Categories
EKSODO

EKSODO 12

Kuikidwa kwa Paska

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni m’dziko la Ejipito, ndi kuti,

2 Mwezi uno uzikhala kwa inu woyamba wa miyezi; muziuyesa mwezi woyamba wa chaka.

3 Mulankhule ndi gulu lonse la Israele ndi kuti, Tsiku lakhumi la mwezi uno adzitengere munthu yensemwanawankhosa, monga mwa mabanja a atate ao, mwanawankhosa pabanja.

4 Banja likaperewera mwanawankhosa, munthu ndi mnzake ali pafupi pa nyumba yake atenge monga mwa kufikira kwa anthu ao; muziwerengera mwanawankhosa monga mwa kudya kwao.

5 Mwanawankhosa wanu azikhala wangwiro, wamwamuna, wa chaka chimodzi; muzimtenga ku nkhosa kapena ku mbuzi.

6 Ndipo mukhale naye chisungire kufikira tsiku lakhumi ndi chinai la mwezi womwe; ndipo gulu lonse la Israele lizamuphe madzulo.

7 Ndipo azitengako mwazi, naupake pa mphuthu za mbali ndi ya pamwamba m’nyumba zimene adyeramo.

8 Ndipo azidya nyamayo usiku womwewo, yoocha pamoto, ndi mkate wopanda chotupitsa; aidye ndi ndiwo zowawa.

9 Musaidya yaiwisi, kapena yophika ndi madzi konse ai, koma yoocha pamoto; mutu wake ndi miyendo yake ndi matumbo ake.

10 Ndipo musasiyako kufikira m’mawa; koma yotsalira kufikira m’mamawayo muipsereze ndi moto.

11 Ndipo muziidya chotero: okwinda m’chuuno, nsapato zanu pa mapazi anu ndodo yanu m’dzanja lanu, ndipo muziidya msanga; ndiyePaskawa Yehova.

12 Pakuti ndidzapita pakati padziko la Ejipito usiku womwewo, ndi kukantha ana oyamba onse m’dziko la Ejipito, anthu ndi zoweta; ndipo ndidzachita maweruzo pa milungu yonse ya Aejipito; Ine ndine Yehova.

13 Ndipo mwaziwo udzakhala chizindikiro kwa inu pa nyumba zimene mukhalamo; pamene ndiona mwaziwo ndidzapitirira inu, ndipo sipadzakhala mliri wakukuonongani, pakukantha Ine dziko la Ejipito.

14 Ndipo tsiku lino lidzakhala kwa inu chikumbutso, muzilisunga la chikondwerero cha Yehova; ku mibadwo yanu muzilisunga la chikondwerero, likhale lemba losatha.

15 Masiku asanu ndi awiri muzidya mkate wopanda chotupitsa; lingakhale tsiku loyamba muzichotsa chotupitsa m’nyumba zanu; pakuti aliyense wakudya mkate wa chotupitsa kuyambira tsiku loyamba kufikira tsiku lachisanu ndi chiwiri, munthu ameneyo adzachotsedwa kwa Israele.

16 Ndipo tsiku loyamba kukhale kusonkhana kopatulika, ndi tsiku lachisanu ndi chiwiri kukhalenso kusonkhana kopatulika; pasachitike ntchito masikuwo, zokhazi zakudya anthu onse ndizo muzichita.

17 Ndipo muzisungachikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa; pakuti tsiku lomwe lino ndinatulutsa makamu anu m’dziko la Ejipito; chifukwa chake muzisunga tsiku lino m’mibadwo yanu, lemba losatha.

18 Mwezi woyamba, tsiku lake lakhumi ndi chinai madzulo ake, muzidya mkate wopanda chotupitsa, kufikira tsiku la makumi awiri mphambu limodzi la mwezi, madzulo ake.

19 Chisapezeke chotupitsa m’nyumba zanu masiku asanu ndi awiri; pakuti aliyense wakudya kanthu ka chotupitsa, munthuyo adzachotsedwa ku gulu la Israele, angakhale ndiye mlendo kapena wobadwa m’dziko.

20 Musadye kanthu ka chotupitsa; mokhala inu monse muzidya mkate wopanda chotupitsa.

21 Pamenepo Mose anaitana akulu onse a Israele, nanena nao, Pitani, dzitengereni anaankhosa monga mwa mabanja anu, nimuphere Paska.

22 Ndipo muzitenga mpukutu wahisope, ndi kuuviika m’mwazi uli m’mbale, ndi kupaka mwazi uli m’mbalemo pa mphuthu ya pamwamba ndi pambali; koma inu, asatuluke munthu pakhomo pa nyumba yake kufikira m’mawa.

23 Pakuti Yehova adzapita pakatipo kukantha Aejipito; koma pamene adzaona mwaziwo pa mphuthu pamwamba ndi za pambali, Yehova adzapitirira pakhomopo, osalola woononga alowe m’nyumba zanu kukukanthani.

