Categories
EKSODO

EKSODO 24

Mose ndi akulu akwera m’phiri

1 Ndipo Iye ananena ndi Mose, Ukwere kudza kwa Yehova, iwe ndi Aroni, Nadabu ndi Abihu, ndi akulu a Israele makumi asanu ndi awiri; ndipo mugwadire pakudza kutali;

2 ndipo Mose yekha ayandikire kwa Yehova; koma asayandikire iwowa; ndi anthunso asakwere naye.

3 Ndipo Mose anadza nafotokozera anthu mau onse a Yehova, ndi maweruzo onse; ndipo anthu onse anavomera pamodzi, nati, Mau onse walankhula Yehova tidzachita.

4 Ndipo Mose analembera mau onse a Yehova, nalawira kuuka mamawa, namanga guwa la nsembe patsinde paphiri, ndi zoimiritsa khumi ndi ziwiri, kwa mafuko khumi ndi awiri a Israele.

5 Ndipo anatuma ana a Israele a misinkhu ya anyamata, ndiwo anapereka nsembe zopsereza, naphera Yehova nsembe zamtendere, za ng’ombe.

6 Ndipo Mose anagawa mwaziwo, nathira wina m’zotengera, nawaza wina paguwa la nsembe

7 Ndipo anatenga buku laChipangano, nawerenga m’makutu a anthu; ndipo iwo anati, Zonse zimene Yehova walankhula tidzachita, ndi kumvera.

8 Ndipo Mose anatenga mwaziwo, nawaza pa anthu, nati Taonani mwazi wa chipangano, chimene Yehova anachita nanu, kunena za mau awa onse.

9 Ndipo Mose ndi Aroni, Nadabu ndi Abihu, ndi akulu a Israele makumi asanu ndi awiri anakwerako;

10 ndipo anapenya Mulungu wa Israele; ndipo pansi pa mapazi ake panali ngati mayalidwe oyera a miyala yasafiro, ndi ngati thupi la thambo loti mbee.

11 Koma sanatulutse dzanja lake pa akulu a ena a Israele; ndipo anapenya Mulungu, nadya, namwa.

12 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ukwere kudza kwa Ine m’phiri muno, nukhale pompano; ndipo ndidzakupatsa magome amiyala, ndi chilamulo ndi malamulo ndawalembera kuti uwalangize.

13 Ndipo anauka Mose, ndi Yoswa mtumiki wake; ndipo Mose anakwera m’phiri la Mulungu.

14 Ndipo anati kwa akulu, Tilindeni kuno kufikira tidzabwera kwa inu; ndipo taonani, Aroni ndi Huri ali nanu; munthu akakhala ndi mlandu abwere kwa iwowa.

15 Ndipo Mose anakwera m’phirimo, ndi mtambo unaphimba phirilo.

16 Ndipo ulemerero wa Yehova unakhalabe paphiri la Sinai, ndi mtambo unaliphimba masiku asanu ndi limodzi; ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri Iye ali m’kati mwa mtambo anaitana Mose.

17 Ndipo maonekedwe a ulemerero wa Yehova anali ngati moto wonyeketsa pamwamba paphiri, pamaso pa ana a Israele.

18 Ndipo Mose analowa m’kati mwa mtambo, nakwera m’phirimo; ndipo Mose anakhala m’phiri masiku makumi anai usana ndi usiku.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EXO/24-ce154869f3341483f43b4722f4931bf9.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *