Categories
EKSODO

EKSODO 5

Kupempha kwa Mose ndi Aroni kuipsa mlandu wa Aisraele

1 Ndipo pambuyo pake Mose ndi Aroni analowa nanena ndiFarao, Atero Yehova, Mulungu wa Israele, Lola anthu anga apite, kundichitira madyerero m’chipululu.

2 Koma Farao anati, Yehova ndani, kuti ndimvere mau ake ndi kulola Israele apite? Sindimdziwa Yehova, ndiponso sindidzalola Israele apite.

3 Ndipo iwo anati, Mulungu wa Ahebri wakomana ndi ife; timuketu ulendo wa masiku atatu m’chipululu, kumphera nsembe Yehova Mulungu wathu; kuti angatikanthe ndi mliri, kapena ndi lupanga.

4 Ndipo mfumu ya Aejipito inanena nao, Inu, Mose ndi Aroni, chifukwa ninji mumasulira anthu ntchito zao? Mukani ku akatundu anu.

5 Farao anatinso, Taonani, anthu a m’dziko ndiwo ambiri tsopano; ndipo inu muwapumitsa ku akatundu ao.

6 Ndipo tsiku lomwelo Farao analamulira akufulumiza anthu, ndi akapitao ao, ndi kuti,

7 Musawapatsanso anthu udzu wakupanga nao njerwa monga kale; apite okha adzifunire udzu.

8 Ndipo muziwawerengera njerwa, monga momwe anapanga kale; musachepsapo, popeza achita ulesi; chifukwa chake alikufuula, ndi kuti, Timuke, timphere nsembe Mulungu wathu.

9 Ilimbike ntchito pa amunawo, kuti aigwiritsitse, asasamalire mau amabodza.

10 Ndipo akufulumiza anthu ndi akapitao ao anatuluka, nanena ndi anthu ndi kuti, Atero Farao, Kulibe kukupatsani udzu.

11 Mukani inu nokha, dzifunireni udzu komwe muupeza; pakuti palibe kanthu kadzachepa pa ntchito yanu.

12 Pamenepo anthuwo anabalalika m’dziko lonse la Ejipito kufuna chiputu ngati udzu.

13 Ndipo akufulumiza anawakakamiza, ndi kuti, Tsirizani ntchito zanu, ntchito ya tsiku pa tsiku lake, monga muja munali ndi udzu.

14 Ndipo anapanda akapitao a ana a Israele, amene ofulumiza a Farao adawaika, ndi kuti, Nanga dzulo ndi lero simunatsirize bwanji ntchito yanu yoneneka ya njerwa, monga kale?

15 Pamenepo akapitao a ana a Israele anafika nalirira Farao, nati, Mwatero bwanji ndi akapolo anu?

16 Udzu osawapatsa akapolo anu, ndipo amanena ndi ife, Umbani njerwa; ndipo, taonani, amapanda akapolo anu; koma kulakwa nkwa anthu anu.

17 Koma iye anati, Aulesi inu, aulesi: chifukwa chake mulikunena, Timuke, timphere nsembe Yehova.

18 Mukani tsopano, gwirani ntchito; pakuti sadzakupatsani udzu, koma muonetse chiwerengero chake cha njerwa.

19 Ndipo akapitao a ana a Israele anaona kuti kudawaipira, pamene ananena, Musamachepetsa njerwa zanu, ntchito ya tsiku pa tsiku lake.

20 Ndipo potuluka kwa Farao iwo anakomana ndi Mose ndi Aroni, alikuima popenyana nao;

21 ndipo ananena nao, Yehova akupenyeni, naweruze; pakuti mwatinyansitsa pamaso pa Farao, ndi pamaso pa anyamata ake, ndi kuwapatsa lupanga m’dzanja lao kutipha nalo.

Mulungu alonjeza kupulumutsa anthu ake

22 Pamenepo Mose anabwerera nanka kwa Yehova, nati, Ambuye, mwawachitiranji choipa anthuwa? Mwandituma bwanji?

23 Popeza kuyambira kuja ndinafika kwa Farao kulankhula m’dzina lanu, anawachitira choipa anthuwa; ndipo simunalanditse anthu anu konse.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EXO/5-5ac7b77ff7f2c8cb8ea7a6763c30da99.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *