Categories
EKSODO

EKSODO 14

Farao alondola Aisraele

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi kuti,

2 Lankhula ndi anthu a Israele, kuti abwerere m’mbuyo nagone patsogolo pa Pihahiroti, pakati pa Migidoli ndi nyanja, patsogolo pa Baala-Zefoni; pandunji pake mugone panyanja.

3 NdipoFaraoadzanena za ana a Israele, Azimidwa dziko, chipululu chawatsekera.

4 Ndipo ndidzalimbitsa mtima wake wa Farao kuti awalondole; ndipo ndidzalemekezedwa pa Farao ndi pa nkhondo yake yonse; pamenepo Aejipito adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndipo anachita chomwecho.

5 Ndipo anauza mfumu ya Aejipito kuti anthu adathawa; ndi mtima wa Farao ndi wa anyamata ake inasandulikira anthuwo, ndipo anati, Ichi nchiyani tachita, kuti talola Israele amuke osatigwiriranso ntchito?

6 Ndipo anamanga galeta lake, napita nao anthu ake;

7 napita nao magaleta osankhika mazana asanu ndi limodzi, ndi magaleta onse a mu Ejipito, ndi akapitao ao onse.

8 Ndipo Yehova analimbitsa mtima wa Farao, mfumu ya Aejipito, ndipo iye analondola ana a Israele; koma ana a Israele adatuluka ndi dzanja lokwezeka.

9 Ndipo Aejipito anawalondola, ndiwo akavalo ndi magaleta onse a Farao, ndi apakavalo ake, ndi nkhondo yake, nawapeza ali kuchigono kunyanja, pa Pihahiroti, patsogolo pa Baala-Zefoni.

10 Ndipo pamene Farao anayandikira ana a Israele anatukula maso ao, taonani, Aejipito alinkutsata pambuyo pao; ndipo anaopa kwambiri; ndi ana a Israele anafuulira kwa Yehova.

11 Ndipo anati kwa Mose, Kodi mwatichotsera kuti tikafe m’chipululu chifukwa panalibe manda mu Ejipito? Nchiyani ichi mwatichitira kuti mwatitulutsa mu Ejipito?

12 Si awa mauwo tinalankhula nanu mu Ejipito ndi kuti, Tilekeni, kuti tigwirire ntchito Aejipito? Pakuti kutumikira Aejipito kutikomera si kufa m’chipululu ai.

13 Ndipo Mose ananena ndi anthu, Musaope, chilimikani, ndipo penyani chipulumutso cha Yehova, chimene adzakuchitirani lero; pakuti Aejipito mwawaona lerowa, simudzawaonanso konse.

14 Yehova adzakugwirirani nkhondo, ndipo inu mudzakhala chete.

Aisraele aoloka pouma

15 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ufuuliranji kwa Ine? Lankhula ndi ana a Israele kuti aziyenda.

16 Ndipo iwe nyamula ndodo yako, nutambasulire dzanja lako kunyanja, nuigawe, kuti ana a Israele alowe pakati pa nyanja pouma.

17 Ndipo Ine, taonani, ndidzalimbitsa mitima ya Aejipito, kuti alowemo powatsata; ndipo ndidzalemekezedwa pa Farao, ndi pa nkhondo yake yonse, pa magaleta ake, ndi pa okwera pa akavalo ake.

18 Ndipo Aejipito adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, polemekezedwa Ine pa Farao, pa magaleta ake, ndi pa okwera pa akavalo ake.

19 Ndipo mthenga wa Mulungu, wakutsogolera ulendo wa Israele, unachokako, nutsata pambuyo pao; ndipo mtambo njo uja unachoka patsogolo pao, nuima pambuyo pao;

20 nulowa pakati pa ulendo wa Aejipito ndi ulendo wa Aisraele; ndipo mtambo unachita mdima, komanso unaunikira usiku; ndipo ulendo wina sunayandikizane ndi unzake usiku wonse.

21 Ndipo Mose anatambasulira dzanja lake kunyanja; ndipo Yehova anabweza nyanja ndi mphepo yolimba ya kum’mawa usiku wonse, naumitsa nyanja; ndipo madziwo anagawikana.

22 Ndipo ana a Israele analowa pakati pa nyanja pouma; ndi madziwo anakhala kwa iwo ngati khoma palamanja, ndi palamanzere.

23 Ndipo Aejipito anawalondola, nalowa pakati pa nyanja powatsata, ndiwo akavalo onse a Farao, magaleta ake, ndi apakavalo ake.

24 Ndipo kunali, ulonda wa mamawa, Yehova ali m’moto ndi m’mtambo njo anapenyera pa ulendo wa Aejipito, nauvuta ulendo wa Aejipito.

25 Ndipo anagulula njinga za magaleta ao, nawayendetsa molemetsa; pamenepo Aejipito anati, Tithawe pamaso pa Israele; pakuti Yehova alikuwagwirira nkhondo pa Aejipito.

Aejipito amizidwa m’nyanja

26 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Tambasulira dzanja lako kunyanja, kuti madziwo abwerere kudzamiza Aejipito, magaleta ao, ndi apakavalo ao.

27 Ndipo Mose anatambasulira dzanja lake kunyanja, ndi nyanja inabwerera m’mayendedwe ake mbandakucha; ndipo Aejipito pothawa anakomana nayo; ndipo Yehova anakutumula Aejipito m’kati mwa nyanja.

28 Popeza madziwo anabwerera, namiza magaleta ndi apakavalo, ndiwo nkhondo yonse ya Farao imene idalowa pambuyo pao m’nyanja; sanatsale wa iwowa ndi mmodzi yense.

29 Koma ana a Israele anayenda pouma pakati pa nyanja; ndi madziwo anakhala ngati khoma kwa iwo, palamanja ndi lamanzere.

30 Chomwecho Yehova anapulumutsa Israele tsiku lomwelo m’manja a Aejipito; ndipo Israele anaona Aejipito akufa m’mphepete mwa nyanja.

31 Ndipo Israele anaiona ntchito yaikulu imene Yehova anachitira Aejipito, ndipo anthuwo anaopa Yehova; nakhulupirira Yehova ndi mtumiki wake Mose.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EXO/14-b37eeef7335ffce47cc6c0b169cd0ccb.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *