Categories
EKSODO

EKSODO 40

Mose autsa chihemacho

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

2 Tsiku loyamba la mwezi woyamba ukautse Kachisi wachihema chokomanako.

3 Ndipo ukaikemo likasa la mboni, nutchinge likasalo ndi nsalu yotchingayo.

4 Ulongenso gomelo, nukonzerepo zokonzera zake; ulongenso choikaponyalicho, ndi kuyatsa nyali zake.

5 Ndipo ukaike guwa la nsembe lofukizapo lagolide chakuno cha likasa la mboni, numange pa chihema nsalu yotsekera pakhomo.

6 Ndipo ukaike guwa la nsembe yopsereza kunja kwa khomo la Kachisi wa chihema chokomanako.

7 Ukaikenso mkhate pakati pa chihema chokomanako, ndi guwa la nsembe, ndi kuthiramo madzi.

8 Ndipo ukamange mpandawo pozungulira, ndi kupachika nsalu yotsekera pa chipata cha pabwalo.

9 Pamenepo ukatenge mafuta odzoza, ndi kudzoza nao chihema, ndi zonse zili m’mwemo, ndi kumpatula, ndi zipangizo zake zonse; ndipo adzakhala wopatulika.

10 Ndipo udzoze guwa la nsembe yopsereza, ndi zipangizo zake zonse, ndi kulipatula guwalo; ndipo guwalo lidzakhala lopatulika kwambiri.

11 Udzozenso mkhate ndi tsinde lake, ndi kuupatula.

12 Ndipo ubwere nao Aroni ndi ana ake aamuna ku khomo la chihema chokomanako, ndi kuwasambitsa ndi madzi.

13 Nuveke Aroni chovala zopatulikazo; ndi kumdzoza, ndi kumpatula andichitire Ine ntchito ya nsembe.

14 Ndipo ubwere nao ana ake aamuna ndi kuwaveka malaya am’kati;

15 nuwadzoze, monga unadzoza atate wao, kuti andichitire ntchito ya nsembe; ndi kudzozedwa kwao kuwakhalire unsembe wosatha mwa mibadwo yao.

16 Anatero Mose; monga mwa zonse Yehova adamuuza, momwemo anachita.

17 Ndipo kunali, mwezi woyamba wa chaka chachiwiri, tsiku loyamba la mwezi, anautsa chihema,

18 ndipo Mose anautsa chihema, nakhazika makamwa ake, naimika matabwa ake, namangapo mitanda yake, nautsa mizati ndi nsanamira zake.

19 Ndipo anayalika hema pamwamba pa Kachisi, naika chophimba cha chihema pamwamba pake; monga Yehova adamuuza Mose.

20 Ndipo anatenga mboniyo, naiika m’likasa, napisa mphiko palikasa, naika chotetezerapo pamwamba pa likasa;

21 nalowa nalo likasa mu chihema, napachika nsalu yotchinga, natchinga likasa la mboni; monga Yehova adamuuza Mose.

22 Ndipo anaika gomelo m’chihema chokomanako, pa mbali ya kumpoto ya Kachisi, kunja kwa nsalu yotchinga.

23 Nakonzerapo mkate pamaso pa Yehova; monga Yehova adamuuza Mose.

24 Ndipo anaika choikaponyali m’chihema chokomanako, popenyana ndi gome, pa mbali ya kumwera ya Kachisi.

25 Nayatsa nyalizo pamaso pa Yehova; monga Yehova adamuuza Mose.

26 Ndipo anaika guwa la nsembe lagolide m’chihema chokomanako chakuno cha nsalu yotchinga;

27 nafukizapo chofukiza cha fungo lokoma; monga Yehova adamuuza Mose.

28 Ndipo anapachika pa chihema nsalu yotsekera pakhomo.

29 Ndipo anaika guwa la nsembe yopsereza pa khomo la Kachisi wa chihema chokomanako, natenthapo nsembe yopsereza, ndi nsembe yaufa; monga Yehova adamuuza Mose.

30 Ndipo anaika mkhate pakati pa chihema chokomanako, ndi guwa la nsembe; nathiramo madzi osamba.

31 Ndipo Mose ndi Aroni ndi ana ake aamuna anasamba manja ao ndi mapazi ao m’menemo;

32 pakulowa iwo m’chihema chokomanako, ndi pakuyandikiza guwa la nsembe anasamba; monga Yehova adamuuza Mose.

33 Ndipo anautsa mpanda pozungulira pa chihema ndi guwa la nsembe, napachika nsalu yotsekera pa chipata cha pabwalo. Momwemo Mose anatsiriza ntchitoyi.

34 Pamenepo mtambo unaphimba chihema chokomanako, ndi ulemerero wa Yehova unadzaza Kachisiyo.

35 Ndipo Mose sanathe kulowa m’chihema chokomanako, popeza mtambo unakhalabe pamenepo; ndi ulemerero wa Yehova unadzaza Kachisi.

36 Ndipo pakukwera mtambo kuchokera ku chihema, ana a Israele amayenda maulendo ao onse;

37 koma ukapanda kukwera mtambo, samayenda ulendo wao kufikira tsiku loti wakwera.

38 Pakuti mtambo wa Yehova unakhala pa chihema msana, ndi usiku munali moto m’menemo, pamaso pa mbumba yonse ya Israele, m’maulendo ao onse.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EXO/40-49c72d5f4d5f2bedf7af822b0d81e906.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *