Categories
EKSODO

EKSODO 36

1 Pamenepo anachita Bezalele ndi Oholiyabu, ndi anthu aluso, amene Yehova adaika luso ndi nzeru m’mtima mwao adziwe machitidwe ake a ntchito yonse ya utumiki wake wa malo opatulika, monga mwa zonse adauza Yehova.

Amisiri alandira zopereka za anthu

2 Ndipo Mose adaitana Bezalele ndi Oholiyabu, ndi anthu onse aluso, amene Yehova adaika luso m’mtima mwao, onse ofulumidwa mtima ayandikize kuntchito kuichita.

3 Ndipo analandira kwa Mose chopereka chonse, chimene ana a Israele adabwera nacho chikhale cha machitidwe a ntchito ya malo opatulika, aipange nacho. Koma anaonjeza kubwera nazo kwa iye zopereka zaufulu, m’mawa ndi m’mawa.

4 Ndipo aluso onse, akuchita ntchito yonse ya malo opatulika, anadza onse ndi kusiya ntchito yao analinkuchita;

5 nanena ndi Mose, ndi kuti, Anthu alinkubwera nazo zochuluka, zakuposera zoyenera ntchito imene Yehova analamula ichitike.

6 Ndipo Mose analamulira, ndipo anamveketsa mau mu chigono chonse, ndi kuti, Asaonjezere ntchito ya ku chopereka cha malo opatulika, ngakhale mwamuna ngakhale mkazi. Tero anawaletsa anthu asabwere nazo zina.

7 Popeza zipangizo zinakwanira ntchito yonse ichitike, zinatsalakonso.

Mapangidwe a chihemacho

8 Ndipo onse a mtima waluso mwa iwo akuchita ntchitoyi anapanga chihema ndi nsalu zophimba khumi; anaziomba ndi bafuta wa thonje losansitsa, ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndiakerubi, ntchito ya mmisiri.

9 Utali wake wa nsalu yophimba imodzi ndiwo mikono makumi awiri kudza isanu ndi itatu, ndi kupingasa kwake kwa nsalu imodzi mikono inai; nsalu zonse zinafanana muyeso wao.

10 Ndipo analumikiza nsalu zisanu ina ndi inzake; nalumikiza nsalu zisanu zina ina ndi inzake.

11 Ndipo anaika magango ansalu yamadzi m’mphepete mwake mwa nsalu imodzi ku mkawo wa chilumikizano; nachita momwemo m’mphepete mwake mwa nsalu ya kuthungo, ya chilumikizano chachiwiri.

12 Anaika magango makumi asanu pansalu imodzi, naikanso magango makumi asanu m’mphepete mwake mwa nsalu ya chilumikizano china; magango anakomanizana lina ndi linzake.

13 Ndipo anazipanga zokowera makumi asanu zagolide, namanga nsalu pamodzi ndi zokowerazo; ndipo chihema chinakhala chimodzi.

14 Ndipo anaomba nsalu zophimba za ubweya wa mbuzi zikhale chophimba pamwamba pa chihema; anaomba nsalu zophimba khumi ndi imodzi.

15 Utali wake wa nsalu imodzi ndiwo mikono makumi atatu, ndi kupingasa kwake kwa nsalu imodzi ndiko mikono inai; nsalu khumi ndi imodzi zinafanana muyeso wao.

16 Ndipo anamanga pamodzi nsalu zisanu pazokha, ndi nsalu zisanu ndi imodzi pazokha.

17 Ndipo anapanga magango makumi asanu m’mphepete mwa nsalu imodzi, ya kuthungo, ya chilumikizano, naika magango makumi asanu m’mphepete mwa nsalu ya kuthungo, ya chilumikizano china.

18 Ndipo anapanga zokowera makumi asanu zamkuwa kumanga pamodzi hemalo, kuti likhale limodzi.

19 Ndipo anasokera hemalo chophimba cha zikopa za nkhosa zamphongo zonyika zofiira, ndi chophimba cha zikopa za akatumbu pamwamba pake.

20 Ndipo anapanga matabwa a chihema, oimirika, a mtengo wakasiya.

21 Utali wake wa thabwa limodzi ndiwo mikono khumi, ndi kupingasa kwake kwa thabwa limodzi ndiko mkono ndi hafu.

22 Pa thabwa limodzi panakhala mitsukwa iwiri, yomangika pamodzi; anawapanga momwemo matabwa onse a chihema.

23 Ndipo anapanga matabwa a chihema; matabwa makumi awiri a ku mbali ya kumwera, kumwera;

24 napanga makamwa makumi anai asilivapansi pa matabwa makumi awiri; makamwa awiri pansi pa thabwa limodzi kwa mitsukwa yake iwiri, ndi makamwa awiri pansi pa thabwa lina kwa mitsukwa yake iwiri.

25 Ndi ku mbali ina ya chihema, mbali ya kumpoto, anapanga matabwa makumi awiri, ndi makamwa ao makumi anai asiliva;

26 makamwa awiri pansi pa thabwa limodzi, ndi makamwa awiri pansi pa thabwa lina.

27 Ndi ku mbali ya kumbuyo ya chihema kumadzulo anapanga matabwa asanu ndi limodzi.

28 Anapanganso matabwa awiri a kungodya za chihema, m’mbali zake ziwiri.

29 Ndipo anaphatikizika pamodzi patsinde, naphatikizika pamodzi pamutu pake ndi mphete imodzi; anatero nao onse awiri pangodya ziwiri.

30 Ndipo panali matabwa asanu ndi atatu. Ndi makamwa ao asiliva, makamwa khumi kudza asanu ndi limodzi; makamwa awiri pansi pa thabwa limodzi.

31 Ndipo anapanga mitanda ya mtengo wakasiya; isanu ya matabwa a pa mbali ina ya chihema,

32 ndi mitanda isanu ya matabwa a pa mbali inzake ya chihema, ndi mitanda isanu ya matabwa a chihema ali pa mbali ya kumadzulo.

33 Ndipo anapititsa mtanda wa pakatipo, pakati pa matabwa kufikira kuthungo.

34 Ndipo anakuta matabwa ndi golide, napanga mphete zao zagolide zikhale zopisamo mitandayo, nakuta mitandayo ndi golide.

35 Ndipo anaomba nsalu yotchinga ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa; anachiomba ndi akerubi ntchito ya mmisiri.

36 Ndipo anaipangira mizati inai ya kasiya, nazikuta ndi golide; zokowera zao zinali zagolide; ndipo anaziyengera makamwa anai asiliva.

37 Ndipo anaomba nsalu yotsekera pa khomo la chihemacho, ya lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ntchito ya wopikula;

38 ndi nsanamira zake zisanu ndi zokowera zao; nakuta mitu yao ndi mitanda yao ndi golide; ndi makamwa ao asanu anali amkuwa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EXO/36-4c189ebe90c4ff6fb9c2fc97ca738c37.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *