Zinziri ndi mana
1 Ndipo anachoka ku Elimu, ndi khamu lonse la ana a Israele linalowa m’chipululu cha Sini, ndicho pakati pa Elimu ndi Sinai, tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi wachiwiri atatuluka m’dziko la Ejipito.
2 Ndipo khamu lonse la ana a Israele linadandaulira Mose ndi Aroni m’chipululu;
3 nanena nao ana a Israele, Ha? Mwenzi titafa ndi dzanja la Yehova m’dziko la Ejipito, pokhala ife pa miphika ya nyama, pakudya mkate ife chokhuta; pakuti mwatitulutsa kudza nafe m’chipululu muno kudzapha msonkhano uwu wonse ndi njala.
4 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, ndidzavumbitsira inu mkate wodzera kumwamba; ndipo anthu azituluka ndi kuola muyeso wa tsiku pa tsiku lake, kuti ndiwayese, ngati ayenda m’chilamulo changa kapena iai.
5 Ndipo kudzakhala tsiku lachisanu ndi chimodzi, kuti azikonza umene adabwera nao, ataonjezapo muyeso unzake wa pa tsiku limodzi.
6 Ndipo Mose ndi Aroni ananena ndi ana onse a Israele, Madzulo mudzadziwa kuti Yehova anakutulutsani m’dziko la Ejipito;
7 ndi m’mawa mwake mudzaona ulemerero wa Yehova, popeza alinkumva mulikudandaulira Yehova; pakuti ife ndife chiyani, kuti mutidandaulira ife?
8 Nanenanso Mose, Pakukupatsani Yehova nyama ya kudya madzulo, ndi mkate wokhuta m’mawa, atero popeza Yehova adamva madandaulo anu amene mumdandaulira nao. Koma ife ndife chiyani? Simulikudandaulira ife koma Yehova.
9 Ndipo Mose anati kwa Aroni, Nena ndi khamu lonse la ana a Israele, Yandikizani pamaso pa Yehova, pakuti anamva madandaulo anu.
10 Ndipo kunakhala, pakunena Aroni ndi khamu lonse la ana a Israele kuti iwo anatembenukira kuchipululu, ndipo, taonani, ulemerero wa Yehova unaoneka mumtambo.
11 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,
12 Ndamva madandaulo a ana a Israele; lankhula nao ndi kuti, Madzulo mudzadya nyama, ndi m’mawa mudzakhuta mkate; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
13 Ndipo kunali madzulo zinakwera zinziri, ndipo zinakuta tsasa, ndi m’mawa padagwa mame pozungulira tsasa.
14 Ndipo atakamuka mame adagwawo, taonani, pankhope pa chipululu pali kanthu kakang’ono kamphumphu, kakang’ono ngati chipale panthaka.
15 Ndipo pamene ana a Israele anakaona, anati wina ndi mnzake, Nchiyani ichi? Pakuti sanadziwe ngati nchiyani. Ndipo Mose ananena nao, Ndiwo mkatewo Yehova wakupatsani ukhale chakudya chanu.
16 Amenewo ndiwo mau walamulira Yehova, Aoleko yense monga mwa njala yake; munthu mmodzi omeri limodzi, monga momwe muli, yense atengere iwo m’hema mwake.
17 Ndipo ana a Israele anatero, naola wina wambiri, wina pang’ono.
18 Ndipo pamene anayesa ndi omeri, iye amene adaola wambiri sunamtsalire, ndi iye amene adaola pang’ono sunamsowe; yense anaola monga mwa njala yake.
19 Ndipo Mose ananena nao, Palibe munthu asiyeko kufikira m’mawa.
20 Koma sanammvere Mose; ndipo ena anasiyako kufikira m’mawa; koma unagwa mphutsi, nununkha. Ndipo Mose anakwiya nao.
21 Ndipo anauola m’mawa ndi m’mawa, yense monga mwa njala yake; popeza likatentha dzuwa umasungunuka.
22 Ndipo kunali tsiku lachisanu ndi chimodzi, anaola mkate, naonjezapo linzake, maomeri awiri pa munthu mmodzi; ndipo akazembe a khamulo anadza nauza Mose.
23 Ndipo ananena nao, Ichi ndi chomwe Yehova analankhula, Mawa ndiko kupuma,Sabatalopatulika la Yehova; chimene muziotcha, otchani, ndi chimene muziphika phikani; ndi chotsala chikukhalireni chosungika kufikira m’mawa.
24 Ndipo anausunga kufikira m’mawa, monga adalamulira Mose; koma sunanunkhe, ndipo sunagwe mphutsi.
25 Ndipo Mose anati, Muudye lero; pakuti lero ndilo Sabata la Yehova; simuupeza lero pabwalo.
26 Muziola uwu masiku asanu ndi limodzi; koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndilo la Sabata, pamenepo padzakhala palibe.
27 Ndipo kunali tsiku la Sabata, kuti anthu ena anatuluka kukaola, koma sanaupeze.
28 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Mukana kusunga zouza zanga ndi malamulo anga kufikira liti?
29 Taonani, popeza Yehova anakupatsani Sabata, chifukwa chake tsiku lachisanu ndi chimodzi alikupatsa inu mkate wofikira masiku awiri; khalani yense m’malo mwake munthu asatuluke m’malo mwake tsiku lachisanu ndi chiwiri.
30 Ndipo anthu anapumula tsiku lachisanu ndi chiwiri.
31 Ndipo mbumba ya Israele inautcha dzina lakeMana; ndiwo ngati zipatso zampasa, oyera; powalawa akunga timitanda tosakaniza ndi uchi.
32 Ndipo Mose anati, Awa ndi mau anauza Yehova, Dzazani omeri nao, asungikire mibadwo yanu; kuti aone mkatewo ndinakudyetsani nao m’chipululu, muja ndinakutulutsani m’dziko la Ejipito.
33 Ndipo Mose anati kwa Aroni, Tenga mphika, nuthiremo mana odzala omeri, nuuike pamaso pa Yehova, usungikire mibadwo yanu.
34 Monga Yehova analamula Mose, momwemo Aroni anauika patsogolo pa Mboni, usungikeko.
35 Ndipo ana a Israele anadya mana zaka makumi anai, kufikira atalowa dziko la midzi; anadya mana kufikira analowa malire a dziko la Kanani.
36 Koma omeri ndilo limodzi la magawo khumi la efa.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EXO/16-0743f611e7db315835126056b1733a3a.mp3?version_id=1068—