Yetero azonda Mose nampangira
1 Ndipo Yetero, wansembe wa Midiyani, mpongozi wa Mose, anamva zonse zimene Mulungu adachitira Mose ndi Israele anthu ake, kuti Yehova adatulutsa Israele mu Ejipito.
2 Ndipo Yetero, mpongozi wa Mose, anabwera naye Zipora mkazi wa Mose (atamtuma kwao), ndi ana ake awiri;
3 dzina la winayo ndiye Geresomo, pakuti anati, Ndakhala mlendo m’dziko lachilendo;
4 ndi dzina la mnzake ndiye Eliyezere; pakuti anati, Mulungu wa kholo langa anakhala thandizo langa nandilanditsa ku lupanga laFarao.
5 Ndipo Yetero, mpongozi wa Mose, anadza ndi ana ake aamuna ndi mkazi wake kwa Mose kuchipululu kumene adamangako, paphiri la Mulungu;
6 nati kwa Mose, Ine mpongozi wako Yetero ndadza kwa iwe, ndi mkazi wako, ndi ana ake omwe awiri.
7 Ndipo Mose anatuluka kukakomana ndi mpongozi wake, nawerama, nampsompsona; nafunsana ali bwanji, nalowa m’hema.
8 Ndipo Mose anafotokozera mpongozi wake zonse Yehova adazichitira Farao ndi Aejipito chifukwa cha Israele; ndi mavuto onse anakomana nao panjira, ndi kuti Yehova adawalanditsa.
9 Ndipo Yetero anakondwera chifukwa cha zabwino zonse Yehova adazichitira Israele, ndi kuwalanditsa m’dzanja la Aejipito.
10 Nati Yetero, Woyamikika Yehova, amene anakulanditsani m’dzanja la Aejipito, ndi m’dzanja la Farao; amene analanditsa anthu awa pansi padzanja la Aejipito.
11 Tsopano ndidziwa kuti Yehova ali wamkulu ndi milungu yonse, pakuti momwe anadzikuza okha momwemo anawaposa.
12 Ndipo Yetero, mpongozi wa Mose, anamtengera Mulungu nsembe yopsereza, ndi nsembe zophera; ndipo Aroni ndi akulu onse a Israele anadza kudzadya mkate ndi mpongozi wa Mose pamaso pa Mulungu.
13 Ndipo kunatero kuti m’mawa mwake Mose anakhala pansi kuweruzira anthu milandu yao; ndipo anthu anakhala chilili pamaso pa Mose kuyambira m’mawa kufikira madzulo.
14 Ndipo pamene mpongozi wake wa Mose anaona zonsezi iye anawachitira anthu, anati, Chinthu ichi nchiyani uwachitira anthuchi? Umakhala pa wekha bwanji, ndi anthu onse amakhala chilili pamaso pako kuyambira m’mawa kufikira madzulo?
15 Ndipo Mose anati kwa mpongozi wake, Chifukwa anthu amadza kwa ine kudzafunsira Mulungu;
16 akakhala nao mlandu adza kwa ine, kuti ndiweruze pakati pa munthu ndi mnansi wake, ndi kuti ndiwadziwitse malemba a Mulungu, ndi malamulo ake.
17 Koma mpongozi wa Mose ananena naye, Chinthu uchitachi sichili chabwino ai.
18 Udzalema konse, iwe ndi anthu amene uli nao; pakuti chikukanika chinthu ichi; sungathe kuchichita pa wekha.
19 Tamvera mau anga tsopano, ndikupangire nzeru, ndi Mulungu akhale nawe; ukhale m’malo mwa anthu kwa Mulungu, nupite nayo milandu kwa Mulungu;
20 nuwamasulire malemba, ndi malamulo, ndi kuwadziwitsa njira imene ayenera kuyendamo, ndi ntchito imene ayenera kuchita.
21 Koma iwe, dzisankhire mwa anthu ako onse, amuna anzeru, akuopa Mulungu, amuna oona, akudana nalo phindu la chinyengo; nuwaikire iwo oterewa, akulu a pa zikwi, akulu a pa mazana, akulu a pa makumi asanu, akulu a pa makumi;
22 ndipo iwo aweruze milandu ya anthu nthawi zonse; ndipo kudzakhala kuti milandu yaikulu yonse abwere nayo kwa iwe; koma milandu yaing’ono yonse aweruze okha; potero idzakuchepera ntchito, ndi iwo adzasenza nawe.
23 Ukachite chinthuchi, ndi Mulungu akakuuza chotero, udzakhoza kupirira, ndi anthu awa onse adzapita kwao mumtendere.
24 Ndipo Mose anamvera mau a mpongozi wake, nachita zonse adazinena.
25 Ndipo Mose anasankha amuna anzeru mwa Aisraele onse, nawaika akulu a pa anthu, akulu a pa zikwi, akulu a pa mazana, akulu a pa makumi asanu, ndi akulu a pa makumi.
26 Ndipo anaweruza anthu nthawi zonse; mlandu wakuwakanika amabwera nao kwa Mose, ndi milandu yaing’ono yonse amaweruza okha.
27 Ndipo Mose analola mpongozi wake amuke; ndipo anachoka kunka ku dziko lake.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EXO/18-a21f16efc489b3414e3c459b26a51257.mp3?version_id=1068—