Chozizwitsa chakhumi: Imfa ya ana oyamba kubadwa
1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Watsala mliri umodzi ndidzamtengeraFarao, ndi Ejipito; pambuyo pake adzakulolani muchoke kuno; pamene akulolani kupita, zoonadi adzakuingitsani kuno konse.
2 Lankhula tsopano m’makutu a anthu, kuti mwamuna yense apemphe kwa mnzake, ndi mkazi yense kwa mnzake, zokometsera zasilivandi zagolide.
3 Ndipo Yehova anawapatsa anthu chisomo pamaso pa Aejipito. Munthuyo Mose ndiyenso wamkulu ndithu m’dziko la Ejipito, pamaso pa anyamata a Farao, ndi pamaso pa anthu.
4 Ndipo Mose anati, Atero Yehova, Monga pakati pa usiku ndidzatuluka Ine kunka pakati pa Aejipito;
5 ndipo ana oyamba a m’dziko la Ejipito adzafa, kuyambira mwana woyamba wa Farao wokhala pa mpando wachifumu wake, kufikira mwana woyamba wa mdzakazi wokhala pa miyala yopera; ndi ana onse oyamba a zoweta.
6 Ndipo kudzakhala kulira kwakukulu m’dziko lonse la Ejipito, kunalibe kunzake kotere, sikudzakhalanso kunzake kotere.
7 Koma palibe galu adzafunyitsira lilime lake ana onse a Israele ngakhale anthu kapena zoweta; kuti mudziwe kuti Yehova asiyanitsa pakati pa Aejipito ndi Aisraele.
8 Ndipo anyamata ako onse awa adzanditsikira, nadzandigwadira, ndi kuti, Tulukani inu, ndi anthu onse akukutsatani; ndipo pambuyo pake ndidzatuluka. Ndipo anatuluka kwa Farao wakupsa mtima.
9 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Farao sadzamvera inu; kuti zozizwa zanga zichuluke m’dziko la Ejipito.
10 Ndipo Mose ndi Aroni anachita zozizwa izi zonse pamaso pa Farao; koma Yehova analimbitsa mtima wake wa Farao, ndipo sanalole ana a Israele atuluke m’dziko lake.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EXO/11-7657d8605d4477b167ba808b09b09743.mp3?version_id=1068—