24 Ndipo muzisunga chinthu ichi chikhale lemba la kwa inu, ndi kwa ana anu ku nthawi zonse.

25 Ndipo kudzakhala, pamene mulowa m’dziko limene Yehova adzakupatsani, monga analankhula, muzisunga kutumikira kumeneku.

26 Ndipo kudzakhala, pamene ana anu adzanena ndi inu, Kutumikiraku muli nako nkutani?

27 Mudzati, Ndiko nsembe ya Paska wa Yehova, amene anapitirira nyumba za ana a Israele mu Ejipito, pamene anakantha Aejipito, napulumutsa nyumba zathu.

28 Ndipo anthu anawerama, nalambira. Ndipo ana a Israele anamuka nachita monga Yehova adalamulira Mose ndi Aroni; anachita momwemo.

Ana oyamba kubadwa aphedwa

29 Ndipo panakhala pakati pa usiku, Yehova anakantha ana oyamba onse a m’dziko la Ejipito, kuyambira mwana woyamba waFaraowakukhala pa mpando wachifumu wake kufikira mwana woyamba wa wam’nsinga ali m’kaidi; ndi ana oyamba onse a zoweta.

30 Ndipo Farao anauka usiku, iye ndi anyamata ake onse ndi Aejipito onse; ndipo kunali kulira kwakukulu mu Ejipito; pakuti panalibe nyumba yopanda wakufa m’mwemo.

31 Ndipo anaitana Mose ndi Aroni usiku, nati, Ukani, tulukani pakati pa anthu anga, inu ndi ana a Israele; ndipo mukani katumikireni Yehova, monga mwanena.

32 Muka nazoni zoweta zanu zazing’ono ndi zazikulu, monga mwanena; chokani, ndi kundidalitsa inenso.

33 Ndipo Aejipito anaumiriza anthuwo, nafulumira kuwatulutsa m’dziko; pakuti anati, Tili akufa tonse.

34 Ndipo anthu anatenga mtanda wao usanatupe, ndi zoumbiramo zao zomangidwa m’zovala zao pa mapewa ao.

35 Ndipo ana a Israele anachita monga mwa mau a Mose; napempha Aejipito zokometsera zasiliva, ndi zagolide, ndi zovala.

36 Ndipo Yehova anapatsa anthu chisomo pamaso pa Aejipito, ndipo sanawakanize. Ndipo anawafunkhira Aejipito.

Ana a Israele atuluka mu Ejipito

37 Ndipo ana a Israele anayenda ulendo wakuchokera ku Ramsesi kufikira ku Sukoti, zikwi mazana asanu ndi limodzi oyenda okha, ndiwo amuna, osawerenga ana.

38 Ndipo anthu ambiri osokonezeka anakwera nao; ndi nkhosa ndi ng’ombe, zoweta zambirimbiri.

39 Ndipo anaotcha timitanda topanda chotupitsa ta mtanda umene anabwera nao ku Ejipito, popeza sadaikamo chotupitsa; pakuti adawapirikitsa ku Ejipito, ndipo sanathe kuchedwa, kapena kudzikonzeratu kamba.

40 Ndipo kukhala kwa ana a Israele anakhala mu Ejipito ndiko zaka mazana anai kudza makumi atatu.

41 Ndipo kunakhala pakutha zaka mazana anai kudza makumi atatu, inde panakhala tsiku lomwelo, makamu onse a Yehova anatuluka m’dziko la Ejipito.

42 Ndiwo usiku wosungira Yehova ndithu, chifukwa cha kuwatulutsa m’dziko la Ejipito; usiku womwe uno ukhale wosungira Yehova ana onse a Israele ku mibadwo yao.

Lamulo la Paska

43 Ndipo Yehova anati kwa Mose ndi Aroni, Lemba la Paska ndi ili: mwana wa mlendo aliyense asadyeko;

44 koma kapolo wa mwini aliyense, wogula ndi ndalama, utamdula, ndipo adyeko.

45 Mlendo kapena wolembedwa ntchito asadyeko.

46 Audye m’nyumba imodzi; usatulukira nayo kubwalo nyama ina; ndipo musathyole fupa lake.

47 Gulu lonse la Israele lizichita ichi.

48 Koma akakhala nanu mlendo, nakonzera Yehova Paska, adulidwe amuna ake onse, ndipo pamenepo asendere kuuchita; nakhale ngati wobadwa m’dziko; koma wosadulidwa aliyense asadyeko.

49 Pakhale lamulo lomweli pa wobadwa m’dziko, ndi pa mlendo wakukhala pakati pa inu.

50 Ndipo ana onse a Israele anachita monga Yehova adawalamulira Mose ndi Aroni, momwemo anachita.

51 Ndipo kunakhala tsiku lomwelo, kuti Yehova anatulutsa ana a Israele m’dziko la Ejipito, monga mwa makamu ao.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EXO/12-90a3e3ea3dfeac75a69656724a3a3d4e.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *