Za mabodza ndi zonyenga
1 Usatola mbiri yopanda pake; usathandizana naye woipa ndi kukhala mboni yochititsa chiwawa.
2 Usatsata unyinji wa anthu kuchita choipa; kapena usachita umboni kumlandu, ndi kupatukira kutsata unyinji ndi kukhotetsa mlandu;
3 kapena usakometsera munthu wosauka pa mlandu wake.
4 Ukakomana ndi ng’ombe kapena bulu wa mdani wako zilinkusokera, uzimbwezera izo ndithu.
5 Ukaona bulu wa munthu wakudana nawe alikugona pansi ndi katundu wake, ndipo ukadaleka kuthandiza, koma uzimthandiza ndithu.
6 Usakhotetsa mlandu wa mnzako waumphawi.
7 Uzikhala kutali ndi mlandu wonama; ndipo usapha munthu wosachimwa ndi wolungama; pakuti sindidzayesa wolungama munthu woipa.
8 Usalandira chokometsera mlandu; pakuti chokometsera mlandu chidetsa maso a openya, ndipo chisanduliza mlandu wa olungama.
9 Usampsinja mlendo; pakuti mudziwa mtima wa mlendo popeza munali alendo m’dziko la Ejipito.
Za nthawi zopumula
10 Ndipo uzibzala m’munda mwako zaka zisanu ndi chimodzi, ndi kututa zipatso zako;
11 koma chaka chachisanu ndi chiwiri uuleke, ugone; kuti aumphawi a anthu a mtundu wako adyemo, ndipo zotsalira nyama zakuthengo zizidye; momwemo uzichita ndi munda wako wampesa, ndi munda wako waazitona.
12 Uzichita ntchito yako masiku asanu ndi limodzi, koma tsiku lachisanu ndi chiwiri uzipumula; kuti ng’ombe yako ndi bulu wako zipumule, ndi kuti mwana wa mdzakazi wako ndi mlendo atsitsimuke.
13 Ndipo samalirani zonse ndanena ndi inu; nimusatchule dzina la milungu ina; lisamveke pakamwa pako.
Za madyerero atatu m’chaka
14 Muzindichitira Ine madyerero katatu m’chaka.
15 Uzisungachikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa; masiku asanu ndi awiri uzidya mkate wopanda chotupitsa, monga ndinakuuza, nyengo yoikika, mwezi wa Abibu, pakuti m’menemo unatuluka mu Ejipito; koma asaoneke munthu pamaso panga opanda kanthu;
16 ndichikondwerero cha Masika, zipatso zoyamba za ntchito zako, zimene udazibzala m’munda; ndi chikondwerero cha Kututa, pakutha chaka, pamene ututa ntchito zako za m’munda.
17 Katatu m’chaka amuna onse azioneka pamaso pa Ambuye Yehova.
18 Usapereka mwazi wa nsembe yanga pamodzi ndi mkate wa chotupitsa; ndi mafuta a madyerero anga asagonamo kufikira m’mawa.
19 Uzibwera nazo zoyambayamba za m’munda mwako kunyumba ya Yehova Mulungu wako. Usaphike mwanawambuzi mu mkaka wa make.
Mulungu alonjezana nao za Kanani
20 Taona, ndituma mthenga akutsogolere, kukusunga panjira, ndi kukufikitsa pamaso pomwe ndakonzeratu.
21 Musamalire iye, ndi kumvera mau ake; musamuwawitsa mtima, pakuti sadzakhululukira zolakwa zanu; popeza dzina langa lili m’mtima mwake.
22 Pakuti ukamveratu mau ake, ndi kuchita zonse ndizilankhula, ndidzakhala mdani wa adani ako, ndipo ndidzasautsa akusautsa iwe.
23 Pakuti mthenga wanga adzakutsogolera, nadzakufikitsa kwa Aamori, ndi Ahiti, ndi Aperizi, ndi Akanani, Ahivi, ndi Ayebusi; ndipo ndidzawaononga.
24 Usagwadira milungu yao, kapena kuwatumikira, kapena kuchita monga mwa ntchito zao; koma uwapasule konse, ndi kugamulatu zoimiritsa zao.
25 Ndipo muzitumikira Yehova Mulungu wanu, potero adzadalitsa chakudya chako, ndi madzi ako; ndipo ndidzachotsa nthenda pakati pa iwe.
26 M’dziko mwanu simudzakhala wakutaya mwana, kapena wosabala; ndidzakwaniritsa kuwerenga kwa masiku ako.
27 Ndidzatumiza kuopsa kwanga kukutsogolere, ndipo ndidzapirikitsa anthu onse amene udzafika kwao, ndipo ndidzachita kuti adani ako onse adzakuonetsa m’mbuyo mwao.
28 Ndipo ndidzatumiza mavu akutsogolere amene adzaingitsa Ahivi, Akanani, ndi Ahiti, pamaso pako.
29 Sindidzawaingitsa pamaso pako chaka chimodzi; kuti dziko lingakhale bwinja, ndi zilombo zakuthengo zingakuchulukire.
30 Ndidzawaingitsa pang’onopang’ono pamaso pako, kufikira utachuluka, ndi kulandira dziko cholowa chako.
31 Ndipo ndidzalemba malire ako kuyambira ku Nyanja Yofiira, kufikira ku nyanja ya Afilisti, ndi kuyambira kuchipululu kufikira ku Nyanja; popeza ndidzapereka okhala m’dzikolo m’dzanja lako, ndipo uziwaingitsa pamaso pako.
32 Usapangana nao, kapena ndi milungu yao.
33 Asakhale m’dziko lako iwowa, kuti angakulakwitse pa Ine; pakuti ukatumikira milungu yao, kudzakukhalira msampha ndithu.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EXO/23-9a4a96869e9ec6834a0af6278544f917.mp3?version_id=1068—