umo akhalira Estere, ndi chimene chidzamchitikira.

12 Kunafika tsono kulowa kwake kwa namwali aliyense, kuti alowe kwa mfumu Ahasuwero, atamchitira monga mwa lamulo la akazi, miyezi khumi ndi iwiri; pakuti ankakwaniritsa masiku a mayeretsedwe ao motero, miyezi isanu ndi umodzi ndi mafuta amure, ndi miyezi isanu ndi umodzi ndi zonunkhira bwino, ndi zoyeretsa akazi.

13 Ndipo namwali aliyense analowa kwa mfumu motero, zilizonse anafuna anampatsa zochokera m’nyumba ya akazi, alowe nazo kunyumba ya mfumu.

14 Madzulo ake analowamo, nabwera m’mawa mwake kunka kunyumba yachiwiri ya akazi, amsunge Saasigazi mdindo wa mfumu, wosunga akazi aang’ono a mfumu; iyeyu sanalowenso kwa mfumu, koma akakondwera naye mfumu, ndi kumuitana kumtchula dzina lake, ndiko.

15 Pofika tsono kulowa kwake kwa Estere mwana wa Abihaili, atate wamng’ono wa Mordekai, amene adadzitengera akhale mwana wake, kuti alowe kwa mfumu, sanafune kanthu koma zonena Hegai mdindo wa mfumu wosunga akazi ndizo. Ndipo Estere anayamikizidwa pamaso pa onse ompenya.

16 Momwemo anatengedwa Estere kunka kwa mfumu Ahasuwero, kunyumba yake yachifumu, mwezi wakhumi, ndiwo mwezi wa Tebeti, chaka chachisanu ndi chiwiri cha ufumu wake.

17 Ndipo mfumu inakonda Estere koposa akazi onse, nalandira iye kuyanja ndi chifundo pamaso pake, koposa anamwali onse; motero anaika korona wachifumu pamutu pake, namuyesa mkazi wamkulu m’malo mwa Vasiti.

18 Pamenepo mfumu inawakonzera madyerero akulu ake onse, ndi omtumikira, ndiwo madyerero a Estere; napumulitsa maiko, naninkha zaufulu monga mwa ufulu wa mfumu.

19 Ndipo posonkhanidwa anamwali nthawi yachiwiri Mordekai anali wa m’bwalo la mfumu.

20 Estere sadawulule chibale chake kapena mtundu wake, monga Mordekai adamuuza; popeza Estere anachita mau a Mordekai monga m’mene analeredwa naye.

Mordekai awulula chiwembu chofuna kupha mfumu

21 Masiku awa pokhala Mordekai wa m’bwalo la mfumu, Bigitana ndi Teresi, adindo awiri a mfumu osunga pakhomo, anapsa mtima, nayesa kumthira manja mfumu Ahasuwero.

22 Koma chidadziwika ichi kwa Mordekai, ndiye anafotokozera Estere mkazi wamkulu; ndi Estere anamuuza mfumu, kumnenera Mordekai.

23 Ndipo atafunsira mlanduwo, anaupeza momwemo, napachikidwa onse awiri pamtengo; ndipo anachilemba m’buku la mbiri pamaso pa mfumu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EST/2-6467998a4abb2f90d80dbbdaafe464df.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *