Categories
EKSODO

EKSODO 35

Zopereka zofunika za pa chihemacho

1 Ndipo Mose anasonkhanitsa khamu lonse la ana a Israele, nanena nao, Siwa mau amene Yehova analamula, kuti muwachite.

2 Masiku asanu ndi limodzi azigwira ntchito, koma tsiku lachisanu ndi chiwiri muliyese lopatulika,Sabatalakupuma la Yehova: aliyense agwira ntchito pamenepo, aphedwe.

3 Musamasonkha moto m’nyumba zanu zilizonse tsiku la Sabata.

4 Ndipo Mose ananena ndi khamu lonse la ana a Israele, ndi kuti, Ichi ndi chimene Yehova analamula ndi kuti,

5 Mumtengere Yehova chopereka cha mwa zanu; aliyense wa mtima womfunitsa mwini abwere nacho, ndicho chopereka cha Yehova; golide, ndisiliva, ndi mkuwa;

6 ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ndi ubweya wa mbuzi;

7 ndi zikopa za nkhosa zamphongo zonyika zofiira, ndi zikopa za akatumbu, ndi mtengo wakasiya;

8 ndi mafuta akuunikira, ndi zonunkhira za mafuta odzoza, ndi chofukiza cha fungo lokoma;

9 ndi miyala yasohamu, ndi miyala yoika yaefodi, ndi ya chapachifuwa.

Zipangizo za m’malo opatulika

10 Ndipo abwere yense wa mtima waluso mwa inu, napange zonse zimene Yehova analamula;

11 chihema, ndi chophimba chake, zokowera zake, ndi matabwa ake, mitanda yake, mizati, nsanamira, ndi nsichi zake, ndi makamwa ao;

12 likasa, ndi mphiko zake, chotetezerapo, ndi nsalu yotchinga yotseka;

13 gome, ndi mphiko zake, ndi zipangizo zake zonse, ndi mkate woonekera;

14 ndi choikaponyali cha kuunika, ndi zipangizo zake, ndi nyali zake, ndi mafuta a kuunika;

15 ndi guwa la nsembe lofukizapo, ndi mphiko zake, ndi mafuta odzoza, ndi chofukiza cha fungo lokoma, ndi nsalu yotsekera pakhomo, pa khomo la chihema;

16 guwa la nsembe yopsereza, ndi sefa wamkuwa, mphiko zake, ndi zipangizo zake zonse, mkhate ndi tsinde lake;

17 nsalu zotchingira za kubwalo, nsichi zake, ndi makamwa ake, ndi nsalu yotsekera ku chipata cha pabwalo;

18 zichiri za chihema, ndi zichiri za kubwalo, ndi zingwe zao;

19 zovala za kutumikira nazo m’malo opatulika, zovala zopatulika za Aroni wansembe, ndi zovala za ana ake, zakugwira nazo ntchito ya nsembe.

Anthu abwera ndi zopereka mwaufulu

20 Ndipo khamu lonse la ana a Israele linachoka pamaso pa Mose.

21 Ndipo anadza, aliyense wofulumidwa mtima, ndi yense mzimu wake wamfunitsa, nabwera nacho chopereka cha Yehova, cha ku ntchito yachihema chokomanako, ndi ku utumiki wake wonse, ndi ku zovala zopatulika.

22 Ndipo anadza amuna ndi akazi, onse akufuna mtima eni ake, nabwera nazo mphete za mphuno, mphete za m’makutu, ndi mphete zosindikizira, ndi zigwinjiri, zonsezi zokometsera za golide; inde yense wakupereka kwa Yehova chopereka chagolide.

23 Ndipo aliyense kwao kunapezeka lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ndi ubweya wa mbuzi, ndi zikopa za nkhosa zamphongo zonyika zofiira, ndi zikopa za akatumbu, anabwera nazo.

24 Yense wakupereka chopereka cha siliva ndi mkuwa, anabwera nacho chopereka cha Yehova; ndi yense amene kwao kunapezeka mtengo wakasiya wa ku machitidwe onse a ntchitoyi, anabwera nao.

25 Ndi akazi onse a mtima waluso anapota ndi manja ao, nabwera nalo thonje lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.

26 Ndi akazi onse ofulumidwa mtima ndi luso anapota ubweyawo wa mbuzi.

27 Ndi akulu anabwera nayo miyala yasohamu, ndi miyala yoti aiike kuefodi, ndi kuchapachifuwa;

28 ndi zonunkhira, ndi mafuta akuunikira, ndi mafuta odzoza, ndi chofukiza za fungo lokoma.

29 Amuna ndi akazi onse a ana a Israele amene mitima yao inawafunitsa eni kubwera nazo za ku ntchito yonse imene Yehova analamula ipangike ndi dzanja la Mose, anabwera nacho chopereka chaufulu, kuchipereka kwa Yehova.

Za amisiri opanga ntchitoyi

30 Ndipo Mose anati kwa ana a Israele, Taonani, Yehova anaitana, ndi kumtchula dzina lake, Bezalele, mwana wa Uri, mwana wa Huri, wa fuko la Yuda;

31 ndipo anamdzaza ndi mzimu wa Mulungu, ndi luso, ndi nzeru, ndi chidziwitso, za m’ntchito zilizonse;

32 kulingirira ntchito zaluso, kuchita ndi golide, ndi siliva, ndi mkuwa;

33 ndi kuzokota miyala yoikika, ndi kuzokota mitengo, kuchita m’ntchito zilizonse zaluso.

34 Ndipo anaika m’mtima mwake kuti alangize ena, iye ndi Oholiyabu mwana wa Ahisamaki, wa fuko la Dani.

35 Amenewo anawadzaza ndi luso lamtima, lakuchita ntchito zilizonse, ya kuzokota miyala, ndi ya mmisiri waluso, ndi ya wopikula ndi lamadzi ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ndi ya muomba, ya iwo akuchita ntchito iliyonse, ndi ya iwo olingirira ntchito yaluso.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EXO/35-3d8f746aa0121f7f9936cf9c6ca936fe.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *