Chihema ndi nsalu zophimba zake
1 Ndipo uzipanga chihema ndi nsalu zophimba khumi, za bafuta wa thonje losansitsa, ndi thonje lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira; uombemoakerubi, ntchito ya mmisiri.
2 Utali wake wa nsalu yophimba imodzi ndiwo mikono makumi awiri kudza isanu ndi itatu, ndi kupingasa kwa nsalu imodzi ndiko mikono inai; nsalu zonse zikhale za muyeso umodzi.
3 Nsalu zisanu zilumikizane ina ndi inzake; ndi nsalu zisanu zina zilumikizane ina ndi inzake.
4 Ndipo uziika magango a nsalu ya madzi m’mphepete mwake mwa nsalu imodzi, ku mkawo wa chilumikizano; nuchite momwemo m’mphepete mwake mwa nsalu ya kuthungo ya chilumikizano china.
5 Uziika magango makumi asanu pansalu yochingira imodzi, nuikenso magango makumi asanu m’mphepete mwake mwa nsalu ya chilumikizano china; ndipo magango akomanizane lina ndi linzake.
6 Uzipanganso zokowera makumi asanu zagolide, ndi kumanga nsaluzo pamodzi ndi zokowerazo; kuti chihema chikhale chimodzi.
7 Ndipo uziomba nsalu zophimba za ubweya wa mbuzi zikhale chophimba pamwamba pa chihema; uziomba nsalu khumi ndi imodzi.
8 Utali wake wa nsalu imodzi ndiwo mikono makumi atatu, ndi kupingasa kwake kwa nsalu imodzi ndiko mikono inai; nsalu khumi ndi imodzi zikhale za muyeso womwewo.
9 Nuzisoka pamodzi nsalu zisanu pazokha, ndi nsalu zisanu ndi imodzi pazokha, nupinde nsalu yachisanu ndi chimodziyo pa khomo la hema.
10 Ndipo uziika magango makumi asanu m’mphepete mwa nsalu imodzi, ya kuthungo ya chilumikizano, ndi magango makumi asanu m’mphepete mwa nsalu ya kuthungo ya chilumikizano china.
11 Ndipo uzipanga zokowera makumi asanu zamkuwa, ndi kukowetsa zokowerazo m’magangomo, ndi kumanga pamodzi hemalo likhale limodzi.
12 Ndipo chotsalacho pansalu yophimbayo, hafu yake ya nsalu yotsalirayo, itchinge pambuyo pake pa chihemacho.
13 Ndi mkono wa pa mbali ino, ndi mkono wa pa mbali inzake, wakutsalira mu utali wake wa nsalu zophimbazo, itchinge pambali zake za chihemacho, mbali ino ndi mbali ina, kumphimba.
14 Ndipo uzipangira hema chophimba cha zikopa za nkhosa zamphongo zonyika zofiira, ndi chophimba za zikopa za akatumbu pamwamba pake.
Za matabwa oimirika a chihema
15 Ndipo uzipangira chihema matabwa oimirika, a mtengo wakasiya.
16 Utali wake wa thabwa limodzi ndiwo mikono khumi, ndi kupingasa kwake kwa thabwali mkono ndi hafu.
17 Pa thabwa limodzi pakhale mitsukwa iwiri, yomangika pamodzi; uzitero pa matabwa onse a chihema.
18 Ndipo uzipanga matabwa a chihema, matabwa makumi awiri ku mbali ya kumwera, kumwera.
19 Nuzipanga makamwa makumi anai asilivapansi pa matabwa makumi awiri; makamwa awiri pansi pa thabwa limodzi kwa mitsukwa yake iwiri, ndi makamwa awiri pansi pa thabwa lina kwa mitsukwa yake iwiri;
20 ndi pa mbali yake ina ya chihema, mbali ya kumpoto, pakhale matabwa makumi awiri; ndi makamwa asiliva makumi anai;
21 makamwa awiri pansi pa thabwa limodzi, ndi makamwa awiri pansi pa thabwa lina.
22 Ndipo uzipanga matabwa asanu ndi limodzi kwa mbali ya chihema cha kumbuyo.
23 Nupange matabwa awiri angodya za chihema cha kumbuyo.
24 Ndipo akhale ophatikizika pamodzi patsinde, nakhalenso ophatikizika pamodzi kumutu kwake ndi mphete imodzi; azitero onse awiri; azikhala angodya ziwiri.
25 Ndipo pakhale matabwa asanu ndi atatu, ndi makamwa ao asiliva, ndiwo makamwa khumi mphambu asanu ndi limodzi; makamwa awiri pansi pa thabwa limodzi, ndi makamwa awiri pansi pa thabwa lina.
26 Ndipo uzipanga mitanda ya mtengo wakasiya; isanu ya matabwa a pa mbali ina ya chihema,
27 ndi mitanda isanu ya matabwa a pa mbali ina ya chihema, ndi mitanda isanu ya matabwa a pa mbali ya chihema cha kumbuyo kumadzulo.
28 Ndi mtanda wa pakati pa matabwa ufikire kuthungo.
29 Ndipo uzikuta matabwa ndi golide, ndi kupanga mphete zao zagolide zopisamo mitandayo; uzikutanso mitandayo ndi golide.
30 Ndipo uutse chihema monga mwa makhalidwe ake amene anakusonyeza m’phiri.
Za nsalu yosiyanitsa ya pakhomo
31 Ndipo uziomba nsalu yotchinga ya thonje lamadzi, ndi lofiirira ndi lofiira, ndi la bafuta wa thonje losansitsa, aiombe ndi akerubi ntchito ya mmisiri;
32 ndipo uitchinge pa mizati inai ya mitengo wakasiya, zokuta ndi golide; zokowera zao zikhale zagolide, ndi makamwa anai asiliva.
33 Ndipo uzitchinga nsalu yotchinga pa zokowerazo, nulowetse likasa la mboni kukati kwa nsalu yotchinga; ndipo nsalu yotchingayo idzakugawirani pakati pa malo opatulika ndi malo opatulika kwambiri.
34 Ndipo uziika chotetezerapo pa likasa la mboni, m’malo opatulika kwambiri.
35 Nuziika gomelo kunja kwa nsalu yotchinga, ndi choikaponyali pandunji pa gome, pa mbali ya kumwera ya chihema; koma uike gomelo pa mbali ya kumpoto.
36 Ndipo uziomba nsalu yotsekera pa khomo la hema, ya lakuda, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ntchito ya wopikula.
37 Ndipo uzipangira nsalu yotsekerayo nsanamira zisanu za mtengo wakasiya, ndi kuzikuta ndi golide; zokowera zao zikhale zagolide; nuziyengera makamwa asanu amkuwa.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EXO/26-8341ceb2770dc65361d78f2556c37352.mp3?version_id=1068—