Categories
EKSODO

EKSODO 7

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Taona, ndakuika ngati Mulungu kwaFarao; ndi Aroni mkulu wako adzakhala mneneri wako.

2 Iwe uzilankhula zonse ndikulamulira; ndi Aroni mkulu wako azilankhula kwa Farao, kuti alole ana a Israele atuluke m’dziko lake.

3 Koma Ine ndidzaumitsa mtima wake wa Farao, ndipo ndidzachulukitsa zizindikiro ndi zozizwa zanga m’dziko la Ejipito.

4 Koma Farao sadzamvera inu, ndipo ndidzaika dzanja langa pa Aejipito, ndipo ndidzatulutsa makamu anga, anthu anga ana a Israele, m’dziko la Ejipito ndi maweruzo aakulu.

5 Ndipo Aejipito adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pakutambasula Ine dzanja langa pa Aejipito, ndikutulutsa ana a Israele pakati pao.

6 Ndipo Mose ndi Aroni anachita monga Yehova anawalamulira, momwemo anachita.

7 Ndipo Mose anali nazo zaka makumi asanu ndi atatu, ndi Aroni anali nazo zaka makumi asanu ndi atatu kudza zitatu, pamene ananena ndi Farao.

Mose ndi amatsenga

8 Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, ndi kuti,

9 Pamene Farao adzalankhula nanu, ndi kuti, Dzichitireni chodabwitsa; pamenepo uzinena ndi Aroni, Tenga ndodo yako, iponye pansi pamaso pa Farao, isanduke chinjoka.

10 Ndipo Mose ndi Aroni analowa kwa Farao, nachita monga momwe Yehova adawalamulira; ndipo Aroni anaponya pansi ndodo yake pamaso pa Farao, ndi pamaso pa anyamata ake, ndipo inasanduka chinjoka.

11 Pamenepo Farao anaitananso anzeru, ndi amatsenga; ndipo alembi a Aejipito, iwonso anachita momwemo ndi matsenga ao.

12 Pakuti yense anaponya pansi ndodo yake, ndipo zinasanduka zinjoka; koma ndodo ya Aroni inameza ndodo zao.

13 Koma mtima wa Farao unalimba, ndipo sanamvere iwo; monga adalankhula Yehova.

Chozizwitsa choyamba: Madzi asanduka mwazi

14 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Walemera mtima wa Farao, akana kulola anthu apite.

15 Muka kwa Farao m’mawa; taona, atuluka kunka kumadzi; nuime kumlinda m’mbali mwa mtsinje; ndi ndodo idasanduka njokayo uigwire m’dzanja lako.

16 Ndipo ukanena naye, Yehova, Mulungu wa Ahebri anandituma kwa inu, ndi kuti, Lola anthu anga amuke kuti anditumikire m’chipululu; koma, taona, sunamvere ndi pano.

17 Atero Yehova, Ndi ichi udzadziwa kuti Ine ndine Yehova; taonani, ndidzapanda madzi ali m’mtsinje ndi ndodo ili m’dzanja langa, ndipo adzasanduka mwazi.

18 Ndi nsomba zili m’mtsinje zidzafa, ndi mtsinje idzanunkha; ndi Aejipito adzachita mtima useru ndi kumwa madzi a m’mtsinjemo.

19 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni, Tenga ndodo yako, nutambasule dzanja lako pamadzi a mu Ejipito, pa mitsinje yao, pa ngalande zao, ndi pa matamanda ao, ndi pa matawale ao onse amadzi, kuti asanduke mwazi; mukhale mwazi m’dziko lonse la Ejipito, m’zotengera zamtengo, ndi zamwala.

20 Ndipo Mose ndi Aroni anachita monga momwe Yehova adawalamulira; nasamula ndodo, napanda madzi ali m’mtsinjemo pamaso pa Farao, ndi pamaso pa anyamata ake; ndipo madzi onse a m’mtsinjemo anasanduka mwazi.

21 Ndi nsomba za m’mtsinjemo zinafa; ndi mtsinjewo unanunkha; ndipo Aejipito sanakhoze kumwa madzi a m’mtsinjemo; ndipo munali mwazi m’dziko lonse la Ejipito.

22 Ndipo alembi a Aejipito anachita momwemo ndi matsenga ao; koma mtima wa Farao unalimba, ndipo sanamvere iwo; monga adalankhula Yehova.

23 Ndipo Farao anatembenuka, nalowa m’nyumba yake, osasamalira ichi chomwe mumtima mwake.

24 Koma Aejipito onse anakumba m’mphepete mwa mtsinje kufuna madzi akumwa; pakuti sanakhoze kumwa madzi a m’mtsinjemo.

25 Ndipo anafikira masiku asanu ndi awiri atapanda mtsinje Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EXO/7-d567f6baf72b1042a279266f408e3476.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *